Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Silika—“Nsalu Yapamwamba Kwambiri”

Silika—“Nsalu Yapamwamba Kwambiri”

Silika—“Nsalu Yapamwamba Kwambiri”

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU JAPAN

ZINA mwa zovala zokongola kwambiri padziko lonse, kuphatikizapo za ku Japan zotchedwa kimono, za ku India zotchedwa sari, ndi za ku Korea zotchedwa hanbok, n’zofanana m’njira imodzi. Nthawi zambiri zimakhala za silika, yomwe ndi nsalu yowala ndi yokongola imene anthu ena aitchapo nsalu yapamwamba kwambiri. Anthu padziko lonse lapansi, kuyambira mafumu akale mpaka anthu wamba amasiku ano, akopeka ndi kukongola kwa silika. Koma kale silika sankapezeka paliponse ngati masiku ano.

Kale, ku China kokha n’komwe ankapanga silika. Palibe munthu wina aliyense kunja kwa China amene ankadziwa kapangidwe kake, ndipo aliyense wa ku China woulula chinsinsi cha momwe ankapangira silika ankatha kuphedwa monga woukira boma. Choncho n’zosadabwitsa kuti silika anali wokwera mtengo kwambiri chifukwa cha zimenezi. Mwachitsanzo, mu Ufumu wonse waukulu wa Roma, silika anali wokwera mtengo koopsa.

Patapita nthawi, dziko la Persia linayamba kuyendetsa malonda a silika yense wochokera ku China. Koma mtengo wake unali wokwerabe, ndipo ngakhale kuti anthu anayesayesa kuti azigula silika mwachindunji osadzera mwa amalonda a ku Persia, sanaphule kanthu. Kenako, Mfumu yaikulu ya ku Byzantium dzina lake Justinian inatulukira nzeru inayake. Cha m’ma 550 C.E, inatumiza amonke awiri ku China mwachinsinsi. Patatha zaka ziwiri anabwerako. M’kati mwa ndodo zawo zansungwi anabisamo chuma cha mtengo wapatali kwambiri chomwe mfumuyi inakhala ikudikirira. Munali mazira a mbozi zopanga silika. Chinsinsi chija chinaululika tsopano. Zopanga silika ku China kokha zinathera pomwepo.

Mmene Silika Amapangidwira

Silika amapangidwa ndi mbozi zopanga silika, zochokera ku gulugufe winawake. Pali mitundu yambirimbiri ya mbozi zopanga silika, koma dzina lasayansi la mbozi zimene zimapanga silika wabwino kwambiri ndi Bombyx mori. Pamafunika mbozi zambiri kuti apange nsalu za silika, ndipo zimenezi zachititsa kuti anthu ayambe kuweta mbozi zopanga silika. Banja la a Shoichi Kawaharada, omwe amakhala ku Gumma Prefecture, ku Japan, ndi limodzi mwa mabanja pafupifupi 2,000 a m’dzikoli amene akugwirabe ntchito yofuna zambiri yoweta mbozi zimenezi. Nyumba yawo ya nsanjika ziwiri, yomwe ndi yoyenererana kwambiri ndi kuweta mbozi zopanga silika, ili pakaphiri pafupi ndi munda wa mabulosi (1).

Gulugufe wamkazi amaikira mazira amene amatha kukwana 500, ndipo dzira lililonse limakhala laling’ono ngati kanjere ka mpiru (2). Pakatha masiku mwina 20, mazirawo amaswa n’kutulutsa timbozi. Timbozi ting’onoting’onoto timadya koopsa. Usana ndi usiku timakhala tikudya masamba a mabulosi, ndipo timadya masamba a mabulosi okha basi (3, 4). Pomatha masiku 18, mbozizo zimakhala zitakula kuwirikiza ka 70 kuposa momwe zinalili pobadwa ndipo zimakhala zitafundula khungu lawo kanayi.

Pa famu ya a Kawaharada amawetapo mbozi za silika pafupifupi 120,000. Zikamadya, zimachita phokoso lomwe limamveka ngati momwe imamvekera mvula yambiri ikamagwera pamasamba. Mbozi yopanga silika ikafika pokhwima, kulemera kwake kumakhala kutawirikiza nthawi 10,000 kuposa momwe inkalemerera pobadwa. Ikafika pamenepa ndiye kuti yakonzeka kuyamba kuluka chikwa.

Zimapanga Silika Mwakachetechete

Mbozi yopanga silika ikamalizika kukula, thupi lake limasintha mtundu n’kuyamba kumaonetsa m’kati, zomwe zimasonyeza kuti ikufuna kuyamba kuluka chikwa. Mbozizo zikayamba kulowera uku ndi uku kufunafuna malo oti zipachikepo zikwa zawo, ndiye kuti zafika poti aziike m’bokosi lomwe limakhala ndi zipinda zambirimbiri za makona anayi. Akaziika mmenemo, zimayamba kutulutsa ulusi wosalala woyera wa silika (5), womwe zimalukira zikwa. Izo zimakhala m’kati mwa zikwazo.

