Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndakhala Wokhulupirika kwa Mulungu kwa Zaka Zoposa 70

Ndakhala Wokhulupirika kwa Mulungu kwa Zaka Zoposa 70

Ndakhala Wokhulupirika kwa Mulungu kwa Zaka Zoposa 70

Yosimbidwa ndi Josephine Elias

“Usadandaule, kaya andipha kapena andimasula ndipitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Yehova.” Amenewa ndi mawu amene mwamuna wanga anandinong’oneza ali m’ndende. Nanenso ndinatsimikiza mtima kuti ndipitirizabe kukhala wokhulupirika. Ndipo ndakhalabe wokhulupirika mpaka pano.

NDINABADWA m’chaka cha 1916, m’tawuni yaing’ono ya Sukabumi yomwe ili kumapiri a ku West Java, m’dziko la Indonesia. Makolo anga anali ochokera ku China ndipo anali olemera. Anali ndi nyumba yaikulu ndiponso antchito ambiri. M’banja mwathu tinalimo ana 6, ndipo ine ndinali wachinayi kubadwa. Mwana wamkazi ndinalipo ndekha, ndipo chifukwa cha zimenezi ndinkachita zinthu ngati mnyamata. Ndinkakwera padenga ndiponso ndinkakonda masewera omwe anyamata amakonda kuchita. Koma panali nkhani inayake imene inkandidetsa nkhawa kwambiri.

Aphunzitsi anga ankanena kuti atsikana osamvera adzakapsa kumoto. Ndipo chifukwa chakuti ineyo ndinali wosamvera, ndinkaopa kwambiri. Nditapita kusukulu yasekondale ku Jakarta (mzinda womwe poyamba unkatchedwa kuti Batavia), ndinadwala kwambiri. Dokotala amene ankandisamalira ankaganiza kuti sindichira, choncho mayi amene anali eniake a nyumba yomwe ndinkakhala anandiuza kuti ndisadandaule chifukwa ndikafa ndipita kumwamba. Koma ndinkaopa chifukwa ndinkaona kuti ndikafa ndipita kumoto.

Mayi anga, dzina lawo Kang Nio, ndiponso mchimwene wanga wamkulu, dzina lake Dodo, anabwera mwamsanga ku Jakarta kudzanditenga. Tili m’njira, Dodo anandifunsa kuti, “Kodi umadziwa kuti Baibulo silinena kuti anthu adzakapsa kumoto?”

Ineyo ndinamufunsa kuti: “Ukudziwa bwanji zimenezi?” Mayi anga anandiwerengera malemba a m’Baibulo onena kuti anthu akufa sadziwa kanthu ndipo akuyembekezera kudzaukitsidwa. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 5:28, 29) Mayi ndiponso mchimwene wangayo anandiuza kuti anaphunzira zimenezi kwa Mboni za Yehova. Kenako anandipatsa kabuku kakuti Kodi Akufa Ali Kuti? ndipo ndinayamba kukawerenga nthawi yomweyo. * Ndisanafike n’komwe kunyumba ndinanena kuti: “Ichi ndiye choonadi.”

Ndinayamba Ntchito Yolalikira

Panthawi yomwe ndimadwalayi, banja lathu linali litasamukira ku Bandung, tawuni yaikulu ku West Java. Patapita nthawi ndinachira. Kenako m’March 1937, munthu wina wa Mboni za Yehova wa ku Australia dzina lake Clem Deschamp, yemwe ankakhala ku Jakarta, anabwera m’dera lakwathu. Panthawiyi, ineyo, mayi anga, achimwene anga aakulu atatu, Felix, Dodo ndi Peng, tinabatizidwa. M’kupita kwa nthawi, achimwene anga aang’ono, Hartanto ndi Jusak, komanso bambo anga a Tan Gim Hok anakhalanso Mboni. *

Titangobatizidwa, tinachita nawo ntchito yapadera yolalikira kwa masiku 9 pamodzi ndi M’bale Deschamp. Iye anatiphunzitsa mmene tingalalikirire pogwiritsa ntchito timakadi tomwe tinkakhala ndi uthenga wa m’Baibulo m’zinenero zitatu. Nthawi zinanso tinkalalikira achibale ndi anzathu. Pasanapite nthawi yaitali, ku Bandung kunakhazikitsidwa mpingo, womwe unali wachiwiri kukhazikitsidwa ku Indonesia.

