Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilengedwe Chimatiphunzitsa Zambiri

Chilengedwe Chimatiphunzitsa Zambiri

Chilengedwe Chimatiphunzitsa Zambiri

“Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru.”—Salmo 104:24.

ANTHU ambiri amagwiritsa ntchito mawu akuti “chilengedwe” ponena za chinthu chimene chinapangitsa kuti zinthu zimene timaona zikhalepo. Mwachitsanzo, magazini ina inati: “Nthenga ndi zogometsa komanso zilipo zamitundu yambiri kuposa zinthu zonse za pa khungu la nyama zimene chilengedwe chinapanga.” (Scientific American, March 2003) Ngakhale kuti mwina munthu amene analemba nkhaniyi ankangotanthauza mphamvu inayake ponena mawu akuti “chilengedwe,” iye ananena kuti chilengedwe chinapanga nthenga. Koma kodi chilengedwe chingapange zinthu?

Mawu akuti “kupanga” amatanthauza kukonza chinthu uli ndi cholinga chinachake m’maganizo mwako. Anthu okha ndi amene angakonze kapena kupanga chinthu chifukwa amatha kuganiza. Ndipo munthu amene wapanga chinthucho amakhala ndi dzina. Mlengi amene anapanga chilengedwechi ali ndi dzina, ndipo dzina lakelo ndi Yehova. Iye ndi “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” ndipo ‘analenga zinthu zonse.’—Salmo 83:18; Chivumbulutso 4:11.

Kodi chilengedwe chimatiphunzitsa chiyani? Chimatiphunzitsa za Yehova ndiponso makhalidwe ake apamwamba monga nzeru. Baibulo limati: “Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Tikayang’ana chilengedwe, timaona kuti Mulungu ali ndi nzeru zakuya kuposa ifeyo. Choncho, ngati iye amapanga zinthu zabwino kuposa zimene akatswiri amapanga, tiyenera kukhulupiriranso kuti iye angatipatse malangizo abwino kwambiri kuposa amene anthu angatipatse.

Malangizo amenewa amapezeka m’Mawu ake, Baibulo. Kodi mukuganiza kuti Mlengi amene anatipanga kuti tizitha kulankhula, amafunanso kuti azilankhula nafe? Inde, chifukwa Baibulo limati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16.

Ngati mumasangalala kuphunzira za anthu amene anatulukira nzeru zopangira zinthu zatsopano, mungasangalale kwambiri kuphunzira za Mlengi. Mwachitsanzo, mwina mungasangalale kudziwa mayankho a mafunso awa: Kodi n’chifukwa chiyani anthufe timavutika komanso kufa? Kodi n’cholinga cha Mulungu kuti tizivutika komanso kufa? Ngati si cholinga chake, n’chifukwa chiyani iye amalola kuti tizivutika?

Asayansi aphunzira kapangidwe ka zinthu zosiyanasiyana kuchokera ku zinthu zimene Yehova anapanga. Inunso mungaphunzire zambiri kuchokera kwa Mlengi wathu. Mwachitsanzo, mungaphunzire mmene mungakhalire ndi banja losangalala, mmene mungalerere ana, ndiponso mungadziwe cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili ndi zinthu zinanso zimene zingakuthandizeni pamoyo wanu. Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lingakuthandizeni kwambiri kumvetsa Mawu a Mulungu.