Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makolo Thandizani Ana Anu

Makolo Thandizani Ana Anu

Makolo Thandizani Ana Anu

MAKOLO amene amakonda ana awo, amafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri akumwa mankhwala mozemba?” Pali zifukwa zosiyanasiyana. Achinyamata ena amangofuna kusangalala. Ena amafuna kuti aiwale mavuto kapena aziwerenga kwambiri. Enanso amamwa mankhwalawo akamadwala kapena akasokonezeka maganizo. Panopa ana, ngakhale a zaka 12, akugwiritsa ntchito mankhwala mwachisawawa ndipo nthawi zambiri amaitanitsa mankhwala kudzera pa Intaneti chifukwa chakuti amangowagulitsa popanda kuwafunsa zambiri. Ena amagula mankhwala kuchokera kwa anzawo. Kodi makolo mungatani kuti muthandize ana anu?

Choyamba, langizani ana anu kuti kumwa mankhwala akuchipatala mwachisawawa kapena kumwa mankhwala ozunguza bongo, n’koopsa. Komanso muzisunga mankhwala akuchipatala pamalo poti ana sangafikepo, mwina kuwatsekera pabwino. Muzidziwa mankhwala amene muli nawo ndiponso mmene akuthera. Ngati mankhwala enaake mwathana nawo, atayeni. Ngati mwana wanu wachira koma akumwabe mankhwala, m’funseni kuti afotokoze chifukwa chake. Komanso muzionetsetsa zimene mwana wanu akuchita pa Intaneti. Ndiponso muzionetsetsa anthu amene iye akucheza nawo, mmene iye akuonekera, khalidwe lake kapena mmene akukhozera kusukulu.

Ngati Mwana Wanu Ali ndi Vuto Logwiritsa Ntchito Mankhwala

Kodi mungatani ngati mwana wanu ali ndi vuto logwiritsa ntchito mankhwala mosayenera, kapena ngati mukungokayikira kuti ali ndi vutoli? Muyenera kukambirana naye mwana wanuyo mwachikondi. Baibulo limati: “Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” (Miy. 20:5) Kudziwa zoona zokhudza mwana wanu amene mukumuganizira kuti ali ndi vuto la mankhwala kungafanane ndi kutunga madzi m’chitsime chakuya pogwiritsira ntchito chingwe chosalimba. Ngati mutachikoka kwambiri chingaduke. N’chimodzimodzinso ndi mwana, mukamukalipira kwambiri, mungalephere kukambirana naye. Dziwani kuti zolinga zanu ndi ziwiri. Choyamba, mukufuna kudziwa vuto lake. Ndipo chachiwiri, mukufuna kudziwa zinthu zimene zayambitsa vutoli. Zinthuzo zingakhale izi:

Kucheza ndi anthu olakwika. Lemba la 1 Akorinto 15:33 limati: “Musasocheretsedwe. Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.” Choncho, makolo anzeru amathandiza ana awo kudziwa kuti kucheza ndi anthu olakwika, amene angawononge khalidwe lawo, n’koipa. Ndipo makolo otere amathandizanso ana awo kupeza anthu abwino ocheza nawo. (Miyambo 13:20) Mwina makolo angaitane anthu otere kunyumba kwawo kapena kupita nawo limodzi kokasangalala.

Kupanikizika. Makolo ambiri amafuna kuti ana awo azichita bwino, choncho nthawi zina amawakakamiza kuchita zinthu zimene zimapangitsa anawo kupanikizika. * Kodi mumadziwa zimene ana anu angathe kuchita ndi zimene sangathe? Kodi mumawauza zimene angadzachite pamoyo wawo ndiponso kuwathandiza kukwaniritsa zolinga zimenezo? Kodi mumapewa kunena zinthu zowayerekezera ndi ana ena? Dziwani kuti kuwayerekezera ndi ana ena kungawakhumudwitse kwambiri ndi kuwachititsa kuvutika maganizo. Ngati ana aona kuti makolo awo sakuwakonda, iwo amasakasaka anthu ena amene angawakonde. Makolo anzeru amathandiza banja lawo mwauzimu, mwina powerenga Baibulo limodzi ndi ana awo. Yesu Khristu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyo 5:3.

Kuwalekerera. Ana ena amayamba kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo chifukwa chakuti makolo awo amawalekerera. Lemba la Miyambo 29:15 limati: “Mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.” Ana amayamikira kwambiri mukamawaletsa kuchita zinthu zina ndipo mukamatero iwo amaona kuti mukuwakonda ndi kuwateteza, ngakhale kuti angamadandaule. N’chifukwa chake Baibulo limalimbikitsa makolo kulangiza ana awo komanso kuwasonyeza chitsanzo. (Aefeso 6:4) Baibulo limalimbikitsanso makolo kuti asamasinthesinthe mfundo zawo, chifukwa limati: “Mukati Inde akhaledi Inde ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Yakobe 5:12.

Komabe, mukadziwa kuti mwana wanu akugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, ndi bwino kudziwitsa dokotala. N’zovuta kusiya chizolowezi chogwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, choncho mungafunikire malangizo a dokotala kuti muthandize mwana wanu. Ndiponso ngati banja lanu ndi la Mboni za Yehova, mungapemphe thandizo kwa akulu a mumpingo wanu. (Yakobe 5:13-16) Akuluwo angakuthandizeni kupeza mfundo za m’Baibulo zomwe mungatsatire kuti vutoli lithe.

Nkhani yotsatira ikunena mfundo zina zothandiza ndiponso ikufotokoza za zinthu zabwino zimene tikuyembekeza m’tsogolo.

[Mawu a M’munsi]

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.”—Miyambo 20:5

[Bokosi patsamba 7]

ACHINYAMATA ANGAYAMBE MANKHWALA OZUNGUZA BONGO . . .

▪ Ngati munthu wina m’banja mwawo akugwiritsa ntchito mankhwalawa kapena ndi chidakwa

▪ Ngati amavutika maganizo kapena amadzikaikira

▪ Ngati akuona kuti sakondedwa ndi anzawo komanso anthu ena

▪ Ngati nthawi zambiri amatopa kapena amalephera kugona

▪ Ngati safuna kumvera anthu audindo *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Mfundozi n’zofalitsidwa ndi a Teen Help.