Chakumapeto kwa chaka cha 1937, banja lathu linasamukira ku Jakarta n’cholinga choti tikalalikire anthu ochokera ku China omwe analipo 80,000 mumzindawu. Ineyo, Felix ndi mayi anga tinavomerezedwa kuti tikhale apainiya, kapena kuti alaliki anthawi zonse. Ndinkalalikira ku Bandung, Surabaya ndi madera ena. Nthawi zambiri ndinkapita ndekha kolalikira. Panthawiyi ndinali wachitsikana, wamphamvu, ndipo ndinkasangalala kutumikira Mulungu. Koma pasanapite nthawi yaitali nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba.

Tinavutika Kwambiri Panthawi ya Nkhondo

Mu December 1941, mayiko a ku Asia anayamba kumenya nawo nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Panthawiyi dziko la Japan linalanda dziko la Indonesia. Mabuku athu onena za m’Baibulo analetsedwa ndipo sitinkaloledwa kulalikira. Ndikamapita kolalikira ndinkanyamula zipangizo zosewerera tchesi n’cholinga choti anthu aziganiza kuti ndikukasewera tchesi.

Mu 1943, ndinakwatiwa ndi André. Iye anali mlaliki wanthawi zonse wolimba mtima. André anali ndi mawu amphamvu moti akamalankhula aliyense ankamvetsera. Iye ndi ine tinkalowetsa mozemba mabuku onena za m’Baibulo ku Java kuti Mboni za Yehova zinzathu m’madera osiyanasiyana ziziwerenga. Tikanagwidwa, chilango chake chikanakhala kuzunzidwa ndi kuphedwa. Ndipo panali nthawi zambiri pamene tinatsala pang’ono kugwidwa.

Mwachitsanzo, tsiku lina tikukwera sitima ku Sukabumi, ine ndi André tinaimitsidwa ndi apolisi oopsa kwambiri a ku Japan, omwe ankadziwika kuti Kempeitai. M’chikwama changa munali mabuku onena za m’Baibulo. Mmodzi wa apolisiwo anandifunsa kuti: “M’chikwama chakochi muli chiyani?”

André anamuyankha kuti: “Zovala.”

Wapolisiyu anafunsanso kuti: “Nanga pansi pa zovalazo pali chiyani?”

André anayankha kuti: “Zovala zinanso.”

Iye anafunsanso kuti: “Pansi penipeni pa chikwama chako pali chiyani?” Ndinayamba kuchita mantha kwambiri ndipo ndinapemphera chamumtima kwa Yehova. André anamuyankha kuti: “Bwanji mufufuze nokha?”

Wapolisi mnzake anapisa dzanja m’chikwama changacho. Kenako analira mokuwa, n’kutulutsa dzanja lakelo mwamsangamsanga. Iye anali atabayidwa ndi singano moti anachita manyazi kwambiri. Nthawi yomweyo iye anatilamula kuti titseke chikwamacho n’kukakwera sitima.

Panthawi inanso tikupita ku Sukabumi, apolisi a Kempeitai anandizindikira kuti ndine wa Mboni za Yehova ndipo anandilamula kuti ndikawonekere ku likulu lawo. André komanso mchimwene wanga Felix anandiperekeza. André ndi amene anayamba kufunsidwa mafunso. Apolisiwo anamufunsa mafunso ambirimbiri nthawi imodzi. Ena mwa mafunsowo anali akuti: “Mboni za Yehova ndi ndani? Kodi cholinga cha ntchito yanu ndi kulimbana ndi boma la Japan? Kodi ndiwe kazitape?”

André anayankha kuti: “Ndife atumiki a Mulungu Wamphamvuyonse, ndipo palibe chimene talakwa.” Mkulu wa apolisi pamalowa anatenga lupanga n’kulikweza m’mwamba.

Mokwiya, iye ananena kuti: “Bwanji ndikuphe?” André anaweramitsa mutu wake patebulo la mkulu wa apolisiyo n’kuyamba kupemphera chamumtima. Patapita nthawi, apolisiwo anayamba kuseka. Mkulu wa apolisiyo anamuuza André kuti: “Ndiwe wolimba mtima.” Kenako analamula André kuti atuluke ndipo anaitana ineyo ndi Felix kuti tilowe. Zimene tinanena zinagwirizana ndendende ndi zimene André ananena. Choncho, mkulu wa apolisiyo ananena mokuwa kuti: “Basi, chokani muzipita! Ndatsimikiza kuti sindinu akazitape.”

