Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anabadwa Liti?

Kodi Yesu Anabadwa Liti?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Yesu Anabadwa Liti?

BUKU lina la maumboni limati: “Tsiku lenileni la kubadwa kwa Khristu silikudziwika.” (Encyclopedia of Early Christianity) Komabe, padziko lonse anthu ambiri amene amati ndi Akhristu, amakumbukira kubadwa kwa Yesu pa 25 December. Koma tsiku limeneli silimapezeka m’Baibulo. Kodi Yesu anabadwadi mu December?

Ngakhale kuti Baibulo silitchula tsiku lenileni limene Yesu anabadwa, komabe lili ndi umboni wosonyeza kuti Yesu sanabadwe mu December. Komanso, umboni wa m’mabuku ena umasonyeza chifukwa chake anthu anasankha 25 December kukhala tsiku lokumbukira kubadwa kwa Yesu.

Mfundo Zosonyeza Kuti Yesu Sanabadwe mu December

Yesu anabadwira ku Yudeya mu mzinda wa Betelehemu. Uthenga Wabwino wa Luka umati: “M’dzikomo munalinso abusa amene anali kugonera ku busa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda.” (Luka 2:4-8) Izi sizinali zachilendo. Buku lina limati: “Nthawi zambiri pachaka nkhosa zinkakhala panja.” (Daily Life in the Time of Jesus) Koma kodi abusa akanakhala ndi nkhosa zawo panja usiku mu December kunja kukuzizira? Bukuli limanenanso kuti: “Nkhosa zinkakhala m’khola nyengo yonse ya dzinja; chifukwa cha mfundo imeneyi munthu akhoza kuona kuti tsiku lodziwika la Khirisimasi, la m’nthawi ya dzinja, silingakhale lolondola, popeza Uthenga Wabwino umati abusa anali ali kuthengo.”

Mfundo imeneyi ikugwirizana ndi mfundo ina ya mu Uthenga Wabwino wa Luka yakuti: “M’masiku amenewo, Kaisara Augusito analamula kuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula; (kulembetsa m’kaundula kumeneku kunali koyamba, ndipo kunachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Suriya;) anthu onse anapita kukalembetsa, aliyense ku mzinda wa kwawo.”—Luka 2:1-3.

N’kutheka kuti Augusito analamula kuchita kalembera ameneyu kuti apeze nambala ya anthu ofunika kupereka msonkho ndiponso oyenera kuwalemba usilikali. Pomvera zimenezi, Mariya ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kubereka, anapita ndi mwamuna wake, Yosefe, ku Betelehemu kuchokera ku Nazareti, ulendo wa makilomita 150. Tsopano ganizirani izi: Kodi Augusito, wolamulira amene zochitika za m’madera ena sizimam’khudza kwenikweni, akanauza anthu amene amafuna kum’pandukira kuti ayende ulendo wautali ngati umenewo m’nthawi yozizira?

Akatswiri ochuluka a mbiri yakale ndiponso a Baibulo savomereza kuti Yesu anabadwa pa 25 December. Mosakayikira mungapeze zimenezi m’mabuku ena a maumboni. Buku lina limati: “Anthu ambiri amaona kuti Yesu sanabadwe pa 25 December.”—Our Sunday Visitor’s Catholic Encyclopedia.

Chifukwa Chake Anasankha 25 December

Patapita zaka zambiri Yesu atamwalira, anthu anasankha tsiku la 25 December kukhala limene Yesu anabadwa. Kodi anasankhiranji tsiku limeneli? Akatswiri a mbiri yakale ochuluka amakhulupirira kuti nthawi ya pachaka imeneyi yomwe anthu anasankha kuchita Khirisimasi, kwenikweni inali yochita miyambo yachikunja.

Mwachitsanzo, buku lina la maumboni linati: “Anthu ambiri amati tsiku la 25 December analikhazikitsa pofuna kuti mwambo wa dies solis invicti nati (‘tsiku la kubadwa kwa dzuwa losagonjetseka’), usanduke wachikhristu. Umenewu unali mwambo wotchuka kwambiri mu Ufumu wa Roma umene unkachitika m’nthawi yozizira monga chizindikiro cha kubadwa kwa dzuwa, kutha kwa nthawi yozizira ndi kuyamba kwa nthawi yotentha.”—Encyclopæedia Britannica.

Buku linanso la maumboni limatiuza kuti: “Chifukwa chimene anakhazikitsira 25 December kukhala tsiku la Khirisimasi sichikudziwika bwinobwino. Koma anthu ambiri amakhulupirira kuti anasankha tsiku limeneli kuti ligwirizane ndi mapwando achikunja okondwerera ‘kubadwanso kwa dzuwa’ amene ankachitika m’nyengo yozizira, nthawi imene dzuwa limayamba kuchedwa kulowa. . . . Phwando lachiroma lotchedwa Saturnalia (limene ankalichita posangalatsa Saturn, mulungu wa zaulimi ndiponso wa dzuwa), linkachitikanso panthawi imeneyi.” (Encyclopædia Americana) Nthawi zambiri anthu pa mapwando amenewa ankachita zachiwerewere komanso amasangalala monyanyira. Ndipo masiku ano, zimenezi n’zomwe zimachitikanso pa mapwando ambiri akhirisimasi.

Kodi Khristu Tingamulemekeze Bwanji?

Ngakhale kuti tsiku lenileni la kubadwa kwa Yesu silidziwika, anthu ena amaganiza kuti Akhristu afunika kumakumbukirabe kubadwa kwake. Iwo amaganiza kuti ngati achita mwambowu mwaulemu ndiye kuti akulemekeza Khristu.

N’zoona kuti kubadwa kwa Yesu ndi nkhani yapadera m’Baibulo. Ndipotu Baibulo limanena kuti Yesu atabadwa, khamu lalikulu la angelo linaoneka mwadzidzidzi ndipo linatamanda Mulungu mosangalala, likumati: “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.” (Luka 2:13, 14) Komabe chochititsa chidwi n’chakuti, m’Baibulo mulibe pamene pamanena kuti tizikumbukira kubadwa kwa Yesu. Koma muli lamulo lakuti tiyenera kukumbukira imfa yake, ndipo Mboni za Yehova zimachita mwambo umenewu kamodzi pachaka. (Luka 22:19) Imeneyi ndi njira imodzi imene tingalemekezere Yesu.

Usiku wake womaliza ali padziko lapansi pano, Yesu anati: “Mukhalabe mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.” (Yohane 15:14) Iye ananenanso kuti: “Ngati m’mandikonda ine, mudzasunga malamulo anga.” (Yohane 14:15) Ndithudi, palibe njira ina yolemekezera Yesu Khristu yoposa kuphunzira ndi kutsatira zimene anaphunzitsa.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sanabadwe mu December?—Luka 2:1-8.

▪ Kodi chofunika n’chiyani kuposa tsiku limene munthu anabadwa?—Mlaliki 7:1.

▪ Kodi ndi njira iti yabwino kwambiri yolemekezera Yesu?—Yohane 14:15.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Baibulo lili ndi umboni wosonyeza kuti Yesu sanabadwe mu December

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi abusa akanakhala ndi nkhosa kunja usiku nthawi yozizira kwambiri?

[Mawu a Chithunzi]

Todd Bolen/​Bible Places.com