Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinasankha Ntchito Yabwino

Ndinasankha Ntchito Yabwino

Ndinasankha Ntchito Yabwino

Yosimbidwa ndi Plamen Kostadinov

INALI 12 koloko masana ndipo ndinali ndikungodzuka kumene. Mabotolo a mowa anali mbwee m’nyumba monse komanso munkangonunkha fodya yekhayekha. Tsiku limeneli ndinali wokhumudwa kwambiri ngakhale kuti dzulo lake tinali pachisangalalo. Anzanga onse anali atachoka n’kundisiya ndekhandekha. Chilichonse sichinkandisangalatsa. Ndiloleni ndifotokoze chimene chinachititsa kuti zinthu zifike poipa chonchi pamoyo wanga.

Mu 1980, ndili ndi zaka 14, ndinayamba maphunziro a luso la zojambulajambula. Bambo anga anali atangondiuza kumene kuti ndasankhidwa kukachita maphunziro a zojambulajambula pakoleji ina m’tawuni ya Troyan, ku Bulgaria. Ndinasangalala kwambiri ndipo kumapeto kwa chaka chimenechi, ndinachoka m’tawuni yakwathu ya Lovech kupita ku Troyan.

Kukhala kutali ndi makolo anga kunkandisangalatsa kwambiri chifukwa ndinali ndi ufulu wochita chilichonse chimene ndikufuna. Ndinayamba kusuta ndiponso nthawi zambiri ine ndi anzanga akusukulu tinkaledzera kwambiri ngakhale kuti sitinkaloledwa kuchita zimenezi. Koma ine ndinkasangalala kwambiri kuphwanya malamulo amenewa.

Chidwi changa pa zojambulajambula chinapitiriza kukula. Ndinkachita bwino kwambiri pankhani ya zojambulajambula kuposa anzanga ndipo ndinayamba kulakalaka kuti ndidzakhale katswiri wotchuka kwambiri. Patapita zaka zisanu, ndinamaliza maphunziro anga ku Troyan, koma ndinkafunitsitsa kukapitiriza maphunziro kusukulu ina mumzinda wa Sofia, womwe ndi likulu la dziko la Bulgaria. Sukuluyi inali imodzi mwa sukulu zapamwamba kwambiri ku Bulgaria. Mu 1988, ndinayamba maphunzirowa ndipo ndinali mmodzi mwa ana 8 okha m’dziko lonse la Bulgaria omwe anasankhidwa kukaphunzira pasukuluyi. Ndinanyadira kwambiri ndipo tsiku lina ndinadziyang’ana pagalasi n’kudziuza monyada kuti, ‘Plamen, tsopano usakaikire zoti ukhala katswiri wa zojambujambula wotchuka kwambiri.’

Ndinalowerera

Pasanapite nthawi yaitali, ndinayamba kuvala zovala za mtundu wakuda ndipo sindinkameta tsitsi ndi ndevu. Anthu ambiri ankaona kuti katswiri wa zojambulajambula ayenera kumaoneka chonchi. Choncho, ndinayamba kuchita zinthu zimene ndinkaona kuti ndi zimene anthu amayembekezera kwa akatswiri a zojambulajambula. Ndinachita lendi nyumba inayake yomwe ndinkangosiya katundu ali mbwee. Kenako ndinagula kagalu ndiponso mphaka wa ana atatu n’kumaweta. Ndinkasakaza kwambiri ndalama.

Koma chidwi changa pa zojambulajambula chinapitirizabe kukula ndipo nthawi zambiri ndinkakhalira kujambula zinthu zosiyanasiyana zimene zinali m’maganizo mwanga. Ngakhale m’nyumba yanga ndinajambulajambulamo zithunzi. Ndinkaona kuti chimenechi ndi chiyambi cha ntchito yabwino kwambiri.

Ndinali munthu wokonda kwambiri zisangalalo. Nthawi zambiri ine ndi anzanga akusukulu tinkakumana m’nyumba yanga ndipo tinkamvetsera nyimbo kwinaku tikumwa mowa. Tinkachita zimenezi ngakhale panthawi yomwe tinkakonzekera mayeso. Tinkakonda kukambirana za anthu oimba osiyanasiyana, luso la zojambulajambula ndiponso cholinga cha moyo. Nthawi zina tinkakambirana zinthu zokhudza mizimu. Zimene tinkakambiranazi ndinkatha kuziona m’maganizo mwanga ndipo zinkandichititsa kuti ndisasowe chojambula. Ndinkafuna kuti ndizikhala wosangalala nthawi zonse, koma mowa ukangochoka m’mutu ndinkakhala wokhumudwa komanso wosasangalala.

