Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Ana Amene Ali ndi Vuto Lophunzira

Kuthandiza Ana Amene Ali ndi Vuto Lophunzira

Kuthandiza Ana Amene Ali ndi Vuto Lophunzira

YOLEMBEDWA KU MEXICO

Steven amalephera kuwerenga bwino ndipo akangodziwa kuti aphunzitsi ake akufuna kumuuza kuti awerenge m’kalasi, amachita mantha kwambiri moti amayamba kumva kupweteka m’mimba.

Maria amalephera kulemba zooneka bwino, ngakhale kuti aphunzitsi ake amayesetsa kumulimbikitsa kuti azilemba bwino. Akamupatsa ntchito yoti akalembere kunyumba, zimamutengera nthawi yaitali kuti amalize.

Noah amawerenga kwambiri pokonzekera mayeso. Koma panthawi ya mayesowo, iye amaiwala zonse zimene anawerenga zija ndipo sakhoza bwino.

STEVEN, Maria ndi Noah ali ndi vuto lophunzira zinthu. Nthawi zambiri munthu amene ali ndi vutoli amalephera kuwerenga. Mwachitsanzo, ena amene ali ndi vutoli nthawi zambiri amalephera kusiyanitsa zilembo zooneka ngati zofanana. Enanso amalephera kulemba zooneka bwino, pomwe ena amavutika ndi masamu. Komabe, ambiri mwa ana amene ali ndi vuto lophunzira zinthu, amakhala anzeru ndithu.

Mwana amene ali ndi vutoli amachedwa kulankhula, amavutika kutchula mawu ofanana ndiponso amalephera kutchula mawu molondola. Komanso akamakula, amalankhulabe ngati mwana wamng’ono, amavutika kuzindikira zilembo ndi manambala, amalephera kutchula zilembo momveka bwino ndiponso amalephera kutsatira malangizo. *

Zimene Mungachite Kuti Muthandize Mwana Wanu

Kodi mungatani ngati mwana wanu akuoneka kuti amavutika kuti aphunzire zinthu? Choyamba, pitani naye kuchipatala kuti akamuyeze ngati ali ndi vuto la kumva kapena kuona. * Akapezeka ndi mavuto amenewa, pezani chithandizo cha mankhwala. Dziwani kuti mwana wotereyu amafunika kumusamalira mwapadera. Ndiponso musaiwale kuti mwana wanu akakhala ndi vutoli, sizitanthauza kuti ndi wopanda nzeru.

Kuwonjezera pa zimene amaphunzira ku sukulu, mungamupezerenso mphunzitsi woti azim’phunzitsa mwapadera akaweruka. M’pempheni mphunzitsiyo kuti azithandiza mwanayo mwakhama. Ndiponso mungapemphe aphunzitsi ake kuti azionetsetsa kuti mwanayo azikhala kutsogolo m’kalasi, komanso azim’patsa nthawi yambiri yoti alembe ntchito imene am’patsa. Mwinanso aphunzitsi ake akhoza kumuuza zoti akawerenge, kenako n’kungomufunsa mafunso apakamwa m’malo moti achite kulemba. Popeza kuti mwana amene ali ndi vutoli amaiwalaiwala ndiponso sachita zinthu mwadongosolo, zingakhale bwino kuti akhalenso ndi makope ena oti azigwiritsa ntchito kunyumba. Ngati zili zotheka, mwanayo angapatsidwenso kompyuta yoti azigwiritsa ntchito ku sukulu ndiponso kunyumba.

Ngati mwana wanu amavutika kuwerenga, tsiku lililonse muzimpatsa zinthu zochepa zoti awerenge. Ndi bwino kuti mwanayo aziwerenga mokweza kuti inuyo muzimvetsera ndi kuona mmene mungam’thandizire. Choyamba, inuyo werengani ndipo mwanayo azikutsatirani. Kenako, werengani limodzi naye mokweza. Ndiyeno, muuzeni kuti awerenge yekha. Akamawerenga, muziloza mawuwo ndiponso muzidula mzere kunsi kwa mawu amene akumuvuta. Zonsezi zingakutengereni mphindi 15 zokha patsiku.

