Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limanena za Chiyani?

Kodi Baibulo Limanena za Chiyani?

Kodi Baibulo Limanena za Chiyani?

ANTHU ena amaona kuti Baibulo ndi buku la mbiri yakale chifukwa limafotokoza zimene Mulungu wakhala akuchita ndi anthu kwa zaka zambiri. Enanso amaliona kuti ndi buku la mfundo za makhalidwe. Amatero chifukwa chakuti Baibulo lili ndi malamulo oposa 600 okhudza kaweruzidwe ka milandu, moyo wa banja, makhalidwe ndiponso chipembedzo, omwe Mulungu anapereka ku mtundu wa Isiraeli. Anthu enanso amaona Baibulo kuti ndi buku la malangizo auzimu lomwe limatiuza za maganizo a Mulungu.

Zonsezi n’zolondola. Baibulo limadzinenera lokha kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Indedi, zonse zopezeka m’Mawu a Mulungu monga nkhani za mbiri yakale, malamulo ndi malangizo auzimu, n’zothandiza.

Koma sikuti Baibulo langokhala buku la nkhani zosiyanasiyana zothandiza. Ilo ndi buku lapadera chifukwa ndi lochokera kwa Yehova Mulungu. Lili ndi malangizo ochokera kwa iye omwe ndi othandiza pamoyo. Limanenanso za cholinga cha Yehova cha dziko lapansi ndi anthu ndiponso mmene Mulungu adzathetsera mavuto a anthu. Chofunika kwambiri n’chakuti, Baibulo limatiuza kuti Mulungu wanenezedwa mabodza ndipo limafotokoza mmene iye adzathetsera mabodzawo.

Mulungu Ananenezedwa Kuti Ndi Wabodza Ndiponso Wolamulira Woipa

Baibulo limanena kuti Mulungu analenga anthu oyamba, Adamu ndi Hava, ali angwiro ndipo anawaika m’malo abwino kwambiri. Anawapatsa udindo wosamalira dziko ndi nyama. (Genesis 1:28) Monga ana a Mulungu, Adamu ndi Hava akanakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, malinga ngati akanamvera Atate wawo wakumwamba. Mulungu anawaletsa chinthu chimodzi basi. Iye anati: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:16, 17.

Koma mngelo wina amene Baibulo limam’tchula kuti Satana Mdyerekezi ananena zosiyana kwambiri ndi zimene Mulungu ananena. Iye anati: “Kufa simudzafai.” (Genesis 3:1-5) Potsutsa mwamphamvu zimene Mulungu ananena, Satana kwenikweni anati, Mlengi ndi wabodza ndiponso kuti iye salamulira bwino anthu koma anthuwo zingawayendere bwino popanda kulamulidwa ndi Mulungu. Satana anachititsa Hava kukhulupirira kuti kusamvera Mulungu kungam’chititse kukhala paufulu ndipo angamachite chilichonse chimene akufuna. Anamuuza kuti adzakhala “ngati Mulungu.” Choncho, Satana anaipitsa dzina labwino la Yehova ndiponso cholinga chake.

Zimene anakambiranazi zinayambitsa nkhani yaikulu. Ndipotu, mfundo yaikulu m’Baibulo ndi yonena za cholinga cha Yehova choyeretsa dzina ndi mbiri yake. Zimenezi zinafotokozedwa mwachidule m’pemphero la chitsanzo la Yesu, lomwe limadziwika kwambiri kuti Pemphero la Ambuye kapena Pemphero la Atate Wathu. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.”—Mateyo 6:9, 10.

Kodi Mulungu Adzayeretsa Bwanji Dzina Lake?

Zimene Satana ananena zinayambitsa mafunso ofunika kwambiri monga akuti: Kodi pakati pa Yehova ndi Satana ananena zoona ndani? Kodi Yehova amalamulira bwino ndiponso mwachilungamo chilengedwe chake? Kodi n’zoyenera kuti Mulungu aziyembekezera anthu kumumvera? Kodi anthu zingawayenderedi bwino atamadzilamulira okha? Kuti ayankhe mafunso amenewa, Yehova walola anthu kudzilamulira okha kwa nthawi ndithu.

