Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoona Kapena Zopeka?

Zoona Kapena Zopeka?

Zoona Kapena Zopeka?

Timoteyo, yemwe anali mkulu mumpingo wachikhristu, anachenjeza anthu amene anali ndi chidwi cholambira Mulungu woona kuti asamvere “chiphunzitso chosiyana” ndiponso “nkhani zonama.” (1 Timoteyo 1:3, 4) Kodi chenjezo limeneli n’lofunika masiku ano? Inde, ndi lofunika kwambiri chifukwa maganizo olakwika onena za Baibulo ndi zimene limaphunzitsa amachititsa anthu kuti asalambire Mulungu molondola. M’munsimu muli zikhulupiriro zofala zokhudza Baibulo zimene anthu osiyanasiyana ali nazo. Ndiyeno onani pansi pake mfundo zochokera m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusiyanitsa zinthu zoona ndi zopeka.

Zopeka: Zozizwitsa zotchulidwa m’Baibulo n’zosatheka kuchitika.

Zoona: Pali zinthu zambiri zimene anthu sadziwa zokhudza chilengedwe cha Mulungu. Palibe wasayansi yemwe angafotokoze bwinobwino za mphamvu ya dziko yokokera zinthu pansi, amene angadziwe zonse zimene zili mu atomu, kapena amene angafotokoze kuti nthawi n’chiyani kwenikweni. Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Kodi ukhoza kupeza [zakuya za, NW] Mulungu mwa kufunafuna? Ukhoza [kudziwa zonse za, NW] Wamphamvuyonse?” (Yobu 11:7) Popeza kuti n’zosatheka kudziwa zonse za chilengedwe, asayansi odziwa ntchito yawo ayamba kupewa kunena kuti zakuti sizingachitike.

Zopeka: Zipembedzo zonse n’zovomerezeka kwa Mulungu.

Zoona: Yesu ananena kuti: “Ngati mukhala m’mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga, mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) Ngati zipembedzo zonse n’zovomerezeka kwa Mulungu, kodi anthu ake angafunikire kumasulidwa? Ndipotu, Yesu anaphunzitsa kuti ndi anthu ochepa chabe omwe ali pa ‘msewu wa kumoyo.’—Mateyo 7:13, 14.

Zopeka: Anthu onse abwino akafa amapita kumwamba.

Zoona: Baibulo limati: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha. Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.” (Salmo 37:11, 29, 34) Ndi anthu okhulupirika 144,000 okha amene ali opita kumwamba. Mulungu wawapatsa anthu amenewa ntchito ‘yodzalamulira dziko lapansi monga mafumu.’—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 4.

Zopeka: “Chipangano Chakale” sichigwiranso ntchito pa Akhristu.

Zoona: Baibulo limati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Limatinso: “Zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Mu “Chipangano Chakale,” kapena kuti Malemba Achiheberi, muli malangizo auzimu ofunika kwambiri ndipo amatithandiza kukhulupirira “Chipangano Chatsopano,” kapena kuti Malemba Achigiriki Achikristu.

Zopeka: Nkhani zambiri za m’buku la Genesis, kuphatikizapo nkhani ya Adamu ndi Hava, ndi nthano chabe.

Zoona: Mu uthenga wake wabwino, Luka analemba za mzera wobadwira wa Yesu womwe umayambira pa Adamu. (Luka 3:23-38) Ngati nkhani za m’buku la Genesis ndi zopeka, kodi mayina enieni a m’mzera umenewu anathera pati ndipo ongopekawo anayambira pati? Ngakhale Yesu, yemwe anali kumwamba asanabwere padziko lapansi, ankakhulupirira nkhani za mu Genesis, kuphatikizapo za Adamu ndi Hava. (Mateyo 19:4-6) Choncho, kukayikira nkhani za mu Genesis ndi chimodzimodzi ndi kukayikira kuti Yesu ngakhalenso olemba Baibulo ambiri ankanena zoona.—1 Mbiri 1:1; 1 Akorinto 15:22; Yuda 14.