Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Chikodzera Chimadzitetezera

Mmene Chikodzera Chimadzitetezera

Panagona Luso!

Mmene Chikodzera Chimadzitetezera

▪ Ngakhale kuti kachilombo ka chikodzera n’kakang’ono pafupifupi masentimita awiri, n’kodziwika ndi njira yake yapadera yodzitetezera. Kachilomboka kakadzidzimutsidwa ndi zinthu monga akangaude, mbalame ngakhale achule, kamatulutsa madzi kumchira kwake pofuna kudziteteza. Madzi amenewa amakhala otentha komanso onunkha kwambiri.

Taganizirani izi: Kachilomboka kali ndi “tinthu tina totulutsira madzi kumchira [kwake].” Mkati mwa tinthu timeneti muli malo osungirako mpweya wa asidi ndi mpweya wina umene umakhala ndi okosijeni wambiri. Komanso muli malo ena omwe mpweyawu umasakanikirana ndi madzi. Ndipo pofuna kuti kachilomboka kadziteteze, madzi ndi mpweyawu zimasakanikirana. Zikatere, kodi chimachitika n’chiyani? Kamatulutsa madzi a poizoni onunkha komanso otentha kwambiri. Ngakhale kuti malo amene kamasungiramo komanso kusakanizira madzi ndi mpweyawu ndi aang’ono kwambiri, osafika 1 milimita, kachilomboka kamatha kusintha katulukidwe ndiponso kuchuluka kwa poizoniyo.

Akatswiri ena afufuza kachilomboka kuti adziwe mmene angapangire zipangizo zopopera mankhwala zabwino kwambiri komanso zosawononga chilengedwe. Iwo apeza kuti kachilomboka kali ndi njira yolowetsera madzi kuti asakanikirane ndi mpweya komanso kali ndi njira ina yotulutsira poizoni. Akatswiri a luso la zopangapanga akufuna kudzagwiritsa ntchito luso la kachilombo kameneka popanga mainjini a galimoto, zinthu zozimitsira moto komanso popanga zipangizo zogwiritsa ntchito popereka mankhwala kwa odwala. Pulofesa Andy McIntosh wa pa yunivesite ya Leeds ku England, anati: “Palibe amene wafufuza kachilombo ka chikodzera pankhani ya sayansi ya kapangidwe ka zinthu monga tachitira ife, ndipo taphunzira zambiri ku kachilombo kameneka.”

Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi njira yodzitetezera yodabwitsa ya kachilomboka inangochitika mwangozi? Kapena kodi pali Mlengi wanzeru amene anapanga zimenezi?

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Oxford Scientific/photolibrary