Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipangizo Zamakono N’zothandizadi?

Kodi Zipangizo Zamakono N’zothandizadi?

Kodi Zipangizo Zamakono N’zothandizadi?

Galimoto yasiya msewu n’kuwomba mtengo wamagetsi, ndipo munthu wina amene anali m’galimotoyo wavulala kwambiri. Nthawi yomweyo woyendetsa galimotoyo akuimbira foni anthu ena kuti adzamuthandize. Koma kodi n’chiyani chimene chachititsa ngoziyo? Ngoziyo yachitika chifukwa chakuti woyendetsa galimotoyo amayankha foni.

CHITSANZOCHI chikusonyeza kuti zipangizo zamakono zili ndi ubwino komanso kuipa kwake. Zimangodalira mmene tikuzigwiritsira ntchito. Ndipotu ndi anthu ochepa amene angakonde kumagwiritsabe ntchito zinthu zimene zinkagwiritsidwa ntchito kalekale. Mwachitsanzo, makompyuta amatipeputsira ntchito ndipo titha kugula zinthu kapena kusungitsa ndalama kubanki tili kunyumba kwathu, ndiponso amatithandiza kucheza ndi anzathu akutali.

Kale anthu apabanja akachoka pakhomo m’mamawa sankalankhulananso mpaka madzulo. Koma nyuzipepala ya USA Today inanena kuti masiku ano “anthu apabanja 70 pa 100 alionse omwe ali ndi mafoni am’manja amaimbirana tsiku lililonse kuti angofunsa kuti mnzawo ali bwanji. Ndipo anthu apabanja 64 pa 100 alionse amaimbirana kuti auzane zochita, pamene makolo 42 pa 100 alionse amaimbira ana awo tsiku lililonse.”

Tiyenera Kuzigwiritsa Ntchito Mwanzeru

Kodi kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kuli ndi vuto lililonse? Ganizirani chitsanzo cha mwamuna ndi mkazi wina ku Ulaya amene anali atangokwatirana kumene. Malinga ndi zimene nyuzipepala ina inanena, iwo “ankangokhalira kulankhula pa foni, kaya ali pagalimoto kapena akuchita masewera olimbitsa thupi. Ankaimbirananso ngakhale onse ali m’nyumba imodzi.” Nthawi zina ankatha mphindi 4,000, zomwe ndi maola oposa 66, pamwezi akulankhula pa foni, ndipo ankanena kuti sangathe kukhala popanda foni. Dokotala wina, dzina lake Harris Stratyner, ananena kuti anthuwa “amasonyeza zizindikiro zoti sangakhale opanda foni. Ndipo ngakhale banja lawo limayendetsedwa ndi foni.”

Mwina mungaone kuti banja limeneli linkachita zinthu mowonjeza, koma zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri akugwiritsa ntchito mafoni monyanyira. Anthu ambiri amaona kuti sangathe kukhala popanda foni ngakhale kwa ola limodzi lokha. Mtsikana wina wazaka za m’ma 20 anati: “Nthawi zonse timafunika kuona ngati wina watitumizira uthenga, timafuna kufufuza zinthu pa Intaneti kapena kutumiza uthenga kwa anzathu.”

Malinga ndi nyuzipepala ina, Dr Brian Yeo ananena kuti ngati foni ndiponso Intaneti “zimakuwonongerani nthawi yambiri moti mumalephera kuchita zinthu zina, ndiye kuti pali vuto.” (The Business Times of Singapore) Komanso nthawi zambiri anthu amene amangokhalira kugwiritsa ntchito foni kapena Intaneti sachita masewera olimbitsa thupi, ndipo akhoza kudwala matenda a mtima, a shuga kapena matenda ena oopsa.

Mavuto ena amaonekera nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, kafukufuku wina waposachedwapa anasonyeza kuti anthu amene amalankhula pa foni yam’manja akuyendetsa galimoto, amafanana ndi munthu amene akuyendetsa galimoto ataledzera. Kulemba uthenga mukuyendetsa galimoto n’koopsanso kwambiri, koma kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu 40 pa 100 aliwonse azaka zapakati pa 16 ndi 27 amalemba uthenga kwinaku akuyendetsa galimoto. Ngati mukuyendetsa galimoto kwinaku mukulankhula kapena kulemba uthenga pa foni, dziwani kuti ngati mutachita ngozi, apolisi ndiponso a kampani ya inshuwalansi adzafufuza foni yanuyo kuti aone ngati mumaigwiritsa ntchito mukuyendetsa galimoto. Ndipo ngati atapeza kuti mumalankhula pa foni kapena kulemba uthenga, mungakhale pamavuto aakulu. * Mwachitsanzo, m’chaka cha 2008 sitima ina itachita ngozi n’kupha anthu 25 ku California, U.S.A., ofufuza anapeza kuti woyendetsa sitimayo ankatumiza uthenga pa foni akuyendetsa, zomwe zinachititsa kuti alephere kumanga mabuleki.

Popeza kuti ana ambiri masiku ano akugwiritsa ntchito mafoni am’manja ndiponso kompyuta ndi zipangizo zina zamakono, ayenera kuphunzitsidwa mmene angazigwiritsire ntchito mwanzeru. Kodi mungawathandize bwanji? Werengani nkhani yotsatirayi kuti mudziwe mmene mungawathandizire.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Anthu amene amamvera zimene Baibulo limaphunzitsa ayenera kupewa kuchita chilichonse chimene chingachititse ngozi.—Genesis 9:5, 6; Aroma 13:1.

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi foni ndi Intaneti zimakuwonongerani nthawi yambiri?