Kodi zotsatira zake zakhala zotani? Kuchokera pamene Satana ananena bodza mu Edeni, anthu akhala akuvutika kwambiri, ndipo zimenezi zasonyeza kuti Satana ndi wabodza zedi ndi kuti kusadalira Mulungu kumabweretsa mavuto. Komabe, chifukwa cha chikondi ndi nzeru zake zosayerekezeka, Yehova ali ndi cholinga choyeretsa dzina lake mwa kuthetsa mavuto onse amene anayambira mu Edeni. Adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya kuchita zimenezi. Kodi Ufumu umenewu n’chiyani?

Ufumu wa Mulungu Udzathetsa Mavuto

Anthu mamiliyoni ambiri amapemphera Pemphero la Ambuye. Kodi munayamba mwaganizirapo tanthauzo la mawu a m’pemphero limeneli? Mwachitsanzo, taganizirani mawu akuti “Ufumu wanu ubwere.” (Mateyo 6:10) Ufumu umenewu suli mu mtima mwa munthu ngati mmene ena amaganizira. Koma ndi boma lenileni limene lili kumwamba ndipo mfumu yake ndi Yesu Khristu, “Mfumu ya mafumu.” (Chivumbulutso 19:13, 16; Danieli 2:44; 7:13, 14) Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu adzalamulira dziko lonse lapansi, ndipo adzakhazikitsa mtendere ndi mgwirizano pakati pa anthu ndiponso adzachotsa zoipa zonse padziko lapansi. (Yesaya 9:6, 7; 2 Atesalonika 1:6-10) Chotero, Ufumu wa Mulungu, osati boma lililonse la anthu, udzakwaniritsa mawu a Yesu akuti: “Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.”

Kuti akwaniritse mawu amenewa, Yesu anapereka moyo wake dipo lowombola ana a Adamu ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16; Aroma 6:23) Motero, anthu onse amene amakhulupirira nsembe ya Khristu adzaona Ufumu wa Mulungu ukuchotsa mavuto onse obwera chifukwa cha uchimo wa Adamu ndiponso adzaona pamene anthu pang’onopang’ono adzakhalanso angwiro. (Salmo 37:11, 29) Matenda onse, kuphatikizapo obwera chifukwa cha ukalamba, adzatheratu. Kuvutika maganizo chifukwa cha matenda kapena imfa kudzakhalanso ‘kutapita.’—Chivumbulutso 21:4.

N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake? Chifukwa chimodzi n’chakuti, ulosi wochuluka wa m’Baibulo wakwaniritsidwa kale. (Onani tsamba 9.) Choncho, n’zoonekeratu kuti kukhulupirira Baibulo si kupusa kapena kungotengeka maganizo, koma pali zifukwa zomveka ndiponso umboni wambirimbiri otichititsa kulikhulupirira.—Aheberi 11:1.

Malangizo Othandiza M’nthawi Yathu

Kuwonjezera pa kutipatsa chiyembekezo chodalirika, Baibulo limatithandizanso kukhala ndi moyo wosangalala kwambiri ngakhale panopa. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amatipatsa malangizo abwino kwambiri okhudza ukwati, moyo wa banja, kukhala bwino ndi anzathu, mmene tingapezere chimwemwe ndi zinthu zina zambiri. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

Tiziganiza kaye tisanalankhule. “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.”—Miyambo 12:18.

Tizipewa nsanje yosayenera. “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.”—Miyambo 14:30.

Tizilangiza ana athu. “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.”—Miyambo 22:6; 29:15.

Tizikhululuka. Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene ali achifundo, popeza adzachitiridwa chifundo.” (Mateyo 5:7) Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Chikondi chikwirira zolakwa zonse.” (Miyambo 10:12) Ngati munthu watilakwira chinthu chachikulu moti sitingathe kungokhululuka n’kuiwala, Baibulo limatilangiza kuti: “Pita kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo.”—Mateyo 18:15.

Tizipewa kukonda ndalama. “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.” (1 Timoteyo 6:10) Onani kuti Baibulo limanena kuti “kukonda ndalama” ndiko koipa osati ndalamazo.

“Kalata” Yochokera kwa Atate Wathu wa Kumwamba

Choncho monga mmene taonera, kwenikweni Baibulo limanena za Mulungu ndi cholinga chake. Limanenanso za anthufe ndi mmene tingakhalire ndi moyo wosangalatsa panopa ndi m’tsogolo pansi pa Ufumu wa Mulungu. Choncho, Baibulo lili ngati kalata yochokera kwa “Atate wathu wa kumwamba.” (Mateyo 6:9) Kudzera m’Baibulo, Yehova watiuza za maganizo ake apamwamba kwambiri ndipo watiuza za cholinga chake ndi makhalidwe ake osiririka.

Tikamawerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zomwe tikuwerengazo, timayamba kumuona Mulungu monga mmene alili, ndipo zimenezi zimatipangitsa kuyandikira kwa iye. (Yakobe 4:8) Kunena zoona, Baibulo sikuti langokhala buku la mbiri yakale, ulosi, ndi malamulo basi. Limatiuzanso mmene tingakhalire pa ubwenzi ndi Mulungu. Choncho, Baibulo ndi buku lapaderadi komanso lamtengo wapatali.—1 Yohane 4:8, 16.

[Chithunzi patsamba 19]

Mfundo yaikulu ya Baibulo inafotokozedwa mwachidule m’mawu oyamba a pemphero lachitsanzo la Yesu

[Bokosi/Chithunzi patsamba 21]

MMENE MUNGAWERENGERE BAIBULO

Baibulo ndi buku losangalatsa kwambiri kuwerenga. Ndipo nkhani ndi mfundo zake za makhalidwe abwino n’zodziwika bwino moti zimapezeka m’mabuku ambiri a zinenero zosiyanasiyana. Baibulo limatithandiza kudziwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Lilinso ndi nzeru zakuya. M’baibulo muli mwambi wakuti: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m’kutenga kwako konseko utenge luntha.” (Miyambo 4:7) Ndiyeno, kodi mungamawerenge bwanji Baibulo kuti mupindule nalo kwambiri?

Muziyesetsa kuwerenga Baibulo nthawi yomwe simunatope. Powerenga musamangofulumira n’cholinga choti mumalize basi. Cholinga chanu chizikhala kumvetsa ndi kudzaza maganizo anu ndi nzeru za Mulungu. Nthawi iliyonse mukamaliza kuwerenga, muzisinkhasinkha zimene mwawerengazo n’kuziyerekezera ndi zimene mukudziwa kale. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kumvetsa ndi kuyamikira zimene mukuwerenga.—Salmo 143:5.

Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi ndiyambire pati kuwerenga Baibulo?’ Mungayambire koyambirira. Komabe, ena akamayamba kumene kuwerenga Baibulo amaona kuti zimakhala zosavuta kuyambira ndi mabuku a Uthenga Wabwino a Mateyo, Maliko, Luka ndi Yohane, amene amafotokoza za moyo ndi utumiki wa Yesu. Kenako, amawerenga mabuku andakatulo olembedwa mosangalatsa, odzaza ndi nzeru a Masalmo, Miyambo, ndi Mlaliki. Ndipo munthu akamaliza mabukuwo, amakhala ndi chidwi chofuna kudziwa zimene zili m’mabuku enanso a Baibulo. (Onani m’munsimu.) Ndipo musatengere maganizo olakwika ongofuna kuwerenga chimene ambiri amati Chipangano Chatsopano. Kumbukirani kuti, “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16.

Njira yabwino kwambiri yowerengera Baibulo ndiyo kuphunzira nkhani iliyonse payokha. Mwachitsanzo, buku lophunzirira Baibulo lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lomwe limagwiritsidwa ntchito ndi a Mboni za Yehova akamalalikira, lili ndi nkhani zabwino kwambiri monga zakuti: “Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Likhale ndi Moyo Wosangalala,” “Kupembedza Kumene Mulungu Amavomereza,” ndi “Kodi Akufa Ali Kuti?”—Onani bokosi patsamba 18.

[Bokosi patsamba 21]

KUWERENGA BAIBULO NKHANI ILIYONSE PAYOKHA

Mmene moyo unayambira ndi kuchimwa kwa munthu Genesis

Chiyambi cha mtundu wa Isiraeli Eksodo mpaka Deuteronomo

Zochitika zochititsa chidwi Yoswa mpaka Estere

Ndakatulo ndi nyimbo zosangalatsa Yobu, Masalmo, ndi Nyimbo ya Solomo

Nzeru zothandiza pamoyo Miyambo ndi Mlaliki

Ulosi ndi malangizo a makhalidwe abwino Yesaya mpaka Malaki ndi Chivumbulutso

Moyo ndi ziphunzitso za Yesu Mateyo mpaka Yohane

Kuyamba ndi kufalikira kwa Chikhristu Machitidwe

Makalata opita ku mipingo Aroma mpaka Yuda