Nditakhala moyo umenewu kwa zaka 10, ndinkaona kuti palibe chikuyenda. Mosiyana ndi zithunzi zimene ndinkajambula, zomwe zinali zowala, moyo wanga unali mumdima ndipo palibe chinkandisangalatsa. Maganizo omwe ndinali nawo oti ndidzakhale katswiri wa zojambulajambula wotchuka kwambiri anayamba kundichokera. Ndinkavutika maganizo ndipo sindinkadziwa kuti moyo wanga ukulowera kuti. Panthawiyi m’pamene panachitika zimene ndafotokoza kumayambiriro kwa nkhaniyi zija.

Choonadi Chinandithandiza

Mu 1990, ndinaganiza zopita ku chionetsero cha zinthu zojambulajambula ku Lovech n’cholinga choti ndikawonetseko zinthu zanga. Ndinapempha mtsikana wina, dzina lake Yanita, amene ndinkaphunzira naye ku Sofia kuti andiperekeze. Iye anali wochokeranso ku Lovech. Chionetserochi chitatha, ine ndi Yanita tinapita ku lesitilanti yapafupi kuti tikadye. Tikucheza kumeneku, iye anayamba kundifotokozera zinthu zimene ankaphunzira m’Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anandifotokozera kuti Baibulo limati kudzakhala dziko latsopano. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri.

Atabwerera ku Sofia, Yanita anapitirizabe kuphunzira Baibulo ndipo nthawi ndi nthawi ankandibweretsera mabuku ofotokoza Baibulo. Ndimakumbukirabe kuti kwanthawi yochepa chabe ndinamaliza kuwerenga kabuku kakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano” ndiponso buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Nditawerenga mabukuwa, sindinakayikire zoti Mulungu aliko, ndipo nthawi yomweyo ndinafuna kudziwa mmene ndingamapempherere. Ndimakumbukirabe pemphero langa loyamba. Ndinagwada n’kunena nkhawa zanga zonse kwa Yehova. Nditamaliza kupemphera, ndinakhulupirira ndi mtima wonse kuti iye wamva pemphero langa. Kusungulumwa kunayamba kuchepa, ndipo ndinali ndi chimwemwe komanso mtendere wamumtima.

Ku Sofia, Yanita anandithandiza kudziwana ndi banja lina la Mboni za Yehova. Iwo anadzipereka kuti azindiphunzitsa Baibulo ndipo anandiitanira kumisonkhano yawo. Ndinapita koyamba ku msonkhano wa Mboni za Yehova mu June 1991. Ndinafika kutatsala maola awiri kuti msonkhano uyambe ndipo ndinakhala pamalo penapake n’kumayembekezera. Ndinali ndi mantha ndipo ndinali ndi chilendo moti ndinkakayikira ngati angandilandire bwino. Koma ndinadabwa kwambiri kuona kuti aliyense anandilandira mosangalala ngakhale kuti sindinkaoneka bwino chifukwa cha kavalidwe kanga komanso tsitsi langa lalitali. Kuchokera nthawi imeneyi, sindinkajomba kumisonkhano ndipo ndinkaphunzira Baibulo kawiri pa mlungu.

Ndinasangalala kwambiri nditalandira Baibulo langalanga. Nditawerenga ulaliki wapaphiri, ndinakhudzidwa mtima kwambiri chifukwa ndinali ndisanawerengepo mawu anzeru ngati amenewa. Nditapitiriza kuphunzira Baibulo, ndinayamba kuona kuti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yosinthadi munthu, mogwirizana ndi mawu a pa Aefeso 4:23, akuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.” Ndinasiya kusuta ndipo ndinayamba kudzisamalira. Ndinasintha kwambiri moti tsiku lina bambo anga atabwera kudzandichingamira kumalo okwerera sitima ku Lovech, anandidutsa chifukwa sanathe kundizindikira.

Ndinayambanso kusamalira m’nyumba mwanga. Ndinafufuta zithunzi zomwe ndinajambula m’nyumbamo ndiponso ndinasiya kudalira fodya kuti ndigwire bwino ntchito. Ndinkayesetsa kukhala waukhondo pachilichonse. Ndinapaka nyumba yanga penti yoyera ndipo ndinafufuta chithunzi cha maso atatu chomwe ndinajambula pakhoma pa nyumbayo.

