Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

TCHULANI MILILI KHUMI

Lembani milili motsatira ndondomeko imene inachitikira, ndipo lembani mzera wolumikiza yankholo ndi chithunzi chake cholondola. (Dziwani kuti zithunzizi sizili m’ndondomeko yolondola.)

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. ․․․․․

5. ․․․․․

6. ․․․․․

7. ․․․․․

8. ․․․․․

9. ․․․․․

10. ․․․․․

NDINE NDANI?

11. Ndimadziona kuti ndine msungwana wakuda. Ndinafunsiridwapo ndi mfumu.

12. Paulo anadandaulira Suntuke ndi ineyo kuti tikhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani mavesi kapena vesi la m’Baibulo lomwe likusowapo.

Tsamba 3 Kodi n’chiyani chingakuchitikireni ngati mumakonda ndalama? (1 Timoteyo 6:․․․)

Tsamba 8 Kodi mtima wanu udzakhala kuti nthawi zonse? (Mateyo 6:․․․)

Tsamba 21 Kodi moyo wanu ukhale wotani? (Aheberi 13:․․․)

Tsamba 28 Kodi n’chiyani chomwe munthu yemwe akuchita chibwenzi mobisa ayenera kukumbukira? (Aheberi 4:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, longosolani zomwe zikuchitika pa chithunzi chilichonse?

(Mayankho ali pa tsamba 19)

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Mtsinje wa Nailo unasanduka magazi.—Eksodo 7:19-21.

2. Achule.—Eksodo 8:5-14.

3. Nsabwe.—Eksodo 8:16-19.

4. Mizaza.—Eksodo 8:21-24.

5. Mlili wopha ziweto.—Eksodo 9:1-6.

6. Zilonda.—Eksodo 9:8-11.

7. Mvula ya matalala.—Eksodo 9:22-26.

8. Dzombe.—Eksodo 10:12-15.

9. Mdima wandiweyani.—Eksodo 10:21-23.

10. Kuphedwa kwa ana oyamba kubadwa.—Eksodo 12:12, 29.

11. Msulami.—Nyimbo ya Solomo 1:1-6.

12. Euodiya.—Afilipi 4:2.