Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Nthawi Moyenera?
Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Nthawi Moyenera?
“Ndinamva wina akunena kuti ngati munthu akufuna kuti ndikumane naye 4 koloko, ayenera kundiuza kuti ndikumane naye 3 koloko. Apa m’pamene ndinazindikira kuti ndiyenera kumasunga nthawi.”—Anatero Ricky. *
MUTAFUNA kuti akuwonjezereni maola ena patsiku, mungafune kuti akuwonjezereni angati? Kodi maola enawo mungawagwiritse ntchito yanji?
□ Kucheza ndi anzanga
□ Kugona
□ Kuwerenga
□ Kuchita masewera olimbitsa thupi
□ Kapena ․․․․․
Ngakhale kuti zingakhale zabwino atakuwonjezerani maola angapo patsiku, zimenezo sizingatheke. Ndiye kodi mungatani kuti muzikhala ndi nthawi yokwanira? Achinyamata ambiri aona kuti kugwiritsa bwino ntchito nthawi yawo kwawathandiza kukhala ndi nthawi yokwanira. Azindikiranso kuti kugwiritsa bwino ntchito nthawi yawo kwawathandiza kuti asamapanikizike, azikhoza bwino kusukulu ndiponso kuti makolo awo aziwadalira. Zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni inuyo kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.
Choyamba: Kupanga Ndandanda
Chimene chingakulepheretseni. Mwina mumaona kuti kupanga ndandanda ndi ntchito yaikulu. Mwinanso mumakonda kuchita zinthu mwachisawawa osati kutsatira ndandanda nthawi zonse.
Chifukwa chake muyenera kuyesetsa. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.” (Miyambo 21:5) Mosakayikira Solomo anali ndi zochita zambiri. Anali wokwatira, anali ndi ana ndiponso anali mfumu, ndipo ayenera kuti panthawiyi anali asanakwanitse zaka 20. Ndipo pamene amakula, zochita zinkamuchulukira kwambiri. Chimodzimodzinso inuyo, panopo muli ndi zochita zambiri, koma mukadzakula mwina zochitazo zidzakhala zambiri zedi. Choncho, ndi bwino kuti muyambiretu kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu panopo.
Zimene anzanu amanena. “Miyezi 6 yapitayo, ndinayamba kutsatira ndandanda yanga nthawi zonse. Ndandandayo inandithandiza kuti ndizichita zinthu mosavuta.”—Anatero Joey.
“Kukhala ndi ndandanda yochitira zinthu kwandithandiza kwambiri. Ndikakhala ndi zochita zina zambiri, ine ndi mayi anga timazilemba kaye ndipo timathandizana kupeza njira yozichitira.”—Anatero Mallory.
Zimene zingakuthandizeni. Taganizirani izi: Inuyo limodzi ndi anthu a m’banja mwanu muli
paulendo. Ndipo aliyense akungoponya mwachisawawa katundu wake m’galimoto. Ndiyeno malo atha m’galimotomo. Kodi pamenepa mungatani? Mungafunike kutsitsa zinthu zonse ndi kuyambanso kulongedza bwinobwino. Mungayambe kulongedza katundu mkulumkulu kaye ndipo ngati malo atatsala, mungakweze katundu mng’onomng’ono.N’chimodzimodzinso ndi moyo wanu. Mukayamba kuchita zinthu zosafunika kwambiri, mumasowa nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri. Yambani kuchita zinthu zofunika kaye, ndipo mukatero mudzakhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zina.—Afilipi 1:10.
Kodi ndi zinthu zofunika kwambiri ziti zimene muyenera kuchita?
․․․․․
Tsopano ganizirani zinthu zimene mukufuna kuchita, kuyambira ndi zofunika kwambiri. Mukayamba kuchita zinthu zofunika kwambiri mudzatsala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zina. Koma dziwani kuti ngati mutayambira zinazo, zinthu sizingakuyendereni bwino.
Zimene mungachite. Lembani ndandanda ya mmene mungachitire zinthu ndipo muziyenda nayo m’thumba. Mwina zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni.
□ Kalendala ya mu foni yam’manja
□ Dayale
□ Kalendala ya pakompyuta
□ Kalendala ya padesiki
Chachiwiri: Kutsatira Ndandanda
Chimene chingakulepheretseni. Mwina mukaweruka kusukulu mumafuna kupuma kapena kuonera TV kwa mphindi zingapo. Kapena mwina mumakonza zoti muwerenge koma mnzanu wina amakutumizirani uthenga kuti mukaonere filimu. Ndiye mungaone kuti nthawi ya filimuyo singasinthidwe koma inuyo mungasinthe nthawi n’kudzawerenga usiku. Mwinanso munganene mumtima mwanu kuti, ‘Ndimawerenga bwino ndikapanikizika.’
Chifukwa chake muyenera kuyesetsa. Mungamakhoze bwino kusukulu ngati mumawerenga musanatope. Ndiponso muli kale ndi zinthu zambiri zoti muchite, choncho si bwino kuwerenga usiku kwambiri chifukwa kuchita zimenezi n’kudzichulukitsira zochita. Mwinanso simukudziwa kuti m’mawa mwake mungadzuke bwanji. Mwina mungadzuke mochedwa, mungakhale wotopa, kapena mungachedwe kusukulu.—Miyambo 6:10, 11.
