Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulimi wa Maluwa Umafuna Khama

Ulimi wa Maluwa Umafuna Khama

Ulimi wa Maluwa Umafuna Khama

KULIMA maluwa n’kosangalatsa. Ndipo pali mtundu winawake wa maluwa umene anthu ambiri amakonda kulima wotchedwa orchid. Anthu ena amene amakonda kwambiri maluwa amenewa amayesetsa kuphunzira mayina ake a Chilatini n’cholinga choti adziwatchula molondola. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amachita chidwi ndi maluwawa?

Maluwa amenewa alipo a mitundu yosiyanasiyana. Mitundu yoposa 25,000 imapezeka m’tchire ndipo mabungwe ena amati pali mitundu inanso yoposa 100,000 imene anthu anapanga okha. Zimenezi sizikutanthauza kuti anapanga okha kuchokera kudothi, madzi ndi mpweya ayi. Koma amawapanga potenga mungu wa maluwa ena n’kukauika pa maluwa ena.

Maluwa achilengedwe komanso opangidwa ndi anthu amakhala aakulu mosiyanasiyana. Maluwa ena amakhala aang’ono kwambiri moti amaoneka bwino pogwiritsa ntchito magalasi oonera zinthu zing’onozing’ono, ndipo maluwa ena amakhala aakulu. Mwachitsanzo maluwa ena a mtunduwu amene amamera m’nkhalango za ku Indonesia, amatha kulemera makilogalamu oposa 500.

Maluwawa amakhala a mitundu komanso maonekedwe osiyanasiyana. Ena amaoneka ngati njuchi, ena gulugufe, enanso ngati mbalame. Ndipo ena maonekedwe awo ndi ovuta kuwayerekezera ndi chinthu china chilichonse koma nawonso ndi ochititsa chidwi kwambiri. Kwa zaka zambiri, anthu olemera okha ndi amene ankatha kupeza maluwa amenewa, koma masiku ano anthu osauka nawonso amatha kukhala nawo. Tiyeni tikambirane zambiri zokhudza maluwa okongolawa.

Alimi Anayamba Kuchita Chidwi ndi Ulimiwu

Anthu akhala akuchita chidwi ndi maluwa amenewa kwa zaka zambiri, koma posachedwapa ndi pamene alimi apeza njira zabwino zowachulukitsira. Duwa loyamba lopangidwa ndi anthu linakhwima mu chaka cha 1856. Komabe, kusamalira maluwa okongola amenewa kumafuna khama ndipo nthawi zambiri kumakhala kotopetsa.

Njere za maluwa amenewa zimakhala zazing’ono kwambiri moti zina zimangooneka ngati fumbi. Kusamalira njere zazing’ono chonchi kuti zikule n’kovuta kwambiri. Kwa zaka zambiri, alimi akhala akuyesa njira zosiyanasiyana zaulimi n’cholinga choti apeze njira komanso nyengo yabwino yobzalira maluwawa. Mu 1922, Dr. Lewis Knudson, yemwe ndi katswiri wa sayansi payunivesite ya Cornell ku United States, anatulukira kuti njerezi zimakula bwino akaziika m’madzi a shuga komanso okhala ndi madzi enaake omwe amatengedwa m’zomera zapansi pa nyanja. Pasanapite nthawi anthu achidwi anayamba kupanga mitundu yambiri yatsopano. Alimi ambiri anayamba kuchita chidwi ndi ulimi wa maluwawa moti mitundu yambiri yatsopano inkatulukiridwa chaka ndi chaka.

Koma zimenezi zisanayambe, maluwa amenewa ankamera m’tchire. Kodi mitundu yatsopano imayamba bwanji m’tchiremo?

Mmene Mitundu Yatsopano Imayambira M’tchire

Ngati mitundu iwiri yosasiyana kwambiri ya maluwa amenewa yamera moyandikana, pakhoza kubadwa mtundu wina watsopano. Tizilombo touluka tikamafunafuna madzi a m’maluwawa, mungu umakakamira ku matupi awo ndipo tizilomboti tikatera pamaluwa ena, munguwo umagwerapo. Zikatere, maluwa amene pagwera munguwo amakhwima n’kuyamba kubereka tizitheba timene timakhala ndi njere.

M’kupita kwa nthawi, tizithebato tikakhwima timasweka ndipo njere zake zimagwera pansi. Njerezi zimakhalapo zambirimbiri ndipo zina zimaulutsidwa ndi mphepo. Nthawi zambiri njere zomwe zamera sizikula bwino ndipo ndi zochepa zimene zimafika pokhwima. Ngati mungu wauluka kuchoka pa maluwa a mtundu wina n’kupita pa wina, mtundu watsopano umabadwa. Koma anthunso amatha kupanga mtundu watsopano wa maluwa. Kodi amapanga bwanji?