Mwana amene masamu amamuvuta, angaphunzitsidwe potsatira njira zosavuta monga kumusonyeza mmene mumayezera kuchuluka kwa zinthu zoti muphike, m’mene mungayezere matabwa, kapena kupita naye kokagula zinthu. Mungamuthandizenso pomupatsa buku lomwe lili ndi zojambula za masamu ndiponso kope la mizere ya timabokosi kuti azilembamo masamu. Kwa ana amene amalephera kulemba zooneka bwino, mungawapatse pensulo ndi kope la mizera yotalikirana ndiponso yooneka bwino. Mukhozanso kulemba papepala zilembo zikuluzikulu, n’kumata pakhoma kuti mwanayo aziwerenga.

Palinso njira zina zimene mungachite pothandiza mwana amene ndi wosakhazikika, wojijirika ndiponso amene amalephera kumvetsera. Mwachitsanzo, musanayambe kulankhula ndi mwana amene ali ndi vutoli, muyang’anizane naye kaye. Muzionetsetsa kuti mwana wanu ali pamalo opanda phokoso akamachita ntchito yake yakusukulu ndiponso muzimulola kuti azipumira. Popeza mwana yemwe ali ndi vutoli amakhala wojijirika, nthawi zonse yesetsani kumam’patsa zochita zoti zizimutanganitsa.

N’zotheka Kuthana ndi Vutoli

Onani mbali zimene mwana wanu akuchita bwino ndiponso luso limene ali nalo ndipo mulimbikitseni kukulitsa lusolo. Muzimuyamikira komanso kum’patsa mphatso akachita zabwino, ngakhale zitakhala zazing’ono. Pom’patsa zoti alembe kapena kuwerenga, musam’patse zambiri nthawi imodzi. Zimenezi zingathandize kuti azisangalala chifukwa choona kuti wayamba kukhoza. Gwiritsani ntchito zithunzi kapena zojambulajambula zina zosonyeza mmene angagwirire ntchitoyo, kuti aimalize mosavuta.

M’pofunika kwambiri kuti mwana wanu adziwe masamu, kuwerenga, ndiponso kulemba. Dziwani kuti mukamamulimbikitsa ndiponso kumuthandiza, mwana wanu angakwanitse kuchita zimenezi ngakhale kuti mwina zingamutengere nthawi poyerekeza ndi ana ena.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ana amene ali ndi vutoli, nthawi zambiri amakhala osakhazikika, ojijirika ndiponso amalephera kumvetsera. Onani Galamukani! ya March 8, 1997, masamba 27 mpaka 31.

^ ndime 9 Anyamata ndi amene amapezeka kwambiri ndi vutoli poyerekezera ndi atsikana.

[Bokosi patsamba 11]

KUWERENGA MOVUTIKIRA KWANDITHANDIZA M’NJIRA ZINA

“Ndinkati ndikatsegula buku, panalibe chimene ndinali kuona ndipo sindinkatha kuwerenga chilichonse moti zilembozo zinkangooneka ngati za chinenero china. Kuti ndidziwe zimene zalembedwazo, winawake amachita kundiwerengera. Aphunzitsi anga ankaganiza kuti ndine waulesi, wamwano ndiponso sindimvetsera iwo akamaphunzitsa. Koma zimenezi sizinali zoona. Ndinkamvetsera komanso kulimbikira, koma zinkandivutabe kuti ndiphunzire kuwerenga ndi kulemba. Komabe, maphunziro ena monga masamu sankandivuta. Pamene ndinali mwana, sindinkachedwa kuphunzira zinthu zikakhala zosakhudzana ndi kulemba kapena kuwerenga, monga masewera olimbitsa thupi komanso ntchito zina zamanja.

“Patapita nthawi, ndinaganiza kuti ndizingogwira ntchito za manja. Zimenezi zandithandiza kuti ndikhale ndi mwayi wogwira nawo ntchito zomangamanga m’gulu la Mboni za Yehova, m’mayiko okwana asanu. Chifukwa choti ndimafunika kuchita khama kwambiri kuti ndikwanitse kuwerenga, ndimayesetsa kuti ndisaiwale zimene ndawerengazo. Popeza kuti ndine wa Mboni, khama limeneli limandithandiza kwambiri makamaka pantchito yolalikira. Choncho m’malo momangodandaula ndi vutoli, ndimaona kuti landithandiza kwambiri kuchita zinthu zina zofunika kwambiri.”—Anatero Peter, wa Mboni za Yehova, yemwe ndi mtumiki wa nthawi zonse koma ali ndi vuto lolephera kuwerenga.

[Chithunzi patsamba 10]

Ana sangachedwe kuphunzira zinthu akamamvetsera mwatcheru ndiponso kujambula zithunzi zosonyeza zimene akuphunzirazo