Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Mulungu?

Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Mulungu?

Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Mulungu?

KODI mumadabwa chifukwa chake zinthu zonse za m’chilengedwe, kaya za padzikoli kapena zakumwamba, zimatsatira malamulo? Kodi mumachita chidwi mukaganiza za zamoyo zosiyanasiyana za padziko lapansi zomwe zinapangidwa modabwitsa? Anthu ambiri amanena kuti zinthu za m’chilengedwe zinangokhalapo mwangozi kapena zinachita kusanduka. Koma ena amanena kuti kuli Mlengi amene anapanga zinthu zonsezi. Kodi inuyo mukuona kuti maganizo omveka pamenepa ndi ati?

Maganizo awiri onsewa amafuna chikhulupiriro. Kuti munthu anene kuti kuli Mulungu amafunika kukhala ndi chikhulupiriro chifukwa Baibulo limanena kuti, “palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:18) Kuti munthu anenenso kuti zinthu zinakhalapo mwangozi kapena kusanduka amafunika kukhala ndi chikhulupiriro chifukwa palibe munthu anaonapo zinthu za m’chilengedwe zikupangika zokha. Palibenso munthu amene anaona zamoyo zikusanduka. Mwachitsanzo, nyani akusanduka n’kukhala munthu. Mafupa a zinyama amene akatswiri amafukula amasonyeza kuti mitundu ya nyama sinasinthe. * Choncho, funso lofunika kwambiri ndi lakuti: Kodi ndani amakhulupirira zolondola? Kodi ndi amene amati zinthu zinachita kusanduka, kapena amene amati zinachita kulengedwa?

Kodi Muli ndi Umboni Weniweni Wotsimikizira Zimene Mumakhulupirira?

Baibulo limanena kuti “chikhulupiriro” chenicheni chimakhala ndi “umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheberi 11:1) N’zosakayikitsa kuti mumakhulupirira zinthu zambiri zimene simunazionepo.

Mwachitsanzo, akatswiri ambiri otchuka a mbiri yakale amakhulupirira kuti Alexander Wamkulu, Julius Caesar ndiponso Yesu Khristu anakhalapo. Kodi zimene akatswiriwa amakhulupirira ndi zolondola? Inde, chifukwa pali umboni wotsimikizira kuti anthu amenewa anakhalapodi.

Asayansinso amakhulupirira zinthu zosaoneka chifukwa chakuti amakhala ndi “umboni wooneka” wosonyeza kuti zinthuzo zilipodi. Mwachitsanzo, wasayansi wina wa ku Russia wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Dmitry Mendeleyev, anali ndi chidwi kwambiri ndi zinthu za m’chilengedwe monga mpweya, miyala ndi zitsulo zosiyanasiyana. Iye anapeza kuti zinthuzi sizisiyana kwenikweni ndipo zitha kuikidwa m’magulu potengera kulemera kwawo komanso mmene zinapangidwira. Popeza kuti iye anali ndi chikhulupiriro chakuti zinthuzi zinayalana mwatsatanetsatane komanso mwadongosolo potengera magulu awo, anazindikira kuti pali zinthu zina zimene sizinapezedwe. Ndipo m’kupita kwa nthawi, zina mwa zinthuzi zinapezedwa ndipo zinaikidwa m’magulu awo.

Akatswiri ofufuza zinthu zakale amadziwa mmene anthu ankakhalira kale akakumba zinthu zakalekale zimene zinakwiririka pansi pa nthaka. Tayerekezerani kuti katswiri wina wafukula miyala yambirimbiri yosemedwa bwino komanso yofanana kukula kwake, yomwe inamangidwa bwinobwino. Kodi katswiriyo angati bwanji? Kodi angaganize kuti miyalayo inangokhalapo mwangozi? Ayi. M’malomwake iye angadziwe kuti pamalowo panali anthu amene anasema komanso kumanga miyala imeneyi. Ndipotu ndi zomveka kukhulupirira zimenezi.

Kodi si zomvekanso kukhulupirira kuti pali winawake amene anapanga zinthu zodabwitsa zam’chilengedwe? Anthu ambiri, kuphatikizapo asayansi otchuka kwambiri, amaona kuti pali Mlengi amene anapanga zinthu zonsezi.

Kodi Zinakhalapo Mwangozi Kapena Zinachita Kulengedwa?

Zaka zambiri m’mbuyomu, wasayansi wina wa ku Britain, dzina lake Sir James Jeans, analemba kuti chifukwa cha kupita patsogolo kwa sayansi, “tayamba kuona kuti chilengedwe chinapangidwa ndi winawake woganiza bwino osati makina.” Iye ananenanso kuti “chilengedwechi chimaoneka kuti chinapangidwa ndi winawake wodziwa kwambiri masamu” ndipo “amene anachipangayo ayenera kuti ali ndi nzeru ngati anthufe.”