Kupanga Maluwa Atsopano

Kuti apange mtundu watsopano, mlimi amatenga mungu wa maluwa amodzi n’kukauika pa mtundu wina ndipo maluwa atsopanowo amatengera maonekedwe a mitundu yonse iwiri. Choncho, mlimi asanasankhe maluwa amene akufuna kugwiritsa ntchito, amayamba waganizira kaye mtundu wa maluwa amene akufuna kupanga. Mwachitsanzo, iye angafune kupanga maluwa amene adzakhale ndi mtundu winawake, mizere kapena madontho. Iye angafune kuti mtundu umene apangewo udzakhale ndi masamba akuluakulu kapena ang’onoang’ono. Komanso mwina angafune kuti maluwawo adzakhale ndi kafungo kenakake. Poganizira zimenezi, iye angasankhe maluwa oyenerera amene angathandize kuti mtundu watsopanowo udzakhale ndi zonse zimene akufuna. Mwachitsanzo, ngati mlimi akufuna maluwa ooneka a golide, iye angasankhe maluwa enaake a masamba ooneka agolide amene anatulukiridwa koyamba ku China mu 1979. Maluwa atsopano opangidwa kuchokera ku maluwa amenewa, amaoneka agolide ndiponso okongola kwambiri.

Mlimi akasankha mitundu iwiri imene akufuna kugwiritsa ntchito, amachotsa mungu wonse m’maluwa amene akufuna kuikamo mungu wina. Kenako amaika munguwo mkati mwenimweni mwa maluwa pogwiritsa ntchito kamtengo kakang’ono kapena kachipangizo kena. Akatero amalembapo deti ndiponso maina a maluwa awiri onsewa.

Pamafunika Kudekha

Mungu uja ukayamba kugwira ntchito, pamachitika zinthu zodabwitsa. Timachubu tokhala ngati mizu timamera kuchokera pa tsinde la duwa n’kukafika pamene pamakhala dzira la duwa. Kenako dziralo limafufuma n’kupanga kathumba. M’kati mwa kathumba kameneka, tinjere tambirimbiri timakhala tikupangika ndipo kanjere kalikonse kamakhala kolumikizana ndi kachubu kamene kamakhala ndi mungu. Zimatenga miyezi ingapo, chaka kapena kupitirira kuti tinjereto tikhwime. Panthawi imeneyi, mlimi amachotsa tinjereto n’kutiika m’botolo mmene mumakhala madzi amankhwala. Tinjereto tikamera, timakhala tokongola kwambiri ndipo timaoneka tobiriwira bwino ngati kapinga.

Pakangopita miyezi yochepa chabe, mlimiyo amachotsa mbewuzo m’botolomo n’kuziika mu chimphika chachikulu cha maluwa. Akatero, maso ake amakhala pa mbewuzo ndipo amazithirira pafupipafupi kuti zisaume. Pakapita nthawi, mlimiyo amawoka mbewu iliyonse payokha m’miphika ing’onoing’ono ya maluwa. Apa m’pamene pamafunika kudekha chifukwa pangapite zaka zambiri, mwina zoposa 10, kuti maluwawo ayambe kumasula.

Tangoganizirani mmene mlimiyo amasangalalira akaona maluwawo akumasula. Ngati mtundu umenewo ndi watsopano, mlimiyo amaupatsa dzina lililonse limene iye akufuna. Maluwa alionse amene angadzapangidwe ofanana ndi amenewa amawatchulanso dzina lomweli.

Nthawi zina mlimi amapanga maluwa atsopano abwino kwambiri omwe anthu okonda maluwa amachita nawo chidwi. Mlimiyo amatha kulandira mphoto, ndipo maluwa akewo amagulitsidwa modula kwambiri. Ngakhale kuti mlimi amasangalala akapeza ndalama zambiri, iye amasangalala kwambiri akaona maluwa opanga yekha akumasula.

Tsopano mwadziwa kuti pamafunika khama komanso kudekha kuti mlimi apange maluwa okongola kwambiri. Koma kunena zoona, ntchito imene mlimi amagwira kuti apange maluwa atsopano ndi yochepa poyerekeza ndi ntchito imene Mlengi wa zinthu zonse, Yehova, anachita. Iye ndi amene anaika zinthu zonse zofunika m’maluwa zomwe zimathandiza kuti mlimi apange maluwa atsopano. Anthufe tikaona mitundu yosiyanasiyana ya maluwa amenewa, timasangalala kwambiri ndipo timazindikira kuti iye analenga zimenezi chifukwa chotikonda. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene wamasalimo Davide ananena kuti: “Nchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Salmo 104:24.

[Chithunzi patsamba 17]

Maluwa apepo

[Chithunzi patsamba 17]

Maluwa achikasu

[Chithunzi patsamba 18]

Maluwa akhofi