Imeneyi ndi nthawi imene a Kawaharada amakhala otanganidwa kwambiri, chifukwa mbozi zonse 120,000 zimayamba kuluka zikwa chapanthawi imodzimodziyo. A Kawaharada amaika mabokosi ambirimbiri m’chipinda chozizira bwino cha pansanjika yachiwiri ya nyumbayo (6).

Panthawi imeneyi, m’kati mwa mbozi ija mumakhala mukuchitika zinthu zodabwitsa kwambiri. Masamba a mabulosi omwe inadya aja akagayika amasintha n’kusanduka zinthu zinazake zamadzimadzi zomwe zimasungidwa m’tiziwalo tiwiri ta m’mimba mwa mboziyo tokhala ngati matumba tomwe timakhala tatitali kuyambira kumutu mpaka kum’chira kwa mboziyo. Zinthu zamadzimadzi zija zikamayenda m’tiziwalo timeneti, zimamatidwa ndi zinthu zinazake zangati utomoni. Ulusi uwiri wopangidwa ndi zinthu zamadzimadzi zija umatuluka kukamwa kwa mboziyo, koma usanatuluke umamatiriridwa pamodzi ndi zinthu zangati utomoni zija. Zikakhudzana ndi mpweya, zinthu zamadzimadzi zija zimauma n’kupanga ulusi umodzi wa silika.

Mboziyo ikayamba kupanga silika, simungathe kuisiyitsa. Imaluka ulusi wotalika masentimita 30 mpaka 40 mphindi iliyonse, ndipo nthawi yonseyo imakhala ikugwedeza mutu wake. Nkhani inayake inati chikwa chikamatha kupangidwa, mboziyo imakhala itagwedeza mutu wake nthawi zokwana 150,000. Italuka kwa mausana ndi mausiku awiri, mboziyo imapanga ulusi umodzi wa silika wotalika mamita 1,500. Kumeneku n’kutalika kowirikiza kanayi kutalika kwa nyumba yansanjika yaitali kwambiri.

Pomatha mlungu umodzi wokha, a Kawaharada adzakhala atatolera zikwa 120,000 zomwe zidzatumizidwe ku fakitale yopanga nsalu za silika. Pamafunika zikwa pafupifupi 9,000 kuti apange chovala cha mtundu wa kimono chimodzi ndi zikwa pafupifupi 140 kuti apange taye imodzi. Mpango umodzi wa silika umafunika zikwa zoposa 100 kuti aupange.

Mmene Amapangira Nsalu ya Silika

Zikwa zija zikafika ku fakitale, amayamba kuchotsa ulusi wa silika ku zikwazo n’kuukulungiza pa chinthu china. Kodi kuchotsa ulusi ku zikwa kunayamba bwanji? Pali nthano zambiri zofotokoza momwe kunayambira. Nthano ina imati, Mfumukazi ya ku China dzina lake Hsi Ling-Shi inaona kuti chikwa chagwera m’kapu yake ya tiyi kuchokera mumtengo wa mabulosi. Pofuna kuchichotsa, inaona kuti chinkatuluka limodzi ndi ulusi wokongola wa silika. Zimenezi zinayambitsa kuchotsa ulusi wa silika ku zikwa, ntchito yomwe masiku ano amachita ndi makina.

Kuti anthu athe kugula zikwazo, mbozi zomwe zili m’kati mwake ziyenera kuphedwa zisanasanduke agulugufe. Kuti achite zimenezi, amagwiritsira ntchito madzi otentha kapena nthunzi yake. Zikwa zowonongeka amazichotsa, ndipo zotsalazo amayamba kuzikonza. Choyamba, amaika zikwa m’madzi kapena nthunzi yotentha kuti afewetse ulusi wake. Kenaka pomwe ulusiwo unayambira amapakola ndi masache amene amayenda mozungulira (7). Malinga ndi kukhuthala kwa ulusi womwe akufuna, ulusi wochokera ku zikwa ziwiri kapena kuposa, amatha kuuphatikiza n’kupanga ulusi umodzi woneneperapo. Ulusiwo umauma ukamakulungizika pa chinthu chozungulira chabowo pakati. Silikayo amamukulungizanso kachiwiri pa chinthu chokulungizira chokulirapo, ndipo akatero amapanga mpukutu wa silika wotalika ndi kulemera momwe akufunira (8, 9).

Mwina munasisitapo nsalu ya silika yosalala ndi yofewa kwambiri moti mpaka munkafuna kusisita nayo masaya anu. Kodi n’chiyani chimachititsa silika kukhala wosalala? Chinthu chimodzi chimene chimachititsa ndicho kumuchotsa zinthu zomata zija, zomwe zimamatirira zinthu zamadzimadzi zija. Silika amene sanamuchotse zomata amakhala wokhakhala ndipo amavuta kumupaka utoto. Nsalu ya mtundu wa shifoni imakhala yokhakhala, chifukwa choti saichotsa zinthu zonse zomata zija.

