Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

▪ Nsomba imene anaipeza pansi pa nyanja ya Atlantic, akuti “yakhala ndi moyo wautali kwambiri kuposa nyama zina zonse.” Asayansi ataifufuza bwinobwino, anaona kuti nsombayi inakhala ndi moyo zaka 405.—SUNDAY TIMES, BRITAIN.

▪ “M’dziko mukakhala mavuto a zachuma, ngakhale anthu amene ali ndi mabiliyoni ambiri a ndalama amakhudzidwa. Anthu amenewa afunikira kuthandizidwa kuti asasokonezeke kwambiri maganizo.—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.

TV Imalimbikitsa Chiwerewere

Nkhani ina imene inafalitsidwa m’magazini a Pediatrics, inati: “Pali umboni wosonyeza kuti achinyamata amene amaonera zachiwerewere pa TV, amayambanso kuchita zachiwerewere. Kafukufuku wina anasonyeza kuti atsikana amene amakonda kuonera mapulogalamu oterewa, “amatenga mimba ndipo chiwerengero chawo chimakhala chachikulu kuwirikiza kawiri chiwerengero cha atsikana amene saonera mapulogalamuwa.” Mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa achinyamata kuganiza kuti kuchita zachiwerewere kulibe vuto lililonse. Izi zili choncho chifukwa mapulogalamu amenewa saonetsa achinyamata atatenga mimba kapena matenda opatsirana. Koma pali zinthu zinanso zimene zimalimbikitsa achinyamata kuchita chiwerewere. Ofufuza akuti magazini, Intaneti, ndiponso nyimbo zimalimbikitsanso achinyamata kuchita zachiwerewere.

Anthu Odwala Khate Akuchuluka

Anthu pafupifupi 3,000 ku United States akudwala matenda a khate. Chaka chilichonse anthu pafupifupi 150, amapezeka ndi matendawa. Ambiri amene akudwala matendawa ndi anthu ochokera m’mayiko ena. Komabe, bungwe la zaumoyo la ku America linanena kuti nthambi yoona za matendawa ku Louisiana, “imathandiza chaka chilichonse anthu pafupifupi 30 odwala matendawa ndipo ambiri amakhala kuti anabadwira ku America komweko ndipo sanapiteko dziko lina lililonse komwe anthu amadwala khate.” Ofufuza za matendawa sanadziwebe chimene chimachititsa kuti matendawa afale. Munthu amatha kuchira akapita mwachangu kuchipatala. Koma akachedwa, matendawa amalowerera ndipo amawononga maselo a m’thupi moti sangachirenso.

Anthu Akuba Zipangizo Zanyukiliya

Mkulu wa bungwe loona za zipangizo zanyukiliya, dzina lake Mohamed El Baradei, anati: “Zigawenga zikuba kwambiri zipangizo zanyukiliya ndipo zimenezi zikutidetsa nkhawa. Akuti zipangizo zokwana 250 zinabedwa kumayambiriro kwa chaka cha 2008. Choopsa n’chakuti zipangizo zambiri zikabedwa sizimapezekanso.” Chimene chikuchititsa kuti chiwerengero cha zipangizo zobedwa chiwonjezereke sichikudziwika. Koma mwina chiwerengerochi chikukwera chifukwa mayiko akumanena zipangizo zawo zikasowa, komanso chifukwa chakuti anthu ambiri akuzifuna zipangizozi.

Akatswiri Anapeza Zolemba Zakale ku Israel

Akatswiri ofukula zinthu zakale a ku Israel anapeza phale lomwe linalembedwa kale kwambiri zaka 1,000 mipukutu ya m’Nyanja Yakufa isanalembedwe. Phaleli lili ndi mizere isanu yolembedwa ndi inki ndipo analipeza ku Khirbet Qeiyafa, m’dziko la Israeli. Akatswiriwa akuganiza kuti phaleli linalembedwa m’zaka za m’ma 900 B.C.E. Akatswiri a ku Hebrew University of Jerusalem ananena kuti zimene zinalembedwa pa phaleli sizikudziwika bwinobwino, koma zikuoneka kuti panalembedwa zinthu zokhudzana ndi malamulo zimene zinalembedwa ndi munthu wodziwa za ulembi ndipo pali mawu akuti ‘woweruza,’ ‘kapolo,’ ndi ‘mfumu.’

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Gabi Laron/Institute of Archaeology/Hebrew University © Yosef Garfinkel