Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Anthu a ku Amereka amaona kuti Mulungu amene Akhristu amamulambira ndi wamoyo, kungoti iwo amaona kuti Mulungu alibenso mphamvu pa ndale komanso chikhalidwe ngati mmene zinalili m’mbuyo monsemu.”—NEWSWEEK, U.S.A.

“Kusayenda bwino kwa chuma padziko lonse kwabweretsa mavuto atsopano: Mabanja ena akulephera kusudzulana. Chifukwa cha mavuto amene alipowa, anthu ambiri akuona kuti sangawononge ndalama zambiri ngati atapanda kuthetsa ukwati wawo ngakhale atakhala kuti sakugwirizana.”—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.

Mayi mmodzi pa amayi atatu alionse amene anafunsidwa pa kafukufuku wina ku Germany, ananena kuti amaphunzira zinthu kwa mwana wawo wamkazi. Iwo akuti amaphunzira zinthu monga mafashoni a zovala, anthu oyenera kucheza nawo, kusakwiya msanga, komanso kukhala munthu wodzidalira.—BERLINER MORGENPOST, GERMANY.

Adakali ndi Chitetezo Champhamvu

Nyuzipepala ina inati: “Ngakhale kuti papita zaka 90 kuchokera pamene nthenda ya chimfine choopsa cha ku Spain inatha, m’magazi mwa anthu amene anapulumuka atadwala matendawa mwapezeka kuti mudakali chitetezo champhamvu cholimbana ndi tizilombo timene tinkayambitsa matendawa mu 1918. Ndipo zimenezi zikusonyeza kuti thupi la munthu limakhala ndi chitetezo champhamvu kwambiri.” (International Herald Tribune) Atapima magazi a anthu okalamba amene anapulumuka ku matendawa, asayansi anapeza kuti “m’thupi mwawo mudakali chitetezo champhamvu ndipo n’chokonzeka kulimbana ndi matendawa.” Pogwiritsa ntchito chitetezo chimenechi, akatswiri ofufuza za mankhwala anapanga katemera wamphamvu amene anachiza makoswe omwe anali ndi matenda a chimfine chamtunduwu. Akatswiri ofufuza anadabwa kwambiri ndi kukhalitsa kwa chitetezo cha m’thupi kumeneku. Katswiri wina anati: “Ambuye anatipatsa chitetezo cha m’thupi chimene chingatithandize pa moyo wathu wonse. Ndipo matenda akalephera kutipha amangotithandiza kukhala olimba.”

Zimene Anthu Amafuna Kumufunsa Mulungu

“Ngati muli wabwino, n’chifukwa chiyani mukungoyang’anira anthu akuvutika?” Nyuzipepala ya Dagen ku Sweden inanena kuti limeneli ndi limodzi mwa mafunso amene ophunzira a ku koleji m’dzikolo amalakalaka atafunsa Mulungu. Kafukufuku wina anasonyeza kuti mafunso ena amene anthu ambiri amakhala nawo ndi monga: “Kodi cholinga cha moyo ndi chiyani?” ndiponso “Kodi chimachitika ndi chiyani munthu akamwalira?” Dziko la Sweden limadziwika kuti ndi dziko limene anthu ake sakonda zachipembedzo. Ngakhale zili choncho, malinga ndi zimene woimira bungwe la achinyamata achikhristu amene anachita kafukufukuyu ananena, “anthu akumeneko amakhala ndi mafunso amenewa ndipo achinyamata amavutika maganizo ndi mafunso a mtunduwu.”

Anthu Olumala Angathe Kukhala ndi Banja Losangalala

Akatswiri ofufuza ananena kuti, “amuna ndi akazi amisinkhu yosiyanasiyana amanena kuti atalumala, anayamba kusangalala kwambiri m’banja mwawo.” Kulephera kuchita zinthu zimene kale munkachita n’kopweteka, komabe kungathandize kuti mwamuna ndi mkazi azigwirizana. Kafukufukuyu anasonyeza kuti makamaka amuna okalamba ndi amene amakhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi akazi awo. Karen Roberto, yemwe ndi mkulu wa dipatimenti yofufuza zimene zimachitika munthu akamakalamba, pa koleji ya Virginia Tech., ku U.S.A., anati: “Mkazi akavulala kapena akapuwala, mwamuna amakhala ndi udindo wowonjezereka womusamalira ndipo zimenezi zimawapatsa mwayi wambiri wocheza. M’kupita kwa nthawi amayamba kukondana kwambiri.”