Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi pa Chithunzichi Pakusowa Chiyani?

Werengani 1 Mafumu 18:19-24, 30-40. Tsopano yang’anani pachithunzicho. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikusowapo? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani Yehova analandira nsembe ya Eliya? Kodi Yehova amalandira nsembe zotani kuchokera kwa atumiki ake masiku ano?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA  7 Kodi Yehova walenjeka dzikoli pa chiyani? Yobu 26:․․․

TSAMBA 9 Kodi ndi ntchito za ndani zimene zinapangidwa mwanzeru? Masalmo 104:․․․

TSAMBA  13 Kodi tingatani kuti tisankhe moyo? Deuteronomo 30:․․․

TSAMBA  20 Kodi Yehova amapereka chiyani munthu akamapemphera kwa Iye ndi mtima wonse? Afilipi 4:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Kodi Mumawadziwa Bwino Aneneri?

4. ․․․․․

Mfumu ya Yuda dzina lake Yoasi itachita zoipa, kodi ndi mneneri uti amene anaidzudzula?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 24:20-22.

5. ․․․․․

Mfumu Yoasi inapha mneneriyu chifukwa choidzudzula. Kodi izi zikutanthauza kuti Yehova sanasangalale ndi zimene mneneriyu anachita?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 11:50, 51.

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani simuyenera kudandaula anthu akamakuzunzani chifukwa choti mumamvera Yehova?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 5:11, 12 ndi 1 Petulo 4:14.

▪ (Mayankho ali pa tsamba 27)

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Ng’ombe yoti iperekedwe nsembe.

2. Ngalande yodzaza madzi.

3. Aneneri a Baala 450 komanso ena ambirimbiri amene anabwera kudzaonera.

4. Zakariya mwana wa Yehoyada.

5. Ayi.