Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinalipo Kale M’chilengedwe

Zinalipo Kale M’chilengedwe

Zinalipo Kale M’chilengedwe

“Tafunsira . . . mbalame za m’mlengalenga, zidzakuuza; . . . Dzanja la Yehova lichita ichi?”—Yobu 12:7-9.

ZIWALO zonse za mbalame zimaoneka kuti zinapangidwa kuti zizithandiza mbalamezo kuuluka. Mwachitsanzo, mbalame zili ndi nthenga zopepuka koma zolimba kwambiri zimene zimathandiza kuti zizitha kuuluka mosavuta. N’chiyani chimachititsa kuti nthengazi zikhale zopepuka koma zolimba kwambiri? Chifukwa chakuti kamtengo ka nthenga kamakhala ndi mphako mkati mwake koma kunja kwake kamakhala kokhakhala. Akatswiri opanga ndege amaona mmene nthenga za mbalame zinapangidwira kuti athe kupanga ndege.

Mafupa a mbalame anapangidwanso modabwitsa. Mafupa ambiri a mbalame amakhala ndi mphako ndipo ena amakhala ndi tinthu tolimbitsa mafupawo mkati mwake. N’zochititsa chidwi kuti luso limeneli analigwiritsa ntchito popanga chombo chopita kumwezi.

Kuti ndege isagwe ikamauluka, oyendetsa ndegeyo amadina mabatani ena ndi ena othandiza kupinda moyenerera mapiko ndi chipsepse cha ndegeyo. Mbalame imagwiritsa ntchito minofu 48 kuti izitha kupinda mapiko ake kuti iziuluka mosavuta. Imatha kuchita zimenezi maulendo angapo pa sekondi imodzi yokha. M’pake kuti akatswiri opanga ndege amasirira mmene mbalame imaulukira ndipo amaphunzira zambiri ku mbalamezo.

Ndege imafunika injini yamphamvu komanso mafuta ambiri kuti iuluke makamaka ponyamuka. Mbalame zilibe injini, m’malomwake zili ndi mtima wamphamvu ndiponso waukulu, umene umagunda mofulumira kwambiri kuposa mtima wa nyama zina zazikulu ngati mbalamezo. Mbalame zilinso ndi mapapo amphamvu kwambiri ndipo mosiyana ndi nyama zina, mapapowa ali ndi njira imodzi yodutsira mpweya.

Kodi mtima wa mbalame ndi wamphamvu bwanji? Kuti akatswiri adziwe kuti ndege ndi yamphamvu kwambiri amaonera kuchuluka kwa mafuta amene imanyamula. Mwachitsanzo, ndege ya Boeing 747 ikamayenda ulendo wa maola 10, imanyamula mafuta ambiri, pafupifupi 30 peresenti ya kulemera konse kwa ndegeyo. Kambalame kenakake kooneka ngati mpheta kakamayenda ulendo wa maola 10 ngati umenewu, sikelo yake imatsika ndi theka. Koma mbalame inayake yaikulu ngati nantchengwa ikamanyamuka ku Alaska kupita New Zealand imakhala itanenepa kwambiri ndipo n’zochititsa chidwi kuti imatha kuyenda ulendo wa maola 190 osaima paliponse. Palibe ndege iliyonse imene ingayende ulendo wautali choncho popanda kuima.