Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“N’zodabwitsa kwambiri kuti chaka chilichonse, Baibulo ndi buku limene limagulitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse ku America, ngakhale kuti mabanja 90 pa 100 alionse ali nalo kale Baibulo. . . . Mabaibulo pafupifupi 25 miliyoni amagulitsidwa chaka chilichonse.”—THE WALL STREET JOURNAL, UNITED STATES.

“Padziko lonse, anthu 4.5 miliyoni amalumidwa ndi njoka chaka chilichonse. Anthu ena ofufuza akuti anthu osachepera 100,000 amafa chifukwa cholumidwa ndi njoka ndipo ena 250,000 amalumala.”—UNIVERSITY OF MELBOURNE, AUSTRALIA.

“M’chaka cha 2008, anthu ankatumiza mauthenga a pa intaneti okwana pafupifupi 210 biliyoni tsiku lililonse.”—NEW SCIENTIST, BRITAIN.

Phokoso la Mumsewu Limayambitsa Vuto Loiwala

“Anthu ambiri amene nyumba yawo ili pafupi ndi msewu, njanji, kapena bwalo la ndege amavutika kukumbukira zinthu kapena kuphunzira zinthu zatsopano, ngakhale azitha kugona kuli phokoso.” Ananena zimenezi ndi Ysbrand van der Werf, katswiri wa ubongo wa ku Netherlands yemwe amagwira ntchito m’bungwe loona za sayansi ya ubongo. Munthu amavutika kukumbukira zinthu ndiponso kuphunzira zinthu zatsopano ngati sagona mokwanira. Amakhalanso ndi mavuto omwewa ngati “amasokonezedwa akagona . . . ngakhale asadzuke,” inatero magazini inayake ya ku Netherlands. Kuti mbali ya ubongo imene imakhudzana ndi kukumbukira zinthu izigwira bwino ntchito, munthu amafunika kugona tulo tofa nato popanda kusokonozedwa ndi “zinthu monga phokoso ndi kuwala.”

Makombola Angayambitse Matenda a M’chifuwa

Makombola amachititsa chidwi kwambiri, koma tiufa timene timatulutsidwa akaphulika tikhoza kukudwalitsani. Makombola ambiri amakhala ndi tiufa tinatake timene timachititsa kuti azitulutsa mitundu yosiyanasiyana, monga yofiira ndi yobiriwira. Anthu ochita kafukufuku a ku Austria anayeza chipale chofewa chimene chinagwa makombola okondwerera chaka chatsopano asanaphulitsidwe ndiponso ataphulitsidwa. Iwo anapeza kuti chipale chofewa chimene chinagwa makombolawo ataphulitsidwa chinali ndi tiufa toyambitsa matenda tochuluka kwambiri. Tiufati timachititsa kuti njira yodutsa mpweya itsekeke. Choncho, ochita kafukufukuwa anati kupuma mpweya wochokera m’makombola kungakulitse matenda okhudzana ndi kupuma, monga mphumu.

Zitsulo Zoyendera Mphepo Zikupha Mileme

Magazini ya Scientific American inanena kuti ku Alberta, m’dziko la Canada, mileme ikumapezeka itafa pansi pa mapolo a zitsulo zoyendera mphepo. Ochita kafukufuku akudabwa kwambiri ndi zimenezi, chifukwa mileme ili ndi luso lotha kuzemba zinthu zimene zili m’njira yawo ikamauluka. Koma ochita kafukufuku apeza kuti pa mileme 100 iliyonse yakufa, 92 imasonyeza kuti inafa chifukwa chotuluka magazi m’mimba. Zimenezi zachititsa ofufuzawo kuganiza kuti milemeyi imavutika kupuma ikayandikira malo amene pali zitsulo zoyendera mphepozi. Milemeyi imavutika kupuma chifukwa mpweya umakhala ukuthamanga kwambiri pamalowa, popeza nsonga za zitsulozi zimathamanga kwambiri mpaka kufika makilomita 200 pa ola limodzi. Mileme imene ikufa kwambiri ndi yomwe imayenda maulendo ataliatali kupita ku madera ena komanso imadya tizilombo. Anthu ena akuda nkhawa kuti zitsulo zimenezi zisokoneza chilengedwe.