Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakudya Chomwe Tizilombo Timakonda

Chakudya Chomwe Tizilombo Timakonda

Chakudya Chomwe Tizilombo Timakonda

● Tizilombo tambiri timakonda kudya zakudya zimene zili ndi zinthu zambiri zofunika m’thupi. Tizilomboti timapeza zinthu zimenezi m’maluwa. Maluwa ambiri amakhala owala moti amakopa tizilombo. Ndipo tizilomboto tikatera pa maluwawo, timadya mungu kapena kuyamwa timadzi ta m’maluwawo.

Usiku, tizilomboti timazizidwa kwambiri. Choncho kukacha, timadalira dzuwa kuti tiyambenso kuchita zinthu bwino. Maluwa ambiri amakhala ndi zonse zimene tizilombo timafunikira, monga chakudya chopatsa thanzi ndiponso malo oti tiothere dzuwa. Chitsanzo chodziwika bwino cha maluwa amenewa ndi maluwa enaake ooneka ngati mpendadzuwa.

Maluwa amenewa amamera kwambiri ku Ulaya ndiponso ku North America. Mutangowaona koyamba, simungachite nawo chidwi kwenikweni, koma mutawang’anitsitsa, mungaone kuti pamaluwapo pakuchitika zambiri. Tizilombo timakonda kutera pa maluwa amenewa kukangocha. Maluwa amenewa amakhala oyera m’mbali mwake ndipo zimenezi zimachititsa kuti kuwala kwa dzuwa kuzifikira pamenepa. Pakati penipeni pamakhala pachikasu ndipo m’pamene tizilomboti timakhala kwinaku tikuwothera dzuwa. *

Pakatikati pa maluwawa pamakhala mungu wochuluka ndiponso timadzi tambiri, ndipo tizilombo timakopeka kwambiri ndi zimenezi chifukwa ndiye kudya kwawo. M’mawa uliwonse, tizilombo timaona kuti malo abwino kwambiri kupita ndi pamaluwa amenewa chifukwa pamapezeka chakudya chokoma ndiponso pamatentha.

Choncho kunja kukangoti kwawala, tizilombo tambirimbiri timapita kukatera m’maluwa ooneka ngati mpendadzuwa amenewa. Mutayang’anitsitsa, mukhoza kuona tizilombo tosiyanasiyana, monga agulugufe ndi tizilombo tina touluka. Koma ngati mukungoyang’ana mwachisawawa, simungaone tizilombo tochititsa chidwi timeneti.

Choncho, tsiku lina mukadzakhala ndi mwayi woyenda m’tchire, mudzachita bwino kuyesetsa kuona tizilombo timeneti. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuyamikira ndiponso kutamanda Mulungu amene analenga zinthu zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Asayansi apeza kuti maluwa ena amatentha kwambiri kuposa malo apafupi ndi maluwawo.