Zimene anzanu amanena. “Ndimakonda kuonera TV, kuimba gitala ndiponso kucheza ndi anzanga. Kuchita zinthu zimenezi si kulakwa, koma nthawi zina zimandilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri ndipo kenako ndimachita zinthu mothamanga.”—Anatero Julian.
Zimene zingakuthandizeni. Musamangochita zinthu zimene muyenera kuchita basi, muzichitanso zinthu zimene mumazikonda. Julian anati: “Sizivuta kuchita zinthu zimene ndifunika
kuchita ndikadziwa kuti ndikatha zimenezo pali zochita zina zimene ndimakonda.”Zinanso zokuthandizani: Muzikhala ndi chinachake chomwe mukufuna kukwaniritsa, kenako muzichita zinthu zina zing’onozing’ono zokuthandizani kukwaniritsa cholingacho. Joey wazaka 16, yemwe tamutchula poyamba uja, anati: “Ndikufuna kuti ndidzakhale mphunzitsi wa Baibulo. Panopa ndimayesetsa kutsatira ndandanda yanga podziwa kuti m’tsogolo ndizidzakhala ndi zochita zambiri.”
Zimene mungachite. Kodi ndi zinthu ziti zimene mukufuna mutakwaniritsa pa miyezi 6 ikubwerayi? (Tchulani chimodzi kapena ziwiri)
․․․․․
Kodi n’chiyani chimene mukufuna kukwaniritsa pa zaka ziwiri zikubwerazi, ndipo kodi ndi zinthu ziti zimene mukufunika kuchita panopa kuti zimenezi zitheke?
․․․․․
Chachitatu: Kuchita Zinthu Mwaukhondo Ndiponso Mwadongosolo
Chimene chingakulepheretseni. Mwina simudziwa kuti kuchita zinthu mwaukhondo ndiponso mwadongosolo kungakuthandizeni kusunga nthawi. Ndiponso kuika zinthu mwachisawawa n’kosavuta. Mukhoza kumati mudzakonza m’chipinda chanu tsiku lina. Kapenanso zimenezo sizikukhudzani n’komwe.
Chifukwa chake muyenera kuyesetsa. Kuika zinthu mwaukhondo ndiponso mwadongosolo kungakuthandizeni kuti musamataye nthawi pofufuza zinthu zimene zasowa. Zimenezi zingakuthandizeninso kukhala ndi mtendere wa mumtima.—1 Akorinto 14:40.
Zimene anzanu amanena. “Nthawi zina ndikangoika zovala zanga paliponse, ndimavutika kuti ndipeze msanga zinthu zimene ndikufuna.”—Anatero Mandy.
“Kachikwama kanga kandalama kanasowa kwa mlungu umodzi. Zimenezi zinandisokoneza kwambiri maganizo. Kenako nditakonza m’chipinda changa, ndinakapeza.”—Anatero Frank.
Zimene zingakuthandizeni. Muziyesetsa kuika zinthu m’malo mwake mwamsanga mukangotha kuzigwiritsa ntchito. Kuchita zimenezi nthawi zonse kungakuthandizeni kuti musamatenge nthawi yaitali mukukonza m’chipinda chanu komanso kuti zisamakuvuteni kupeza zimene mukufuna.
Zimene mungachite. Muziyesetsa kukhala aukhondo nthawi zonse. Muziika zinthu zonse mwadongosolo, ndipo mudzaona kuti zimenezi n’zothandiza kwambiri.
Yambani pang’onopang’ono, ndipo yambani lero lomwe. Kodi ndi mfundo ziti za m’nkhani ino zimene zakuthandizani kwambiri?
․․․․․
Ndiyesa kuchita izi kwa milungu ․․․․․ kuti ndione ngati zingandithandize.
Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Maina m’nkhaniyi tawasintha.
ZOTI MUGANIZIRE
▪ Kodi mumafunika kugona maola angati kuti mudzuke muli ndi mphamvu?
▪ Kodi mungapemphe ndani kuti akuthandizeni kulemba ndandanda?
▪ Ngati mumagwiritsa kale ntchito ndandanda, kodi mungafunike kuisintha pena ndi pena?
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 20, 21]
Pamlungu umodzi, achinyamata a zaka 8 mpaka 18 amakhala maola:
17
ali ndi makolo awo
30
ali kusukulu
44
akuonera TV, kuchita masewera a pakompyuta, kutumizirana mauthenga ndi kumvetsera nyimbo
KODI NTHAWI YANGA IMATHERA KUTI?
Onkhetsani maola amene mumawononga pa mlungu
kuonera TV: ․․․․․
kuchita masewera a pakompyuta: ․․․․․
kugwiritsa ntchito kompyuta: ․․․․․
kumvetsera nyimbo: ․․․․․
Maola onse pamodzi: ․․․․․
Maola amene ndingathe kuwagwiritsa ntchito kuchita zinthu zofunika kwambiri, m’malo mochita zinthu zosafunika kwenikweni ndi awa: ․․․․․
[Chithunzi patsamba 20]
Mukayamba kulongedza katundu mng’onomng’ono, katundu mkulumkulu angasowe malo