Ine, André ndi Felix tinabwerera kunyumba, ndipo tinathokoza kwambiri Yehova. Koma sitinadziwe kuti tikumana ndi mavuto aakulu kuposa amenewa m’tsogolo.

Mavuto Anawonjezereka

Patapita miyezi ingapo, “abale onyenga” anapereka André m’manja mwa apolisi a Kempeitai. (2 Akorinto 11:26) Apolisiwa atamutsekera m’ndende, ndinkapita kukamuona. Iye anawonda kwambiri ndipo anali wofooka. Zakudya zimene ankadya ankachita kutoleza m’ngalande zakundendeko. Koma apolisiwo analephera kumusiyitsa chikhulupiriro chake. Monga mmene ndafotokozera koyambirira kuja, André anandinong’oneza kuti: “Usadandaule, kaya andipha kapena andimasula ndipitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Ndilolera kufa m’malo mosiya kukhala wokhulupirika.”

Atatha miyezi 6 m’ndende, André anakaonekera mu khoti lalikulu la ku Jakarta. M’khotimo munadzaza anthu a m’banja lathu ndiponso anzathu. Aliyense sankadziwa kuti chichitike ndi chiyani.

Woweruza anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukukana kulowa usilikali?”

André anayankha kuti: “Ndine msilikali wa Ufumu wa Mulungu. Ndipo n’zosatheka kuti ndikhale msilikali wa maufumu awiri, Ufumu wa Mulungu ndi ufumu wa Japan.”

Woweruzayo anamufunsanso kuti: “Kodi umaletsa ena kulowa usilikali?”

André anayankha kuti: “Ayi. Iwonso ali ndi ufulu wosankha.”

André anapitiriza kufotokoza za chikhulupiriro chake, ndipo ankatchula mfundo za m’Baibulo zosonyeza kuti n’kulakwa kulowa usilikali. Woweruzayo, yemwe anali wachisilamu, anachita chidwi kwambiri ndi zimene André anafotokoza, ndipo ananena kuti: “Chikhulupiriro chako ndi changa n’chosiyana, koma sindingakukakamize kuti uchite zinthu zotsutsana ndi chikumbumtima chako. Panopa ndikulamula kuti ulibe mlandu.”

Mitima yathu inakhala pansi, ndipo ine ndinasangalala kwambiri. André anabwera kwa ine n’kundigwira dzanja. Achibale ndiponso anzathu anatizungulira ndipo anatiuza kuti akusangalala kuti André watuluka m’ndende.

Tinapitiriza Kulalikira

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, ku Indonesia kunayamba zipolowe, zomwe zinachitika zaka zinayi. Anthu a kumeneko anatopa ndi ulamuliro wa dziko la Netherlands. Pazipolowezo, anthu ambiri anaphedwa ndipo m’midzi yambiri anthu anathawa m’nyumba zawo. Anthu amene ankafuna kuti zinthu zisinthe ankatikakamiza kuti tizikuwa kuti: “Merdeka!” kutanthauza kuti “Ufulu!” Koma tinkawauza kuti sitilowerera zandale.

Ngakhale kuti kunali zipolowe, tinayambanso kulalikira nyumba ndi nyumba. Tinkagwiritsa ntchito khadi lolalikirira ndi mabuku amene tinasunga nkhondo isanayambe. M’mwezi wa May, 1948, ine ndi André tinayambiranso kugwira ntchito ya upainiya. Panthawiyi zipolowe zinali zitachepa. Kupatulapo ineyo ndi mwamuna wanga, panalibenso apainiya ena ku Indonesia. Patatha zaka zitatu, ku Jakarta kunabwera amishonale 14 omwe anamaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo ku New York m’dziko la United States. Iwo anatiphunzitsa zinthu zochuluka zomwe zinatithandiza kwambiri pa utumiki wathu.

Mu June 1952, ine ndi mwamuna wanga André tinauzidwa kuti tikhale apainiya apadera. Ndipo tinauzidwa kuti tizikalalikira ku Semarang, ku chigawo chapakati cha Java. Chaka chotsatira tinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi, ndipo kalasi yathu inali ya nambala 22. Titamaliza maphunziro athu tinabwerera kuti Indonesia ndipo tinauzidwa kuti tizikalalikira m’tawuni yotchedwa Kupang, ku Timor. Kenako tinatumizidwa kuti tizikalalikira ku South Sulawesi ndi ku North Sulawesi. Kumeneku tinakumananso ndi mavuto ena ambiri.

