Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumapanikizika ndi Ntchito?

Kodi Mumapanikizika ndi Ntchito?

Kodi Mumapanikizika ndi Ntchito?

ANTHU ambiri padziko lonse amapanikizika ndi ntchito ndipo sakhala ndi nthawi yocheza ndi banja lawo. Lipoti lina linati, ‘kugwirizana kwa mayiko pa ntchito zamalonda, zipangizo zamakono, ndiponso kugwira ntchito usiku ndi usana, zapangitsa kuti anthu asamapezeke pakhomo.’ Zinthu zimenezi zachititsa kuti anthu alemere kwambiri koma zabweretsanso mavuto. Munthu wina wolemba mabuku anati: “Ambiri timagwira ntchito mopitirira malire ndiponso timakhala ndi zochita zambiri. Zimenezi zimachititsa kuti tizitopa komanso tizipanikizika kwambiri.”

Kuwonjezera pamenepa, palinso mavuto amene abwera chifukwa cha kusayenda bwino kwa chuma padziko lonse. Anthu ambiri, ogwira ntchito zapamwamba kapena ntchito wamba, achotsedwa ntchito ndipo akusowa pokhala chifukwa sangathe kulipira nyumba. Ndipo mwina iwo amaganiza kuti akanati azilimbikira ntchito kwambiri si bwenzi atachotsedwa.

Kodi mavuto amenewa ndi aakulu bwanji?

▶ Ku Ulaya, anthu 6 pa anthu 10 alionse amadwala chifukwa chopanikizika ndi ntchito.

▶ Ku America, munthu mmodzi pa anthu atatu alionse amaona kuti akugwira ntchito mopitirira malire.

▶ Ku Canada, anthu awiri pa anthu atatu alionse sakhala ndi nthawi yocheza ndi banja lawo chifukwa chotanganidwa ndi ntchito.

▶ Akuti anthu oposa 600 miliyoni, omwe ndi 22 peresenti ya anthu onse ogwira ntchito padziko lonse, amagwira ntchito maola oposa 48 pa mlungu.

Malipoti amenewa akusonyeza kuti zinthu sizili bwino. Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu amene amagwira ntchito maola ambiri sakhala ndi thanzi labwino, sagwirizana ndi anzawo, salera bwino ana awo ndiponso banja lawo siliyenda bwino.

Kodi inunso mumapanikizika ndi ntchito? Kapena kodi muli m’gulu la anthu ambirimbiri amene sali pantchito? Kodi mumafuna mutamakhala ndi mpata wocheza ndi banja lanu? Ngati ndi choncho, kodi mukudziwa zimene mungachite?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 3]

AMAFIKIRANSO PA NTCHITO INA

Mayi wina wapantchito anati: “Ndikaweruka kuntchito, ndimafikiranso pa ntchito ina monga kuphika chakudya chamadzulo, kukonza m’nyumba, kuchapa zovala, kukatenga ana kusukulu kapena kosewera, kuwathandiza homuweki, kuonetsetsa kuti asamba komanso akagona nthawi yabwino. Pomaliza zimenezi, ndimakhala nditatopa kwambiri.” Padziko lonse pali amayi apantchito pafupifupi 1.2 biliyoni ndipo ambiri mwa amenewa, mofanana ndi amuna ambiri, amagwira ntchito ziwiri. Amayiwa akaweruka kuntchito n’kubwerera kunyumba amakafikiranso pa ntchito zina zotopetsa. Ndipo kafukufuku akusonyeza kuti amuna ambiri amazemba ntchito zapakhomo. Nthawi zambiri amayi ndi amene amagwira ntchito yonse ya pakhomo.