Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Madzi Ndi Moyo

Madzi Ndi Moyo

Madzi Ndi Moyo

MADZI ndi chinthu chovuta kuchimvetsa. Amapangidwa ndi tinthu ting’onoting’ono tosaoneka ndi maso timene timapezeka mumpweya. Mpaka pano asayansi samvetsa mmene tinthu timeneti timalumikizirana n’kupanga kadontho ka madzi. Komabe tonse timadziwa kuti madzi ndi moyo. Ndipo mbali yaikulu ya chinthu chilichonse chamoyo ndi madzi. Tiyeni tione zinthu zisanu zokha zochititsa chidwi kwambiri zokhudza madzi.

1. Madzi satentha msanga ndipo izi zimathandiza kuti dziko lisamatenthe kwambiri.

2. Madzi oundana amapepuka choncho amayandama ndipo izi zimateteza madzi a pansi kuti asatenthe kwambiri kapena kuzizira kwambiri. Madzi akanakhala kuti amalemera akaundana, bwenzi madzi onse a m’nyanja ndi m’mitsinje ataundana ndipo zamoyo zonse zam’madzi zikanauma.

3. Kuwala kumayenda bwinobwino m’madzi ndipo izi zimathandiza kuti zamoyo za pansi penipeni pa nyanja zisafe.

4. Madontho a madzi ali ndi mphamvu yotha kumatirirana. N’chifukwa chake madzi amatha kuyenda kuchoka pansi kupita m’mwamba mkati mwa mitengo ngakhale itakhala yaitali kwambiri, ndipo n’chifukwa chakenso tizilombo tina timatha kuthamanga bwinobwino pamwamba pa madzi.

5. Madzi ndiwo chinthu chabwino koposa chosungunulira zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo madzi amatha kusungunula bwinobwino zinthu monga mchere wosiyanasiyana, mpweya wamitundumitundu, komanso zinthu zina zambiri zofunika m’thupi.

Amathandiza Kuti Nyengo Ikhale Yabwino

Mbali yaikulu ya dziko lapansili ndi nyanja ndipo nyanja zimenezi zimathandiza kwambiri kuti nyengo izikhala yabwino. Mphepo ndi mafunde zimachititsa kuti madzi, mpweya, ndi kutentha ziziyenda kuchoka m’nyanja kupita m’mlengalenga n’kubwereranso. Nyanja ndi mphepo zimathandizanso kuti mpweya wa m’madera otentha kwambiri ufike m’madera ozizira. Ndipo zimenezi zimachititsa kuti nyengo ya padziko lonse ikhale yabwino. Madzi ambiri atati aundane kapena kusanduka nthunzi, zamoyo zambiri zikhoza kufa. Buku lina linati:“Zikuoneka kuti nyengo ya padzikoli ndi yolinganizidwa bwino kwambiri” moti zimenezi sizingachitike.—Rare Earth—Why Complex Life Is Uncommon in the Universe.

Poganizira zonsezi, kodi mukuganiza kuti dzikoli linangokhalapo mwangozi kapena linachita kulengedwa ndi Mlengi wanzeru komanso wachikondi? Baibulo limasonyeza kuti linachita kulengedwa. (Machitidwe 14:15-17) Nkhani yotsatirayi ikusonyeza umboni wa zimene Baibulo limanenazi. Ikufotokoza kayendedwe ka zinthu zina kamene kamachititsa kuti dzikoli likhale labwino kwambiri.

[Bokosi patsamba 7]

BAIBULO NDI LOLONDOLA PANKHANI ZA SAYANSI

Dziko lili m’malere. “Ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.”—Yobu 26:7, zimenezi zinanenedwa cha m’ma 1613 B.C.E.

Dzikoli ndi lozungulira. “Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi [lozungulirali, NW].”—Yesaya 40:22, zimenezi zinalembedwa cha m’ma 732 B.C.E.

Madzi akapita kumwamba amabwereranso. “Mitsinje yonse ithira m’nyanja . . . komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.”—Mlaliki 1:7, zimenezi zinalembedwa chaka cha 1,000 B.C.E. chisanafike

Pali malamulo amene chilengedwe chimayendera. ‘Yehova atero . . . ndinalemba malemba [kapena kuti malamulo] a kumwamba ndi dziko lapansi.’—Yeremiya 33:25, zimenezi zinalembedwa chaka cha 580 B.C.E chisanafike

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

Magnetosphere: NASA/Steele Hill; aurora: Collection of Dr. Herbert Kroehl, NGDC; reef: Stockbyte/Getty Images