Ntchito Yathu Inaletsedwanso

Mu 1965 anthu ena ankafuna kulanda boma, ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri aphedwe. Atsogoleri ena achipembedzo analowerera ndipo ankauza boma kuti Mboni za Yehova ndi anthu oukira. Koma akuluakulu a boma sankakhulupirira mabodza amenewa. Komabe, atsogoleri achipembedzowo anapitirizabe kuuza boma kuti Mboni za Yehova ndi anthu oopsa. Choncho pa December 25, 1976, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa.

Atangolengeza zimenezi, mkulu wina woimira boma pamilandu anaitana André kuti apite ku ofesi yake. Atapita anamufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti ntchito ya Mboni za Yehova yaletsedwa?”

André anayankha kuti: “Inde ndikudziwa.”

Mkuluyo anafunsanso kuti: “Kodi panopa usintha chipembedzo chako?”

André anawerama pang’ono ndi kudzimenya pamtima. Kenako ananena mwamphamvu kuti: “Mungathe kucheka mtima wanga, koma simungathe kundisintha chipembedzo.”

Modabwa, mkuluyu anati: “Ndiye ndilembe chiyani?”

André anamuuza kuti: “Mulembe kuti ndidakali wa Mboni za Yehova ndipo palibe chimene ndalakwa.”

Mkuluyu anati: “Ngati zili choncho, tipita kunyumba kwanu kukalanda mabuku ako onse.”

Koma usiku womwewo, anyamata ena a Mboni za Yehova anapita kunyumba kwathu n’kukachotsa mabuku onse, ndipo anangosiya mabokosi opanda kanthu. Tinapitiriza kulalikira pogwiritsa ntchito Baibulo. Ndipo mkulu uja sanativutitsenso.

Ndikusangalala ndi Zimene Ndachita Pamoyo Wanga

M’kupita kwa nthawi, ine ndi André tinayamba kulalikira ku Surabaya, pachilumba cha Java ndi pachilumba cha Bangka, chomwe chili kum’mwera chakum’mawa kwa chilumba cha Sumatra. Koma mu 1982, tinabwerera ku Jakarta chifukwa tinkadwaladwala. M’chaka cha 2000, André anamwalira ali ndi zaka 85, ndipo panthawiyi anali akuchitabe upainiya. M’chaka chotsatira ntchito ya Mboni za Yehova inaloledwanso.

Ndimasangalala kwambiri ndi zimene ndachita pamoyo wanga. Panopa ndili ndi zaka 93, ndipo ndatha zaka zoposa 70 ndikugwira ntchito yolalikira. Panthawi yomwe ndimabatizidwa mu 1937, ku Indonesia kunali Mboni za Yehova 25 zokha. Koma panopa ziliko pafupifupi 22,000. Ndimasangalala kwambiri kuti ndathandiza nawo kuti Mboni za Yehova zichuluke chonchi. Koma ichi n’chiyambi chabe. Ndikufuna kutumikira Mulungu mokhulupirika kwamuyaya.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kabukuka kankafalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma anasiya kukafalitsa.

^ ndime 9 Banja lawo lonse linakhalabe lokhulupirika kwa Yehova. Panopa Josephine ndi Jusak ndi omwe ali ndi moyo ndipo akupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika ku Jakarta.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Ndine msilikali wa Ufumu wa Mulungu. Ndipo n’zosatheka kuti ndikhale msilikali wa maufumu awiri, Ufumu wa Mulungu ndi ufumu wa Japan”

[Mawu Otsindika patsamba 14]

“Mungathe kucheka mtima wanga, koma simungathe kundisintha chipembedzo”

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Malo amene ine ndi mwamuna wanga takhala ndiponso kulalikira

INDONESIA

Sulawesi

Manado

Sumatra

Bangka

Java

JAKARTA

Sukabumi

Bandung

Semarang

Surabaya

Timor

Kupang

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi André cha m’ma 1970

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi zaka 15 ndinawerenga kabuku kakuti “Kodi Akufa Ali Kuti?” ndipo ndinatsimikiza kuti ndapeza choonadi