Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muziyendetsa Bwino Galimoto?

Kodi Mungatani Kuti Muziyendetsa Bwino Galimoto?

Kodi Mungatani Kuti Muziyendetsa Bwino Galimoto?

ANTHU ambiri masiku ano amaona kuti kuyendetsa galimoto n’kofunika. Ngakhale zili choncho, pamsewu pakuchitika ngozi zambiri. Ofufuza apeza kuti padziko lonse anthu opitirira 1,200,000 amafa pangozi zapamsewu chaka chilichonse. Choncho, m’pofunika kuti tiphunzire kuyendetsa bwino galimoto. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene zingatithandize.

Zidziweni Bwino

Magazini ina ya ku Australia inanena kuti, chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene woyendetsa galimoto angachite kuti apewe ngozi ndi kuyendetsa mosamala. Choncho asananyamuke, munthu woyendetsa galimoto ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndadzuka bwino moti ndingathe kuyendetsa galimoto?’ Kutopa kungachititse munthu kuti aziganiza mochedwa poyendetsa galimoto. (Australian Journal of Social Issues) Ofesi yoona za maulendo a pamsewu ku Philippines inanena kuti kukwiya, nkhawa, ndi kusangalala kwambiri zingachititse munthu kuti asayendetse bwino galimoto.

Kudwala ndiponso kuledzera zingachititsenso kuti munthu asamayendetse bwino galimoto. Mwachitsanzo, ngati munthu ali ndi matenda aakulu kapena anavulala angalephere kuyendetsa bwino. Munthu amene amaona kuti moyo wa anthu ena ndi wofunika, sangayendetse galimoto ataledzera. Mankhwala ena amachititsanso kuti munthu asayendetse bwino galimoto. Choncho, ngati munthu wamwa mowa kapena mankhwala enaake, sayenera kuyendetsa galimoto, koma ngati akufuna kuyendabe ulendowo, angapemphe munthu wina kuti ayendetse.

Muziyesetsa Kuyendetsa Bwino

Chiwerengero cha magalimoto chikuchuluka m’mayiko ambiri, ndipo zimenezi zikuchititsa kuti chiwerengero cha oyendetsa galimoto atsopano chichulukenso. Choncho woyendetsa galimoto angachite bwino kuganizira mfundo ziwiri zotsatirazi kuti apewe ngozi.

Muziyendetsa mosamala Musamagone, muziyesetsa kuona zinthu zimene zingakuchititseni ngozi, kutsogolo ndi kumbuyo kwa galimoto yanu. Ndiponso muzionetsetsa zimene oyendetsa galimoto ena akuchita. Ngozi zambiri zimachitikanso chifukwa choyendetsa moyandikana kwambiri ndi magalimoto ena. Woyendetsa galimoto wosamala amasiya mpata wokwanira pakati pa galimoto yake ndi magalimoto ena.

Dziwani zinthu zimene zingachititse ngozi. Muzitulutsa mutu kuti muone zonse zimene zikuchitika pafupi ndi galimoto yanu, ndipo musamangodalira magalasi a m’mbali. Pewani kuchita zinthu zina pamene mukuyendetsa galimoto monga kulankhula pafoni, kuika nyimbo ndi zinthu zina zomwe zingakusokonezeni.

Kwa oyendetsa njinga yamoto: Akuluakulu ena oona za maulendo a pamsewu amanena kuti ngati galimoto ndi njinga yamoto zitayenda ulendo wofanana, woyendetsa njinga yamoto atha kupanga ngozi maulendo 37, pamene wa pagalimoto akhoza kuchita ngozi kamodzi kokha. Kodi mungatani kuti mudziteteze? Mfundo ziwiri zimene tazifotokoza zija zingathandizenso woyendetsa njinga yamoto. Koma kuwonjezera pa mfundo zimenezi, bungwe loona za maulendo a pamsewu ku United States linanena kuti anthu oyendetsa njinga za moto “azioneka akakhala pamsewu.” Muzionetsetsa kuti anthu ena akukuonani. Nthawi zonse nyali zanu zizikhala zoyaka. Musamayende malo oti oyendetsa galimoto sangakuoneni. “Muzivala zokutetezani.” Muzivala zipewa za njinga yamoto ndiponso malaya owala. “Muziyesetsa kupewa ngozi.” Musamachite zinthu zolakwika poganizira kuti oyendetsa galimoto ena akukuonani.

Onetsetsani Kuti Galimoto Yanu Ili Bwino

Muyeneranso kuonetsetsa kuti zinthu zonse pagalimoto yanu zili bwino. Mabuleki ndiponso zinthu zina ziyenera kugwira bwino ntchito. Matayala asakhale akutha kuti galimoto isamaterereke poima ndipo ayenera kukhala ndi mpweya wokwanira kuti galimoto isamakuvuteni kuyendetsa kapena kuimitsa. Magalimoto ambiri masiku ano ali ndi malamba. ndipo malamba amenewa sangakuthandizeni ngati simukuwagwiritsa ntchito.

Muziyendetsa galimoto mogwirizana ndi mmene msewu ulili chifukwa msewu ukanyowa galimoto imachedwa kuima komanso imavuta kuwongolera. Mukamayendetsa usiku, muzionetsetsa kuti nyali zakutsogolo zikugwira bwino ntchito ndipo simuyenera kuthamangitsa kwambiri. Popeza kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, tiziyesetsa kuyendetsa bwino galimoto.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 13]

KODI MUNGATANI KUTI MUSAMAWONONGE MAFUTA AMBIRI?

Musamasinthesinthe liwiro: Kusinthasintha liwiro kumatha mafuta.

Muzithimitsa galimoto mukaima: Magalimoto ambiri masiku ano sachita kufunikira kutenthetsa injini musanayambe kuyendetsa. Ngati mukuona kuti muimitsa galimoto kwa masekondi opitirira 30, ithimitseni.

Matayala azikhala ndi mpweya wokwanira: Matayala amene apopedwa bwino amayenda mosavuta ndipo zimenezi zimachititsa kuti galimoto isamathe mafuta.

Musamathamangitse kwambiri: Kuthamanga kwambiri kungachititse ngozi ndiponso kumawonongetsa mafuta ambiri.

[Chithunzi patsamba 11]

❏ Musamagone

❏ Muzimanga lamba

❏ Pewani kuchita zinthu zambiri nthawi imodzi

❏ Pewani zinthu zina zimene zingakusokonezeni

[Chithunzi patsamba 12]

❏ Muziona zinthu zimene zili pafupi ndi galimoto yanu

❏ Onetsetsani kuti mabuleki ali bwino

❏ Matayala azikhala ndi mpweya wokwanira

❏ Matayala asakhale akutha

❏ Musamayandikire kwambiri galimoto ina

[Chithunzi patsamba 13]

❏ “Valani zokutetezani”

❏ “Muzioneka”

[Chithunzi patsamba 13]

❏ Onetsetsani kuti nyali zakutsogolo zikugwira bwino ntchito