Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyama ndi Zomera Zikutha

Nyama ndi Zomera Zikutha

Nyama ndi Zomera Zikutha

YOLEMBEDWA KU SPAIN

NYAMA ndiponso zomera zambiri zikuwonongedwa padziko lonse. Akatswiri ena a sayansi amati masauzande a mitundu yosiyanasiyana ya nyama ndi zomera zikutha chaka chilichonse. Komabe nyama ndi zomera zambiri zimene zikutha m’madera ambiri, zikupezekabe kumapiri. Ngakhale zili choncho, anthu owononga zachilengedwe ayambanso kuwononga nyama ndi zomera zimenezi. Izi zikuchitika kwambiri ku Ulaya kumene kuli chiwerengero chachikulu cha anthu.

Mapiri amene ali pakati pa dziko la France ndi Spain ali ndi malo ambiri otetezerako nyama ndiponso zomera. Kumalo amenewa, alendo amapitako kuti akaone nyama zimene sizikupezekanso m’madera ena. Tiyeni tione nyama ndi zomera zimene zimapezeka ku malo amenewa.

Mitundu ya Nyama ndi Zomera Zimene Mungazipeze ku Malowa

Maluwa. Ena mwa maluwa am’tchire okongola kwambiri amakonda kupezeka ku mapiri aatali mamita 1,500. Maluwa ooneka ngati maluwa a therere lobala (1), amamera mothinana ndipo ukawaonera patali amaoneka ngati kapeti ya buluu. Cham’munsi mwenimweni mwa mapiriwo muli mitengo ya thundu ndipo m’katikati mwa mitengoyi mumamera maluwa apinki ooneka ngati chibaluni (2). Anthu ambiri okonda zinthu zachilengedwe amapita kukaona malowa chaka chilichonse. Choncho, anthu oyang’anira nkhalango amalondera malowa kwa maola 14 tsiku lililonse kuti maluwa amenewa asawonongedwe kapena kuzulidwa.

Agulugufe. Kumeneko kuli minda yambiri ya maluwa am’tchire okongola amene amakopa agulugufe. Kumapezeka mtundu wina wa agulugufe akuluakulu (3), okhala ndi mapiko a madontho ofiira. Agulugufewa amakonda kuuluka ndi kutera m’maluwa. Agulugufe ena abuluu ndiponso agulugufe akhofi (4)  amakonda kutera pa maluwa ang’onoang’ono. Palinso agulugufe ena achikasu ndi mathotho akuda omwe amaulukauluka m’malo otsika a m’derali.

Nyama. Poyamba nyama zambiri zikuluzikulu za ku Ulaya zinkapezeka madera ambiri m’dzikoli. Koma anthu akumazipha kwambiri ndipo zatsala pang’ono kutha. Nkhandwe, zimbalangondo, amphaka akuluakulu a mthengo (5), njati, zinkhoma ndi mbuzi za m’mapiri (6) tsopano zimangopezeka m’mapiri ena akutali. Nyama zimenezi zimawakumbutsa anthu za nyama zambirimbiri zimene kale zinkapezeka m’derali. Alendo ena odzaona malowa amakayikira ngati nyama zimenezi zidzapitirire kupezeka.

Sitikayikira n’komwe kuti Mlengi wathu Yehova, yemwe ndi mwini wake wa “chuma cha m’mapiri,” amasamalira nyama zimenezi. (Salmo 95:4) M’lemba lina la Salmo, Mulungu anati: “Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m’mapiri.” (Salmo 50:10, 11) Yehova amakonda kwambiri dziko lapansi ndi zamoyo zake kuphatikizapo nyama za kumapiri ndipo sadzalola kuti ziwonongeke.

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Maluwa ooneka ngati maluwa a therere lobala

Maluwa apinki ooneka ngati chibaluni

Agulugufe akuluakulu

Agulugufe akhofi

Amphaka akuluakulu a mthengo

Mbuzi za m’mapiri

[Mawu a Chithunzi]

La Cuniacha