Kuchokera pamene Jeans analemba zimenezi, asayansi ena akhala akunenanso mawu amenewa. Mwachitsanzo, Paul Davies analemba kuti: “Chilengedwe chinapangidwa mwadongosolo kwambiri ndipo zimenezi zachititsa akatswiri ambiri a zinthu zakuthambo kukhulupirira kuti pali winawake amene anachipanga.” Nayenso Albert Einstein, yemwe ndi wasayansi wotchuka kwambiri, analemba kuti: “N’zodabwitsa kwambiri kuti anthufe timatha kumvetsa zinthu zosiyanasiyana zimene zili m’chilengedwechi.” Mwachitsanzo, anthu ambiri amagoma ndi DNA ndiponso ubongo wa munthu.

DNA Ndiponso Ubongo wa Munthu

DNA ndi tinthu timene timakhala mu selo tomwe timachititsa kuti mwana azioneka wofanana ndi makolo ake. * Tinthu timeneti tili ngati pulani ya mmene nyumba idzaonekere. Mu DNA mumakhala malangizo amene amakhudza mmene thupi lathu limagwirira ntchito. Kodi mu DNA mumakhala malangizo ochuluka bwanji? Buku lina limanena kuti ngati malangizo amene amakhala mu DNA atalembedwa m’buku, “bukulo likhoza kukhala ndi masamba opitirira 1 miliyoni.”

Mu zamoyo zambiri, DNA imakhala mu tinthu tooneka ngati ulusi, tomwe timasungidwa mosamala mkatikati mwa selo iliyonse. Malo amene tinthu timeneti timasungidwamo amakhala aang’ono kwambiri. Tangoganizirani: Malangizo onse amene anachititsa kuti inuyo muzioneka wosiyana ndi anthu ena, anaikidwa m’tinthu tating’ono kwambiri tomwe simungathe kutiona. Mogwirizana ndi zimene wasayansi wina ananena, DNA “imasunga malangizo ambiri kuposa amene angasungidwe ndi chipangizo chilichonse.” N’zochititsa chidwi kwambiri kuti malangizo amene amasungidwa mu DNA ndi ochuluka kwambiri kuposa amene amasungidwa mu kompyuta kapena m’zipangizo zina. Ndipotu pali zinthu zambiri zimene sitikudziwa n’komwe zokhudza DNA. Magazini ina inanena kuti: “Nthawi zonse asayansi amatulukira zinthu zatsopano zosonyeza kuti DNA ndi yodabwitsa.” *New Scientist.

Kodi n’zomveka kunena kuti zinthu zodabwitsa monga DNA zinangokhalako mwangozi? Tiyerekeze kuti mukuyenda ndiye mwapeza buku lalikulu la masamba 1 miliyoni ndiponso lolembedwa bwino kwambiri, kodi mungaganize kuti bukulo linadzilemba lokha? Nanga bwanji bukulo litakhala laling’ono kwambiri moti simungathe kuliwerenga popanda kugwiritsa ntchito magalasi oonera zinthu zing’onozing’ono kwambiri? Bwanjinso ngati bukulo lili ndi malangizo olembedwa bwino okhudza mmene makinawo angadzikonzere okha akawonongeka kapena kupanga tizipangizo tatsopano timene tingalowe m’malo mwa tizipangizo timene tawonongeka? Kunena zoona n’zosamveka kunena kuti buku lotereli lingakhalepo lokha popanda winawake wolilemba.

Atafufuza zinthu zatsopano zokhudza mmene maselo amagwirira ntchito zomwe asayansi atulukira posachedwapa, Antony Flew, yemwe poyamba ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu, anati: “M’thupi mumachitika zinthu zodabwitsa kwambiri zomwe zimapangitsa kuti anthu akhale ndi moyo ndipo zimenezi ndi umboni wakuti pali wina wake wanzeru amene analenga zinthu zonsezi.” Flew ananena kuti mfundo imeneyi apitiriza kuifufuza kukafika kulikonse kumene ingamufikitse. Mfundoyi inamufikitsa pokhulupirira kuti kuli Mulungu.

Ubongo wa munthu umadabwitsanso asayansi ambiri. Asayansi amati ubongo ndi “chinthu chovuta kumvetsa kwambiri m’chilengedwe chonse.” Ubongo wa munthu, womwe umalemera pafupifupi kilogalamu imodzi yokha, umachita zinthu zambiri komanso zodabwitsa kuposa kompyuta yapamwamba kwambiri. Katswiri wina wa ubongo ananena kuti pamene asayansi akutulukira zambiri zokhudza ubongo, “m’pamenenso amazindikira kuti ndi wodabwitsa kwambiri ndiponso pali zambiri zimene sakuzidziwa.”

Taganizirani izi: Ubongo umachititsa kuti tizitha kupuma, kuseka, kulira, kuganiza, kupanga kompyuta, kuyendetsa njinga, kulemba ndakatulo ndiponso kuti tizitha kuchita chidwi ndi zinthu zakuthambo. Ndiye kodi n’zomveka kukhulupirira kuti ubongo unangokhalapo mwangozi?