Kusintha kumeneku kunachititsa kuti anzanga ambiri asiye kucheza nane. Komabe pasanapite nthawi yaitali, ndinapeza anzanga ena ambiri kumisonkhano yachikhristu, omwe ndimagwirizana nawo kwambiri mpaka pano. Chifukwa chocheza ndi anthu amenewa ndinkalimbikitsidwa ndipo ndinapita patsogolo mofulumira. Pa March 22, 1992, ndinabatizidwa pa msonkhano woyamba waukulu wa Mboni za Yehova ku Bulgaria, womwe unachitikira mumzinda wa Plovdiv.

Ndinabwerera ku Lovech

Ngakhale kuti zinali zovuta kuti munthu wodziwa zojambulajambula ngati ine akhale m’tawuni yaing’ono, ndinaganiza kuti ndikamaliza maphunziro anga ndibwerere ku Lovech. Ndinaona kuti n’zovuta kwambiri kwa ine kutanganidwa ndi zojambulajambula kwinaku ndi kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo. Choncho ndinaganiza zosintha ntchito yanga n’kuyamba kumaphunzitsa anthu Baibulo. Ndidakali kusukulu ya zojambulajambula ku Sofia, Yanita, yemwe anamaliza maphunziro ake kutatsala zaka zitatu kuti ine ndimalize, anali atayamba kale kuphunzitsa mwachangu choonadi cha m’Baibulo ku Lovech. Kupatula iyeyo kunalibenso wa Mboni wina.

Panthawi imene ndimabwerera ku Lovech n’kuti kuli kagulu ka anthu kamene kankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinkasangalala kwambiri kuyendera anthu m’nyumba zawo ndi kuwathandiza kudziwa choonadi cha m’Baibulo chokhudza tsogolo la anthu, zimene ineyo ndinaphunzira. Kenako ndinayamba kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse.

Koma pasanapite nthawi, mavuto anayamba chifukwa mu 1994, boma linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Ndipo manyuzipepala anayamba kulemba nkhani zambiri zabodza zoipitsa gulu lathu. * Nthawi zambiri Mboni za Yehova zinkaitanidwa kupolisi kukayankha mafunso ndipo mabuku athu ankalandidwa. Panthawi yovuta imeneyi sitinkaloledwa kuchita misonkhano yathu yachikhristu. Komabe tinkachita misonkhano yathu m’nyumba inayake yaing’ono, yomwe inagundizana ndi nyumba imene Yanita ankakhala. Tsiku lina tinapanikizana m’kanyumba kameneka anthu okwana 42. Kuti anthu apafupi asadabwe poimba nyimbo za Ufumu, tinaseka mazenera. Nthawi zina m’nyumbamu munkatentha kwambiri koma tinkakhala osangalala kusonkhana limodzi.

Yehova Wandidalitsa Kwambiri

Ndinkachita chidwi ndi khama la Yanita pa kulambira koona, ndipo m’kupita kwa nthawi tinayamba kukondana. Tinakwatirana pa May 11, 1996. Ine ndi Yanita timagwirizana kwambiri ngakhale kuti ndife anthu osiyana. Iye ndi mnzanga wapamtima amene amandithandiza kwambiri. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa mkazi amene “mtengo wake uposa ngale.”—Miyambo 31:10

Anzanga ambiri anasankha ntchito imene ndinkaifuna poyamba ya zojambulajambula. Koma tsopano ndine wokhutira chifukwa ndinasankha ntchito yabwino kwambiri. Ndathandiza anthu ambiri kukhala ndi cholinga pamoyo wawo, ndipo tsopano ndi abale ndi alongo anga auzimu. Madalitso amene ndapeza chifukwa chotumikira Yehova sangafanane ndi kutchuka kapena zinthu zimene ndikanapeza monga katswiri wojambula zithunzi. Ndimasangalala kwambiri kuti ndinadziwa Yehova Mulungu, Mlengi Wamkulu yemwe sangafanane ndi katswiri aliyense wojambula.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha anasiya kulisindikiza.

^ ndime 22 Mu 1998, Mboni za Yehova zinatengera nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, lomwe lili mumzinda wa Strasbourg, ndipo kenako Mboni za Yehova zinaloledwanso ku Bulgaria.

[Chithunzi patsamba 12]

Ndili ndi mkazi wanga Yanita