Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kalankhulidwe” Kogometsa Koimba Likhweru

“Kalankhulidwe” Kogometsa Koimba Likhweru

“Kalankhulidwe” Kogometsa Koimba Likhweru

YOLEMBEDWA KU MEXICO

▪ Anthu a mtundu wotchedwa Mazateki omwe amakhala m’dera lakumapiri la Oaxaca m’dziko la Mexico alibe matelefoni amtundu uliwonse. Komabe amatha kulankhulana ngakhale atatalikirana pamtunda wamakilomita awiri kapena kuposa pamenepa, mwachitsanzo akamagwira ntchito m’minda ya khofi yomwe ili m’mphepete mwamapiri. Kodi chinsinsi chawo chagona pati? Anthu amenewa anatulukira chinenero choimba malikhweru. Mnyamata wina wa kumeneku, dzina lake Pedro ananena kuti: “Tikamalankhula chinenero cha Chimazateko timakhala ngati tikuimba. Motero tikamaimba malikhweru, timatengera mmene mawuwo amamvekera m’chinenero chathuchi. Ndipo timaimba malikhweruwa ndi milomo basi popanda kugwiritsa ntchito zala zathu.” *

Mnzake wa Pedro dzina lake Fidencio anafotokoza ubwino wolankhula poimba malikhweru. Iye anati: “Timatha kulankhulana ngakhale titatalikirana kwambiri. Mwachitsanzo, bambo amatha kutuma mwana wake kukagula mikate, kenako n’kukumbukira kuti waiwala kumuuza kuti akagulenso tomato. Ndiye mwanayo akakhala kuti ali patali, bamboyo amatha kungomuimbira likhweru n’kumuuza zimene anaiwalazo.”

Nawonso a Mboni za Yehova nthawi zina amaimba likhweru akamalankhulana. Pedro anati: “Ndikafuna kumuitana mnzanga kuti tipitire limodzi kwinakwake, ndimangomuimbira likhweru basi m’malo moyenda chiulendo kupita kwawo kukamutenga.”

Pedro ananenanso kuti: “Aliyense amayimba likhweru m’njira yakeyake kuti tizitha kudziwa amene akulankhula. Kawirikawiri ndi amuna okha amene amalankhula poimba likhweru ku dera limeneli. Akazi amachidziwanso chinenerochi ndipo amatha kuchigwiritsa ntchito pabanja pawo, koma salankhulana ndi amuna ena m’chilankhulochi. Kumeneku kungaoneke ngati kupanda khalidwe.”

Sikuti ndi anthu amtundu wa Mazateki okha amene amalankhulana poimba likhweru. Pali anthu enanso amene amalankhulana m’njira imeneyi ku Papua New Guinea, ku China ndi kuzilumba zotchedwa Canary Islands. Kawirikawiri anthu amenewa amakhala kumapiri kapena kunkhalango zowirira. N’kutheka kuti pali zinenero zoposa 70 zogwiritsira ntchito malikhweru, koma pa zinenerozi ndi 12 zokha zimene akatswiri afufuza.

Luso limene anthu ali nalo n’logometsa zedi. Mutati muganizire nzeru zodabwitsa zimene anthu ali nazo komanso chikhumbo chofuna kulankhulana ndi anthu ena, mutha kuona kuti palibe chimene chingatilepheretse anthufe kulankhulana. Kunena zoona anthufe tingathe kuchita zinthu zambiri kungoti timadziderera.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Buku lina limati: “Anthu a mtundu wa Mazateki amatha kukambirana zinthu zambirimbiri pongosinthasintha kamvekedwe ka malikhweru.”