Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukufunitsitsa Kukhala Wolemera Mwauzimu?

Kodi Mukufunitsitsa Kukhala Wolemera Mwauzimu?

Kodi Mukufunitsitsa Kukhala Wolemera Mwauzimu?

KUTI munthu akhale wolemera pamafunika khama ndi kudzimana. N’chimodzimodzinso ndi kulemera mwauzimu. Yesu anasonyeza zimenezi pamene anati: “Kundikani chuma chanu kumwamba.” (Mateyo 6:20) Chuma chauzimu sichimangobwera chokha. Monga mmene munthu sangakhalire ndi chuma chambiri chifukwa chongokhala ndi akaunti kubanki, munthu sangalemere mwauzimu chifukwa chongokhala ndi chipembedzo. Kuti munthu akhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu, akonde zinthu zauzimu, ndiponso akhale ndi makhalidwe abwino, pamafunika nthawi, khama, kudzimana ndi kuikirapo mtima.—Miyambo 2:1-6.

Kodi Mungakhale ndi Zonse Ziwiri?

Kodi munthu angathe kukhala wolemera mwauzimu komanso n’kukhala ndi chuma chambiri? Mwina zingatheke, koma sangathe kufunafuna zinthu zonse ziwiri nthawi imodzi. Yesu anati: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mateyo 6:24b) N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti zinthu ziwirizi zimasokonezana. Choncho, asanauze ophunzira ake kuti akundike chuma chauzimu, Yesu anati: “Lekani kudzikundikira chuma padziko lapansi.”—Mateyo 6:19.

Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu anganyalanyaze malangizo a Yesu n’kuyamba kufunafuna chuma chambiri komanso kukhala wolemera mwauzimu? Yesu anati: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri; pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo.” (Mateyo 6:24a) Munthu akamafunafuna zonse ziwiri, angayambe kuona kuti zinthu zauzimu, zomwe amangozichita kuti athane nazo, zikumutayitsa nthawi. M’malo modalira Mulungu, munthu angayambe kudalira chuma kuti n’chimene chingamuthandize pa mavuto ake. Izitu n’zimene Yesu ananena kuti: “Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.”—Mateyo 6:21.

Mkhristu aliyense angachite bwino kuganizira kwambiri malangizo a m’Baibulo amenewa asanasankhe zinthu zimene akufuna kuti azitherapo nthawi yake, ndiponso kuikapo maganizo ndi mtima wake. Mulungu sanaike malire a chuma chimene Mkhristu angakhale nacho, koma zimenezi sizisonyeza kuti palibe vuto ngati munthu samvera chenjezo lake loti tisakhale adyera. (1 Akorinto 6:9, 10) Taona kale kuti anthu amene samvera malangizo a m’Baibulo ndi kuyamba kufunitsitsa kulemera, amavutika mwauzimu ndi m’maganizo. (Agalatiya 6:7) Mosiyana ndi zimenezi, Yesu ananena kuti anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu amakhala osangalala. (Mateyo 5:3) Ndithudi, Mlengi wathu pamodzi ndi Mwana wake amadziwa bwino zimene zingatithandize kuti tikhale osangalala—Yesaya 48:17, 18.

Simudzakhumudwa ndi Zimene Mwasankha

Kodi mudzasankha kutumikira Mulungu kapena kufunafuna chuma? N’zoona kuti tiyenera kupeza zinthu zofunika pamoyo. M’kalata yake yoyamba yopita kwa Timoteyo, mtumwi Paulo anati: “Ndithudi, ngati munthu sasamalira ake a iye mwini, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.” Paulo analimbikitsanso Akhristu kuti asadalire chuma koma adalire Mulungu ndiponso kuti “akhale olemera pa ntchito zabwino.” (1 Timoteyo 5:8; 6:17, 18) Kodi mudzafunafuna ndi kuika mtima wanu pazinthu zotani? Ntchito yaikulu mwa ntchito zabwino zimene Paulo anatchula ndi yolalikira ndi kupanga ophunzira, imene Yesu anauza ophunzira ake kuti azichita. (Mateyo 28:19, 20) Akhristu akasankha kukhala ndi moyo wosalira zambiri kuti achite nawo ntchito yofunikayi mokwanira, osati kuti angokhala ndi nthawi yopuma, ndiye kuti ‘akudzisungira okha maziko abwino a tsogolo lawo’ m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Ngakhale panopa amaona kuti chuma chauzimu chimaposa golidi.—1 Timoteyo 6:19; Miyambo 16:16; Afilipi 1:10.

Tiyeni tione chitsanzo cha Eddie. Makolo ake anakhala Mboni za Yehova iyeyo ali mwana. Nthawi ina, chuma chawo chonse chinawonongeka ndipo sanachitire mwina koma kusamuka basi. Eddie anati: “Nthawi zonse ndinkadera nkhawa kuti chidzachitike n’chiyani tikadzakhala opandiratu kanthu. Koma panthawi imeneyo, tinalibiretu chilichonse. Kodi zimene ndinkadera nkhawa zija zinachitika? Ayi ndithu. Tinkapezabe zakudya ndi zovala. Yehova ankatisamalira ndipo patapita nthawi, zinthu zinakhalanso bwino. Zimene tinakumana nazozi zinandiphunzitsa kukhulupirira kwambiri zimene Yesu analonjeza pa Mateyo 6:33. Iye anati tikamafuna Ufumu wa Mulungu choyamba, palibe chifukwa chodera nkhawa zoti tipeza bwanji zinthu zofunika pamoyo.” Tsopano Eddie limodzi ndi mkazi wake amachita utumiki woyendayenda nthawi zonse. Ali ndi zinthu zonse zofunika pamoyo wawo. Ndipo chofunika kwambiri, iwowa ndi olemera mwauzimu.

Phindu Losaneneka

Mosiyana ndi chuma cha padzikoli chimene mbala zingabe, chuma chauzimu n’chokhalitsa. (Miyambo 23:4, 5; Mateyo 6:20) Komabe, n’zovuta kunena kuti munthu wafika pati mwauzimu. Tingathe kudziwa kuchuluka kwa chuma chimene munthu ali nacho, koma n’zovuta kudziwa kuti munthu ali ndi chikondi, chisangalalo, kapena chikhulupiriro chotani. Koma phindu la chuma chauzimu ndi losaneneka. Ponena za ophunzira ake amene anasiya zinthu zowathandiza pamoyo monga nyumba ndi minda kuti achite zinthu zauzimu, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani amuna inu, Palibe amene anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino, amene tsopano lino sadzapeza zochuluka kuwirikiza nthawi 100 m’nthawi ino, nyumba ndi abale ndi alongo ndi amayi ndi ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo, ndipo m’dongosolo la zinthu limene likubweralo, moyo wosatha.”—Maliko 10:29, 30.

Pakati pa Mulungu ndi chuma, kodi n’chiyani chidzakhala patsogolo m’moyo wanu?

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Kodi mukufunafuna chuma . . .

. . . kapena kulemera mwauzimu?