Zimene Muyenera Kukhulupirira

Kuti timvetse mmene moyo wathu unayambira, kodi tiyenera kuchita kuyang’ana anyani ndi nyama zina monga mmene asayansi ena amachitira? Kapena kodi tiyenera kuyang’ana kwa Mulungu kuti atithandize kudziwa zolondola? N’zoona kuti pali zinthu zina zomwe anthufe timafanana ndi nyama. Mwachitsanzo, tonse timadya, kugona ndiponso kubereka. Komabe, ndife osiyana ndi nyama pa zinthu zambiri. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti makhalidwe ena tinawatengera kwa munthu wapamwamba kwambiri, yemwe ndi Mulungu. Baibulo limanena mfundo imeneyi momveka bwino kuti Mulungu analenga anthu “m’chifanizo chake.” (Genesis 1:27) Mungachite bwino kuganizira makhalidwe a Mulungu monga amene amapezeka pa Deuteronomo 32:4; Yakobe 3:17, 18; ndi 1 Yohane 4:7, 8.

Mlengi wathu anatipatsa “nzeru” zomwe zimatithandiza kumvetsa zinthu za m’chilengedwe komanso kupeza mayankho omveka a mafunso athu. (1 Yohane 5:20) Pankhani imeneyi, wasayansi yemwe analandirapo mphoto ya Nobel, dzina lake William D. Phillips, analemba kuti: “Ndikaganizira mozama za kupangidwa bwino kwa zinthu za m’chilengedwe, kukongola kwake komanso mfundo yakuti anthufe timatha kuzimvetsa zinthu zimenezi, sindikaikira kuti pali winawake wanzeru kwambiri amene anapanga zinthu zimenezi. Sayansi yandithandiza kuzindikira kuti zinthu za m’chilengedwe zinapangidwa mwadongosolo komanso zimatsatira malamulo, ndipo zimenezi zimandipangitsa kukhulupirira kwambiri kuti kuli Mulungu.”

Zaka 2,000 zapitazo, munthu wina yemwe ankachita chidwi ndi zinthu za m’chilengedwe analemba kuti: “Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Mtumwi Paulo ndi amene analemba mawu amenewa. Iye anali munthu wanzeru ndiponso wophunzira, ndipo ankadziwa kwambiri Chilamulo cha Mose. Paulo ankakhulupirira kuti kuli Mulungu pazifukwa zomveka ndipo chifukwa chakuti anali munthu wokonda chilungamo, ankalemekeza Mulungu poona zimene analenga.

Tikukhulupirira kuti inunso muona kuti pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti kuli Mulungu. Ndipo, mofanana ndi Paulo, simuyenera kungokhulupirira kuti Mulungu aliko basi. Muyeneranso kukhulupirira kuti Yehova Mulungu ali ndi makhalidwe abwino amene anthu ambiri amachita nawo chidwi ndiponso amawapangitsa kumukonda.—Salmo 83:18; Yohane 6:44; Yakobe 4:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti, “Kodi Chisinthiko Chinachitikadi?” mu Galamukani! ya September 2006.

^ ndime 14 DNA ndi chidule cha mawu akuti deoxyribonucleic acid.

^ ndime 15 Nthawi imene Charles Darwin ankayambitsa mfundo yakuti zamoyo zinachita kusanduka, sankadziwa zambiri zokhudza mmene selo imagwirira ntchito.

[Chithunzi patsamba 24]

KODI ZITHU ZOIPA ZIMENE ZIMACHITIKA M’ZIPEMBEDZO NDI UMBONI WAKUTI KULIBE MULUNGU?

Anthu ambiri sakhulupirira zoti kuli Mlengi chifukwa cha zinthu zoipa zambiri zimene anthu a m’zipembedzo zosiyanasiyana akhala akuchita, monga nkhanza ndi katangale. Kodi zimenezi ndi umboni wakuti kulibe Mulungu? Ayi. M’mawu oyamba a m’buku la Antony Flew, munthu wina dzina lake Roy Abraham Varghese, ananena kuti: “Kuchita zinthu motayirira komanso nkhanza zimene anthu a m’zipembedzo amachita si umboni wakuti kulibe Mulungu.”

[Zithunzi patsamba 23]

Tikaona mabwinja timakhulupirira kuti pali anthu ena amene anamangapo. Kodi sitiyenera kukhulupiriranso kuti palinso amene anapanga zinthu za m’chilengedwe?

[Chithunzi patsamba 23]

Albert Einstein

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

DNA ili ngati kabuku kakang’ono kwambiri kokhala ndi malangizo ofunika kwambiri

[Zithunzi patsamba 25]

Asayansi amati ubongo ndi “chinthu chovuta kumvetsa kwambiri m’chilengedwe chonse”

[Mawu a Chithunzi patsamba 22]

© The Print Collector/age fotostock