Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tchimo Loyambirira Linali Chiyani?

Kodi Tchimo Loyambirira Linali Chiyani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Tchimo Loyambirira Linali Chiyani?

YANKHO la funso limeneli n’lofunika kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti kusamvera Mulungu kwa Adamu ndi Hava kunakhudza mibadwo yonse ya anthu, mpaka kufika nthawi yathu ino. Baibulo limati: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Koma kodi kungothyola chipatso mumtengo n’kuchidya kunabweretsa motani mavuto aakulu ngati amenewo?

Mulungu atalenga Adamu ndi Hava, anawaika m’munda wokongola mmene munali zomera zimene akanatha kudya ndi mitengo yambirimbiri yobereka zipatso. Mtengo umodzi wokha ndi umene anawauza kuti zipatso zake asamadye. Mtengo wake unali “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.” Popeza Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wosankha zomwe akufuna kuchita, akanatha kusankha kumvera Mulungu kapena kusamumvera. Koma Adamu anachenjezedwa kuti “tsiku lomwe udzadya [za mumtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa] udzafa ndithu.”—Genesis 1:29; 2:17.

Lamulo Loyenerera

Lamulo limodzi lokhali silinachititse Adamu ndi Hava kuvutika, chifukwa akanatha kudya zipatso za m’mitengo ina yonse ya m’mundamo. (Genesis 2:16) Ndiponso, lamulolo silinasonyeze kuti Adamu ndi Hava anali ndi malingaliro enaake oipa, komanso silinawachotsere ulemu wawo. Mulungu akanakhala kuti anawaletsa kuchita zinthu zonyansa ngati kugonana ndi zinyama kapena kupha, ena akanatha kunena kuti anthu angwiro anali ndi malingaliro enaake onyansa amene anafunika kuwatsekereza. Koma kudya kunali kwachibadwa ndiponso koyenera.

Kodi chipatso choletsedwacho chinaimira kugonana, monga momwe anthu ena amanenera? Malemba sapereka maziko alionse oganizira choncho. Choyamba, pamene Mulungu ankapereka lamulo limenelo, Adamu anali yekha ndipo zikuoneka kuti anakhala choncho kwa kanthawi ndithu. (Genesis 2:23) Chachiwiri, Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti ‘abalane, achuluke, adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Iye sakanawalamulira kuti aphwanye lamulo lake kenaka n’kuwauza kuti afa chifukwa chochita zimenezo. (1 Yohane 4:8) Chachitatu, Hava anadya chipatsocho Adamu asanadye, kenaka anamupatsako mwamuna wakeyo. (Genesis 3:6) N’zachionekere kuti chipatsocho sichinaimire kugonana.

Anafuna Kukhala Odziimira Paokha

Mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa unali mtengo weniweni. Komabe, unkaimira ufulu wa Mulungu wouza anthu ake kuti zinthu izi n’zabwino koma izi n’zoipa, monga Wolamulira wawo. Choncho kudya za mumtengowo sikunali kuba kokha, kutenga zinthu zomwe mwiniwake anali Mulungu, komanso kunali kuyesera modzitukumula kukhala odziimira paokha, kapena odzilamulira okha. Kumbukirani kuti Satana atanamiza Hava kuti iye ndi mwamuna wake akadya chipatsocho ‘sadzafai,’ Satana anawonjezera kuti: “Chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 3:4, 5.

Koma Adamu ndi Hava atadya chipatsocho, sanatseguke m’maso mofanana ndi Mulungu n’kudziwa zabwino ndi zoipa. M’malo mwake, Hava anauza Mulungu kuti: ‘Njoka inandinyenga ine.’ (Genesis 3:13) Komabe, iye ankadziwa lamulo la Mulungu, ndipo mpaka analibwereza kwa njokayo, yomwe inkalankhulira Satana. (Chivumbulutso 12:9) Choncho zomwe anachitazo anazichita dala chifukwa chosamvera. (Genesis 3:1-3) Koma Adamu sananyengedwe. (1 Timoteo 2:14) M’malo momvera Mlengi wake mokhulupirika, iye anamvera mkazi wake n’kutsatira njira yake yodziimira payekha.—Genesis 3:6, 17.

Chifukwa chofuna kukhala odziimira paokha, Adamu ndi Hava anawonongeratu ubwenzi wawo ndi Yehova ndipo anaika uchimo m’thupi mwawo mpaka unasintha kapangidwe kawo kenikeni. N’zoona kuti anakhala ndi moyo zaka mahandiredi angapo, koma anayamba kufa “m’tsiku” limene anachimwa, monga momwe nthambi yomwe yathyoledwa pamtengo imachitira. (Genesis 5:5) Ndiponso, kwa nthawi yoyamba anayamba kusowa mtendere mumtima mwawo. Anamva kuti anali amaliseche ndipo anayesera kumubisalira Mulungu. (Genesis 3:7, 8) Anadziimbanso mlandu, anamva kuti anali osatetezeka, ndiponso anachita manyazi. Uchimo wawowo unawasokonezera zinthu koopsa, ndipo chikumbumtima chawo chinayamba kuwaimba mlandu kuti achita zinthu zolakwa.

Kuti achite zinthu mogwirizana ndi mawu ake ndi mfundo zake zoyera, Mulungu molungama anauza Adamu ndi Hava kuti adzafa ndipo anawathamangitsa m’munda wa Edene. (Genesis 3:19, 23, 24) Choncho, Paradaiso, chimwemwe, ndi moyo wosatha zinatayika, ndipo m’malo mwake kunabwera uchimo, kuvutika, ndi imfa. Zinalidi zinthu zomvetsa chisoni kwa mtundu wa anthu! Komabe, atangouza Adamu ndi Hava kuti adzafa, Mulungu analonjeza kuti adzathetsa zoipa zonse zomwe zidzabwere chifukwa cha uchimo wawowo, popanda kuphwanya mfundo zake zolungama.

Yehova anakonza zoti adzathandize ana a Adamu ndi Hava kumasuka ku uchimo ndi imfa. Iye anakwanitsa kuchita zimenezi kudzera mwa Yesu Kristu. (Genesis 3:15; Mateyu 20:28; Agalatiya 3:16) Kudzera mwa iye, Mulungu adzachotsa uchimo ndi zotsatirapo zake zonse ndipo adzachititsa dziko lonse lapansi kukhala paradaiso, monga momwe anafunira pachiyambi.—Luka 23:43; Yohane 3:16.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

Kodi tikudziwa bwanji kuti chipatso choletsedwacho sichinaimire kugonana?—Genesis 1:28.

Kodi kudya chipatsocho kunatanthauza chiyani?—Genesis 3:4, 5.

Kodi Mulungu wakonza zotani kuti adzachotse zotsatirapo za uchimo?—Mateyu 20:28.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Chipatso choletsedwacho sichinaimire kugonana

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Hava anafuna kukhala ngati Mulungu kuti azidziwa payekha zabwino ndi zoipa