Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinalipo Kale M’chilengedwe

Zinalipo Kale M’chilengedwe

Zinalipo Kale M’chilengedwe

“Khutu lakumva, ndi diso lopenya, Yehova anapanga onse awiriwo.”—Miyambo 20:12.

MASO anu ali ngati kamera ya TV. Amati akaona chithunzi, amachitumiza ku ubongo kudzera m’mitsempha ya m’maso. Ndipo ubongo ndi umene umathandiza kuti munthu azindikire chithunzicho.

Diso lanu ndi laling’ono kwambiri. Limalemera pafupifupi magalamu 8 ndipo ndi lotambalala mamilimita 24. Koma limachita zinthu zodabwitsa. Mwachitsanzo, lili ndi maselo okuthandizani kuona mukakhala malo owala kwambiri ndiponso ena okuthandizani kuona mukakhala pamdima. Moti mukachoka malo owala kwambiri n’kupita malo amdima, m’mphindi 30 zokha maso anu amayamba kuona bwinobwino, mwina kuwirikiza nthawi 10,000 kuposa poyamba.

Maso anu ndi amphamvu kwambiri kuposa makamera ambiri. Kodi chimachititsa n’chiyani kuti akhale amphamvu chonchi? Chifukwa chakuti ali ndi maselo ambirimbiri okuthandizani kuona. Diso lanu lili ndi malo enaake aang’ono kwambiri omwe ali ndi maselo ambiri okuthandizani kuona bwino kwambiri. Kachigawo kamene kamatithandiza kuona ndi kakang’ono kwambiri, koma anthufe timaganiza ngati ndi diso lonse. N’zochititsa chidwi kuti kachigawo kamene kamatithandiza kuona ndi kakang’ono kwambiri ngati kachizindikiro kopumira kamene kali kumapeto kwa chiganizochi.

Kuwala kochokera ku chinthu kukalowa m’maso, maselo othandiza kuona amasiya zinthu zosafunikira n’kutenga zofunikira zokha n’kuzitumiza ku ubongo kudzera mu mtsempha waukulu wa diso.

Ubongo wanu ukalandira chithunzicho umachikonza kuti chioneke mmene chilili ndiponso mtundu wake, kaya ndi chobiriwira, chofiira kapena chabuluu. Ubongo wanu umathanso kukuthandizani kudziwa kuti chithunzicho chili pa mtunda wautali bwanji.

Tangoganizani: Maso anu amatha kuona khamu la anthu patali ndipo kenako amatumiza uthenga ku ubongo, ndipo ubongowo umakuthandizani kuona anthu osiyanasiyana amene ali pagulupo. Ubongo wanu umayerekezera nkhope zosiyanasiyana za anthuwo ndi zimene munazionapo kale ndipo nthawi yomweyo mumatha kuzindikira kuti pagulupo pali mnzanu. Kodi zimenezi si zodabwitsa?

[Chithunzi patsamba 7]

Mmene diso limagwirira ntchito, ndi umboni wakuti linapangidwa ndi winawake wanzeru kwambiri