Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Zinachitikira Kuti?

1. Kodi thanthwe limene Mose anamenya kuti atulutsire Aisiraeli madzi linali kuti?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Numeri 20:1-8.

Lembani mzere wozungulira yankho lanu pamapupo.

Kadesi

Refidimu

Phiri la Sinai (Horebe)

▪ Kodi Mose ndi Aroni analakwitsa chiyani, ndipo analandira chilango chotani?

․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Numeri 20:9-13; Salmo 106:32, 33.

KAMBIRANANI:

Kodi mukuganiza kuti Mose anakwiyira Aisiraeli chifukwa chiyani? N’chifukwa chiyani muyenera kupewa kupsa mtima msanga?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 7 Kodi mayanjano oipa amawononga chiyani? 1 Akorinto 15:․․․

TSAMBA 8 Kodi osangalala ndi amene amazindikira chiyani? Mateyo 5:․․․

TSAMBA 13 Kodi moyo wathu uyenera kukhala wosakonda chiyani? Aheberi 13:․․․

TSAMBA 18 Kodi chikondi sichichita chiyani? 1 Akorinto 13:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Kodi Mumadziwa Chiyani za Aneneri?

Werengani Amosi 7:10-17, ndiyeno yankhani mafunso otsatirawa.

2. ․․․․․

Kodi wansembe Amaziya anadzudzula Amosi chifukwa chiyani?

3. ․․․․․

Kodi ndi makhalidwe awiri ati amene Amosi anasonyeza poyankha mawu achipongwe a Amaziya?

KAMBIRANANI:

Kodi mungaleke kunena za Yehova chifukwa chakuti ena akukunyozani? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

▪ Mayankho ali pa tsamba 11

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Kadesi.

▪ Mose analankhula mokalipa, ndipo iye ndi Aroni sanayeretse dzina la Yehova, choncho sanaloledwe kulowa Dziko Lolonjezedwa.

2. Anachitira mfumu chiwembu.

3. Kudzichepetsa ndiponso kulimba mtima.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Map: Based on maps copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel