Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zilumba za Faeroe Zinalumikizana Mochititsa Chidwi

Zilumba za Faeroe Zinalumikizana Mochititsa Chidwi

Zilumba za Faeroe Zinalumikizana Mochititsa Chidwi

Zilumba za Faeroe zili kumpoto kwa nyanja ya Atlantic, ndipo zilipo 18. Anthu apazilumbazi amalankhula Chifaeroe. Mukamayang’ana zilumba zokongolazi, mumaona kuti mapiri alumikizana ndi nyanja. Kufupi ndi nyanjayi, kuli midzi yomwe nyumba zake zinapakidwa penti yamitundumitundu. M’nyengo yamvula, m’mapiri onsewa mumakongola kwambiri chifukwa cha udzu wobiriwira.

Anthu okwana 48,000 amene amakhala pazilumbazi amachita zinthu mogwirizana, koma nthawi zina zimavuta kuti akumane. Kale anthu ankagwiritsa ntchito mabwato kuti achoke chilumba china kupita china. Akafuna kuchoka mudzi wina kupita wina, ankayenda wapansi, ndipo ankadutsa m’mapiri ndiponso m’makhwawa. Ndipo nthawi imeneyo zinali zovuta kwambiri kumanga nyumba chifukwa zida zonse zomangira zinkabwera pabwato kuchokera kudoko linalake laling’ono. Zidazo akazitenga padokopo, ankapita nazo kumudzi ndipo kenako ntchito yomanga inkayamba.

Anthu Oyamba Kukhala Pazilumbazi

Nkhani yakale kwambiri yonena za zilumba za Faeroe inalembedwa ndi munthu wina wa ku Ireland cha m’ma 825 C.E. Iye ananena kuti zaka 100 m’mbuyomo iye asanafike, pazilumbazi pankakhala anthu ena a ku Ireland. Komabe, anthu ena amati Grímur Kamban wa ku Norway ndiye anali woyamba kumanga nyumba pazilumbazi, chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 800.

Ngakhale kuti anthu oyambirira kukhala pazilumbazi ankadalira usodzi, iwo ankawetanso nkhosa. Ndipotu dzina lakuti “Faeroe” limatanthauza “Zilumba za nkhosa.” Ngakhale masiku ano anthu ambiri okhala kuzilumbazi amaweta nkhosa. Ubweya wa nkhosa amaugwiritsa ntchito popangira zovala zosiyanasiyana. Ubweya umenewu ndi wofunika kwambiri ndipo anthu ambiri amanena kuti ndi ‘ubweya wa nkhosa ndi golide wa pazilumbazi.’

Ngakhale masiku ano, pazilumbazi pali nkhosa zambiri kuposa anthu. Nkhosa akazipha, amazipachika m’mwamba pamthunzi ndiponso popita mphepo. Zimenezi zimachititsa kuti nyama yake izikhala yokoma kwambiri.

Popeza kuti pazilumbazi pali anthu ochepa, anthu ake amagwirizana kwambiri ndipo amachitira limodzi zinthu zambiri. Kumangidwa kwa misewu yatsopano komanso kubwera kwa zipangizo zolankhulirana kwathandiza kuti anthu apazilumbazi aziyenderana komanso kulankhulana mosavuta.

Misewu ya Pansi pa Nthaka Imagwirizanitsa Anthu

Msewu woyamba wa pansi pa nthaka ku Faeroe unamangidwa m’chaka cha 1963. Msewuwu unadutsa pansi pa phiri ndipo umalumikiza midzi iwiri ya pachilumba cha Suðuroy, chomwe chili kum’mwera kwa zilumba za Faeroe. Pomanga msewuwu, ankakumba mbali zonse ziwiri za phirilo ndi zida za mphamvu kwambiri.

Msewu wina umene wamangidwa posachedwapa, umalumikiza zilumba ziwiri zazikulu kwambiri. Msewuwu uli pansi kwambiri mwina mpaka mamita 150 kuchokera pamwamba pa madzi. Pomanga msewuwu, ankagwiritsa ntchito chitsulo choboolera miyala chachitali mamita asanu. Ndipo kenako kumapeto kwa chitsulochi ankaikako zinthu zoti ziziphulika. Zikaphulika, zinkaswa miyala ndipo kenako ankalambula msewu mamita asanu. Ankachita zimenezi mobwerezabwereza mpaka kulambula msewu wa makilomita 6. Msewuwu unatsegulidwa pa April 29, 2006.

Panopa, pazilumba za Faeroe pali misewu yokwana 18 yomwe inamangidwa pansi pa nthaka. Iwiri ili pansi kwambiri ndipo imalumikiza chilumba ndi chilumba. Tikayerekezera chiwerengero cha misewu ya pansi pa nthaka ndi chiwerengero cha anthu, zilumbazi zili ndi misewu yambiri kuposa dziko lina lililonse. Komabe, boma likufuna kumanga misewu ina ya pansi pa nthaka. Nyumba ya malamulo inagwirizana kuti amange misewu ina iwiri yotere yoti ilumikize zilumba zikuluzikulu. Umodzi wa misewuyi ukuyembekezereka kutha m’chaka cha 2012, ndipo udzakhala wa makilomita pafupifupi 12. Ukadzatha, udzakhala msewu waukulu kwambiri wa pansi pa nthaka padziko lonse.

Chinthu Chinanso Chomwe Chimagwirizanitsa Anthu

Pazilumba za Faeroe pali anthu enanso omwe amagwirizana kwambiri chifukwa cha kutumikira Mulungu. Anthu amenewa ndi a Mboni za Yehova. Anthu oyambirira a Mboni kufika pazilumbazi, anali amayi awiri ochokera ku Denmark ndipo anafika pazilumbazi m’chaka cha 1935. Iwo ankayenda nyumba ndi nyumba, kulalikira za uthenga wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Mulungu. M’kupita kwa nthawi, anthu ena analandira uthengawu ndipo nawonso anayamba kulalikira nyumba ndi nyumba.—Mateyo 24:14.

Masiku ano pazilumbazi pali a Mboni okwana 100 omwe amasonkhana mlungu ndi mlungu mu Nyumba za Ufumu zokwana zinayi. Iwo amachita utumiki wawo mwakhama, ndipo misewu yabwino ya pazilumbazi imawathandiza kuti aziyenda mosavuta popita ku zilumba zokongola zakumpoto kwa nyanja ya Atlantic zimenezi.

[Chithunzi patsamba 17]

Msewu uwu unadutsa umalumikiza zilumba ziwiri zikuluzikulu. Komanso uli pansi kwambiri mwina mamita 150 kuchokera pamwamba pa madzi