Chinthu chachiwiri chomwe chimachititsa ndi momwe ulusiwo aupotera. Nsalu ya ku Japan yotchedwa habutai imakhala yosalala ndi yofewa. Ulusi wake umakhala wongopota pang’ono kapena wosapota n’komwe. Mosiyana ndi zimenezi, nsalu ina yotchedwa crepe imakhala yokhakhala ndi yokanda. Ulusi wake umakhala wopota kwambiri.

Kupaka utoto ndi mbali inanso yofunika kwambiri. Nsalu ya silika siivuta kupaka utoto. Kapangidwe kake kamachititsa kuti utoto uzilowerera mosavuta, ndipo chifukwa cha zimenezi silika sasuluka wamba. Komanso, mosiyana ndi nsalu zochita kupanga ku fakitale, silika ali ndi zinthu zinazake m’kati mwake zomwe zimachititsa kuti utoto uliwonse uzitha kulowerera bwino. Silika amatha kupakidwa utoto akadali ulusi asanawombedwe pa chinthu chowombera nsalu (10) kapena amamupaka utoto ali kale nsalu yowombawomba. Pogwiritsa ntchito njira inayake yofala yopakira utoto pa zovala za mtundu wa kimono, amatha kupanga nsalu zokongola zomwe amazipaka utoto pamanja akatha kuwomba silikayo.

Ngakhale kuti ku China ndi ku India n’kumene amapanga silika wambiri masiku ano, anthu oyambitsa mafashoni a ku France ndi ku Italy ndi amene akutsogolabe pa ntchito yokonza masitayilo a zovala za silika. Komabe, masiku ano kuli nsalu zochita kupanga ku fakitale monga nayiloni ndi zina zotero, zomwe anthu amatha kupangira zovala zambiri zotsika mtengo. Koma silika akadali nsalu yapamwamba kwambiri kuposa zina zonse. Mkulu wa nyumba yosunga zinthu zakale ndi zochititsa chidwi zokhudzana ndi silika ku Yokohama, m’dziko la Japan anati: “Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri, sitingathebe kupanga silika ku fakitale. Tikudziwa zonse zokhudza momwe amapangidwira ndi mmene alili m’kati mwake. Koma sitingathe kumukopera. Chimenecho ndiye chinsinsi cha silika.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

MMENE Silika ALILI

Wolimba: Ulusi wa silika umakhala wolimba ngati ulusi wa chitsulo wofanana nawo saizi.

Wowala: Silika amawala bwino ngati mikanda yoyera. Amatero chifukwa choti m’kati mwake muli zinthu zimene zimanyezimira zikakhudzana ndi kuwala.

Sakhakhala pakhungu: Zinthu zimene zimapanga silika sizikanda khungu. Silika akuti amateteza khungu ku matenda osiyanasiyana. Zodzoladzola zina n’zopangidwa ndi ufa wa silika.

Amayamwa madzi: Zinthu zimene zimapezeka mu silika zili ndi timabowo ndipo zimayamwa thukuta, zimene zimachititsa kuti munthu asanyowe ndi thukuta ndiponso azipitidwa mphepo kunja kukamatentha.

Sapsa msanga: Silika sapsa msanga ndipo satulutsa mpweya wapoizoni akapsa.

Amateteza khungu: Silika amayamwa mphamvu zoipa za dzuwa choncho amateteza khungu.

Samata: Popeza silika ali ndi zinthu zimene zimamuchititsa kuti asamamate ndipo amayamwa madzi, samatirira thupi ngati momwe nsalu zina zimachitira.

KUSAMALIRA Silika

Kuchapa: Ndi bwino kuchapitsa zovala za silika. Ngati mukuchapa kunyumba, gwiritsani ntchito sopo wochapira wamphamvu zachikatikati m’madzi ofunda (ofunda mwina madigiri seshasi 30). Musatikite kwambiri ndipo musafinye chovalacho. Musachiumitse m’makina.

Kusita: Ikani nsalu ina pamwamba pa chovala cha silikacho posita. Yesetsani kusita motsatira ulusi wa chovalacho ndipo ayironi yake ikhale yotentha pafupifupi madigiri seshasi 130. Gwiritsani ntchito nthunzi yochepa kwambiri, kapena musaigwiritse ntchito n’komwe.

Kuchotsa mothimbirira: Ngati mukufunika kuchotsa mwachangu pothimbirira, ikani chovala cha silikacho pa nsalu youma ndipo m’kati mwa chovalacho muyang’ane pansi. Sunsani ndi nsalu yonyowa pamalo pothimbirirapo, osati kutikitapo, ndipo sunsani kuchokera kumbuyo. Kenako kachapitseni chovalacho.

Kusunga: Pewani kuika zovala za silika pamalo a chinyontho, ndipo muziziteteza ku njenjete, ndiponso musamaziike pamalo powala kwambiri. Gwiritsani ntchito zokolekera zovala zokutidwa ndi masiponji, kapena zisungeni pamalo afulati ndipo musazipinde kwambiri.

[Chithunzi patsamba 25]

Zikwa za silika

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Photos 7-9: Matsuida Machi, Annaka City, Gunma Prefecture, Japan; 10 and close-up pattern: Kiryu City, Gunma Prefecture, Japan