Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kusintha Chipembedzo Chanu N’kulakwa?

Kodi Kusintha Chipembedzo Chanu N’kulakwa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kusintha Chipembedzo Chanu N’kulakwa?

Avtar atayamba kuphunzira Baibulo, abale ake omwe ndi a chipembedzo cha Chisiki anakhumudwa kwambiri. Iye anati: “M’dziko lathu munthu akasintha chipembedzo, anthu amamusala. Ngakhale maina athu ndi achipembedzo. Munthu akasintha chipembedzo chake amamutenga kuti wasochera komanso amamuona kuti wanyoza abale ake.”

PATAPITA nthawi Avtar anakhala wa Mboni za Yehova. Kodi iye analakwitsa? Abale ake ankaganiza choncho, ndipo mwina inunso mungaganize choncho. Mungaganize kuti simuyenera kusintha chipembedzo chanu chifukwa anthu onse a mtundu wanu ndiponso chikhalidwe chanu ali m’chipembedzo chimenecho.

Kulemekeza abale anu n’kofunika. Baibulo limati: “Tamvera atate wako anakubala.” (Miyambo 23:22) Koma chinthu chofunika kwambiri ndi kudziwa Mlengi wathu ndiponso zolinga zake. (Yesaya 55:6) Kodi zimenezi n’zotheka? Ngati n’zotheka, kodi kudziwa Mlengi n’kofunika bwanji kwa inuyo?

Kufufuza Choonadi

Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa zinthu zosiyana. Ndipo n’zosatheka kuti zipembedzo zonsezo zikhale zolondola. Choncho, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, pali anthu ambiri “okangalika potumikira Mulungu; koma mosam’dziwa molondola.” (Aroma 10:2) Komabe, palemba la 1 Timoteyo 2:4, mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu amafuna kuti ‘anthu, kaya akhale a mtundu wotani, adziwe choonadi molondola.’ Kodi choonadi chimenechi mungachipeze bwanji?

Kuphunzira Baibulo kungatithandize kupeza choonadi. Paulo, yemwe anauziridwa kulemba Baibulo, anati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Pamene mukufufuza choonadi, fufuzaninso umboni wosonyeza kuti Baibulo ndi lolondola. Mukafufuza mudzapeza kuti nzeru zimene zimapezeka m’Baibulo n’zosayerekezereka, ndi lolondola pa nkhani za mbiri yakale, komanso ulosi wake supita pachabe.

Baibulo silinena kuti zipembedzo zonse n’zovomerezeka kwa Mulungu, ndipo limatichenjeza kuti tisamangokhulupirira chilichonse chimene tikumva. Limatilimbikitsa kuti ‘tiziyesa mawu ouziridwa kuti tione ngati ali ochokera kwa Mulungu.’ (1 Yohane 4:1) Mawu alionse ochokera kwa Mulungu ayenera kugwirizana ndi makhalidwe ake, kuphatikizapo khalidwe lake lalikulu lomwe ndi chikondi.—1 Yohane 4:8.

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amafuna kuti ‘tim’pezedi.’ (Machitidwe 17:26, 27) Popeza kuti Mlengi wathu amafuna kuti tifufuze choonadi, sikungakhale kulakwa kusintha chipembedzo chathu ngati tapeza choonadicho. Nanga bwanji ngati kuchita zimenezi kungatidanitse ndi abale athu?

Muziganizira Kaye Zimene Abale Anu Akunena

Nthawi zambiri munthu akasintha chipembedzo chake, amasiyanso kuchita miyambo ya chipembedzo chakalecho. Zimenezi zimachititsa kuti abale ake asamagwirizane naye. Yesu ankadziwa mfundo imeneyi. Iye nauza otsatira ake kuti: “Ndinabwera kudzagawanitsa, munthu kutsutsana ndi bambo wake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi wake, ndipo mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake.” (Mateyo 10:35) Kodi pamenepa Yesu amatanthauza kuti mfundo za m’Baibulo zimadanitsa anthu? Ayi. Iye anangonena zimene zingachitike ngati munthu wasiya chipembedzo chake ndipo achibale ake sakusangalala ndi zimenezi.

Kodi zingatheke kupeweratu kusiyana maganizo ndi achibale? N’zoona kuti Baibulo limaphunzitsa kuti ana azimvera makolo awo ndiponso akazi azigonjera amuna awo. (Aefeso 5:22; 6:1) Komabe, limalangizanso anthu amene amakonda Mulungu kuti ‘azimvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’ (Machitidwe 5:29) Choncho, chifukwa chofuna kumvera Mulungu, nthawi zina mungachite zinthu zimene sizingasangalatse achibale anu.

Ngakhale kuti Baibulo limasiyanitsa momveka bwino chipembedzo choona ndi chonyenga, Mulungu sakakamiza munthu aliyense kuti atsatire chipembedzo chinachake. (Deuteronomo 30:19, 20) Munthu aliyense sayenera kukakamizidwa kulambira Mulungu m’njira imene akuona kuti si yabwino kapena kuuzidwa kuti asankhe pakati pa chipembedzo ndi achibale. Kodi kuphunzira Baibulo kumachititsa kuti banja lithe? Ayi. Baibulo limalimbikitsa kuti mkazi ndi mwamuna amene ali m’zipembedzo zosiyana, asalekane.—1 Akorinto 7:12, 13.

Kuthetsa Mantha

Mwina inunso mungaope kuti achibale anu sasangalala akamva kuti mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mariamma anati: “Abale anga ankandidera nkhawa kuti sindipeza mwamuna woyenerera woti ndimange naye banja. Choncho, anayamba kundiletsa kuphunzira Baibulo.” Mariamma anakhulupirira kwambiri Yehova Mulungu ndipo anapitirizabe kuphunzira. (Salmo 37:3, 4) Inunso mungachite zomwezo. M’malo mochita mantha, muziganizira phindu lake. Uthenga wa m’Baibulo umathandiza kusintha khalidwe. Anthu amene akuphunzira Baibulo amakonda kwambiri banja lawo. Ndiponso amasiya makhalidwe oipa monga ndewu, kumwetsa mowa, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo. (2 Akorinto 7:1) Baibulo limalimbikitsa makhalidwe abwino monga, kukhulupirika, kuona mtima, ndiponso kulimbikira kugwira ntchito. (Miyambo 31:10-31; Aefeso 4:24, 28) Mukapitiriza kuphunzira Baibulo, mudzaona kuti maphunziro amenewa ndi opindulitsa kwambiri.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ N’chifukwa chiyani muyenera kuunikanso chipembedzo chanu?—Miyambo 23:23; 1 Timoteyo 2:3, 4.

▪ Kodi mungadziwe bwanji chipembedzo choona?—2 Timoteyo 3:16; 1 Yohane 4:1.

▪ Kodi muyenera kusiya kuphunzira Baibulo chifukwa chakuti achibale anu sakugwirizana nazo?—Machitidwe 5:29.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Uthenga wa m’Baibulo umathandiza kusintha khalidwe

[Chithunzi patsamba 29]

Mariamma ndi mwamuna wake