Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukwera Phiri Lalitali N’koopsa Kodi Mungatani Mutadwala Pokwera Phiri?

Kukwera Phiri Lalitali N’koopsa Kodi Mungatani Mutadwala Pokwera Phiri?

Kukwera Phiri Lalitali N’koopsa Kodi Mungatani Mutadwala Pokwera Phiri?

“Ku Peru kuli mapiri ataliatali kwambiri amene anakhala mogundizana otchedwa Pariacaca . . . Nditangomaliza kukwera malo aatali kwambiri pamapiriwa, ndinayamba kumva ululu woopsa moti ndinkafuna kuti ndingodzigwetsa pansi. . . . Kenako m’mimba mwanga munayamba kuwira ndipo ndinayamba kusanza kwambiri moti ndinkaganiza kuti [ndifa]. Mwina zimenezi zikanapitiriza kwa nthawi yaitali, ndikanafadi. Koma mwamwayi patapita maola atatu kapena anayi zinasiya, chifukwa tinali titatsikako phirilo.”—Anatero José de Acosta, m’buku lakuti Natural and Moral History of the Indies.

CHAKUMAPETO kwa zaka za m’ma 1500, wansembe wina wochokera ku Spain, dzina lake José de Acosta, anakumana ndi vuto limeneli pamene ankakwera mapiri a Pariacaca ku Peru. Pa nthawi imeneyo, anthu ankaganiza kuti chimene chinkadwalitsa anthu choncho ndi mpweya wapoizoni wochokera m’phirilo, kapena mpweya umene milungu yoipa inkatulutsa. Koma malinga ndi zimene tikudziwa masiku ano, Acosta anadwala matenda amene munthu amadwala akakwera phiri lalitali kwambiri.

Munthu amadwala matendawa chifukwa chakuti pamwamba pa phiri pamakhala mpweya wochepa wa okosijeni. Munthu akakwera pamwamba kwambiri mapapo ake satha kukoka bwino mpweya, choncho mpweya wa okosijeni umayamba kuchepa m’thupi mwake. *

Nthawi zambiri munthu amayamba kusonyeza zizindikiro za matendawa pakatha maola anayi atakwera phirilo, ndipo akhoza kudwala kwa tsiku limodzi mpaka masiku anayi. Pa masiku amenewa, kuchepa kwa okosijeni m’magazi kumachititsa kuti thupi liyambe kupanga magazi ambiri. Magaziwa akachuluka m’thupi, thupilo limayamba kupeza okosijeni wokwanira.

Koma munthu akakwera pamwamba pa phiri mofulumira, kapena akayamba kugwira ntchito mwamphamvu thupi lake lisanazolowere kukhala pamalo okwerawo, nthawi zina m’mapapo ndi mu ubongo wake mumadzaza madzi. Popanda kuthandizidwa mwamsanga, munthuyo akhoza kufa.

Mmene Mungapewere Matendawa

Anthu apaulendo ndiponso okonda kukwera mapiri ayesapo njira zosiyanasiyana zopewera kapena zochizira matendawa. Mfundo zina zofunika kuzidziwa ndi izi:

● Musamakwere phiri lalitali ngati muli ndi matenda alionse okhudzana ndi kupuma kapena kuperewera magazi.

● Mankhwala amene amachititsa munthu kukodza pafupipafupi, amene amathandiza kuti malo amene atupa aphwere, ndi ena otero, amathandiza kupewa kapena kuchiza matendawa. Kuti mudziwe zambiri, kaonaneni ndi adokotala.

● Njira yabwino kwambiri yochizira matendawa ndiyo kupita pamalo otsikirapo. Ngati zingatheke, muvale zovala zotentha mukamatsika ndipo muyenera kupumula mukafika.

Malo ena okongola kwambiri padziko pano ali m’mapiri. (Salmo 148:9, 13) Mukhoza kukaona chilengedwe chokongolachi popanda kudwala ngati mutamachita zinthu mosamala popita kumalowa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Anthu ambiri akhoza kukwera phiri mpaka kufika pamalo aatali mamita 2,400 popanda vuto lililonse.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

Nthawi zambiri munthu amayamba kusonyeza zizindikiro za matendawa pakatha maola anayi atakwera phirilo, ndipo akhoza kudwala kwa tsiku limodzi mpaka masiku anayi

[Mawu Otsindika patsamba 20]

Njira yabwino kwambiri yochizira matendawa ndiyo kupita pamalo otsikirapo