Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chipatala Choyendayenda

Chipatala Choyendayenda

Chipatala Choyendayenda

● Tsiku lina mayi wina woyembekezera anali pamsonkhano ndipo ankamvetsera mwachidwi nkhani ya m’Baibulo. Mwadzidzidzi matenda anamuyamba. Koma pasanapite nthawi yaitali, panafika ambulansi yomwe inatengera iye ndi mwamuna wake kuchipatala. Mayiyo atafika kuchipatala anabereka mwana wamkazi wokongola kwambiri.

Masiku ano, maambulansi akugwira ntchito yotamandika kwambiri yothandiza anthu amene akudwala mwakayakaya m’mayiko ambiri kwambiri. M’maambulansi amenewa mumakhala anthu anthu odziwa bwino ntchito yawo, monga madokotala, manesi ndiponso madalaivala. * Iwo amakhala okonzeka kuthandiza anthu amene avulala pangozi zapamsewu, komanso amene adwala mwadzidzidzi matenda a mtima, kufa ziwalo, kapena amayi atsala pang’ono kubereka. Chaka chilichonse, maambulansiwa oyendayenda amenewa amapulumutsa miyoyo ya anthu ambiri.

Mwachitsanzo, mu 2004, zigawenga zitachitira chiwembu sitima zinayi zonyamula anthu mumzinda wa Madrid, ku Spain, anthu ogwira ntchito zachipatala oyenda mu maambulansi anafika mwamsangamsanga ndipo anapulumutsa anthu pafupifupi 400. * Dr. Ervigio Corral Torres, yemwe ndi mkulu wa dipatimenti yothandiza anthu pangozi mumzinda wa Madrid, anati: “Atolankhani amakonda kulemba zimene madokotala achita panthawi yomwe kwachitika zauchigawenga, koma ntchito yaikulu timaigwira tikamayendayenda m’misewu tsiku ndi tsiku kuti tithandize anthu. Timapulumutsa anthu amene timawapeza atatsala pang’ono kufa.”

Atafunsidwa kuti afotokoze zimene zingathandize kuti ntchito yawo iziyenda bwino, Dr. Corral Torres, anati: “M’pofunika kuti tiyesetse kudziwitsa anthu kuti azitiimbira foni akakhala ndi vuto. Cholinga chathu n’kupereka thandizo la mankhwala loyenerera kwa anthu amene akufunikira thandizolo mwamsanga. Timapita kukathandiza munthuyo akangotiimbira foni.” M’mizinda ikuluikulu, maambulansiwa amafika pasanathe ndi mphindi 10 zomwe.

M’mizinda ikuluikulu monga São Paulo, m’dziko la Brazil, maambulansi amavutika kuyenda chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto. Choncho pamakhala anthu ena odziwa zachipatala amene amakafika pamalo angoziwo pa njinga zamoto. Akafika amayamba kuthandiza anthu ovulalawo uku akudikirira ambulansi. Mizinda inanso yomwe yayamba kugwiritsa ntchito njinga zoterezi ndi London ku England, Kuala Lumpur ku Malaysia, ndi Miami ku United States.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Madalaivala a maambulansiwa amaphunzitsidwanso mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zachipatala zimene zimakhala mu ambulansimo komanso mmene angaiyendetsere mosamala mogwirizana ndi wodwala amene atenga.

^ ndime 4 Onani Galamukani! ya Chingelezi ya November 8, 2004, tsamba 14.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

MUNGATHANDIZE BWANJI PANGOZI?

Pakachitika ngozi, muziyesetsa kuchita zotsatirazi:

1. Muziimba foni mwamsanga. Nambala yodziwitsira madokotala za ngozi ku Malawi ndi 998, ku Ulaya ndi 112 ndipo ku United States ndi 911.

2. Muzifotokoza bwinobwino malo amene pachitikira ngoziyo.

3. Muzifotokoza mmene wovulalayo alili. Mwachitsanzo, kodi akupuma? Kodi wakomoka? Kodi akutaya magazi?

4. Ngati munthuyo wavulala kwambiri, musamusunthe chifukwa kuchita zimenezo kungawonjezere kuvulalako.

5. Ngati munthuyo akusanza, mugonekeni cham’mbali kuti azitha kupuma bwinobwino.