Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kutembenuzira Munthu Tsaya Lina Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kutembenuzira Munthu Tsaya Lina Kumatanthauza Chiyani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kutembenuzira Munthu Tsaya Lina Kumatanthauza Chiyani?

PA ULALIKI wake wotchuka wa paphiri, Yesu Khristu anati: “Usalimbane ndi munthu woipa; koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja, umutembenuzirenso linalo.”—Mateyo 5:39.

Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Kodi ankalimbikitsa Akhristu kuti ena akamawachitira zoipa, iwo azingoyang’ana? Mwachitsanzo, kodi Akhristu sangapite kukhoti kukadandaula ngati ena atawachitira zoipa?

Zimene Yesu Ankatanthauza

Kuti timvetse zimene Yesu ankatanthauza, tiyenera kuona nkhani yonse bwinobwino ndiponso kuganizira anthu amene ankawauza. Asanapereke malangizo amenewa, Yesu anauza omvera ake mfundo ya m’Malemba imene sinali yachilendo kwa iwo. Iye anati: “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’”—Mateyo 5:38.

Pamenepa Yesu anagwira mawu amene amapezeka pa Eksodo 21:24 ndi Levitiko 24:20. Koma tiyenera kudziwa kuti mogwirizana ndi Chilamulo chimene Mulungu anapereka, chilango cha “diso kulipira diso” chimene chimatchulidwa m’malemba amenewa chinkaperekedwa pambuyo poti munthu wopalamulayo waweruzidwa bwinobwino ndi ansembe komanso oweruza. Iwo ankaunika nkhani yonse bwinobwino komanso kufufuza ngati munthuyo anachita dala kapena ayi.—Deuteronomo 19:15-21.

Patapita nthawi, Ayuda anayamba kugwiritsira ntchito lamulo limeneli molakwa. Katswiri wina wa Baibulo wa m’zaka za m’ma 1800 dzina lake Adam Clarke, anati: “Zikuoneka kuti Ayuda anapangitsa lamuloli [diso kulipira diso, dzino kulipira dzino] kukhala maziko olangira munthu amene ayambana naye. Pobwezerapo, ankamukhaulitsa kwambiri munthuyo ndipo chilango chake chinkakhala chachikulu kuposa zimene munthuyo anawalakwira.” Komabe, Chilamulo sichinkalola kuti anthu akalakwirana, azisungirana chakukhosi n’kumakhaulitsana.

Zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki wa paphiri zokhudza ‘kutembenuzira munthu tsaya lina’ zinkagwirizana kwambiri ndi Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Yesu sankatanthauza kuti otsatira ake akamenyedwa tsaya limodzi aziperekadi tsaya lina kuti awamenyenso. M’nthawi za Baibulo, ngakhalenso masiku ano, munthu amamenya mnzake mbama makamaka chifukwa chongopsa mtima, osati n’cholinga choti amuvulaze.

Choncho, n’zoonekeratu kuti Yesu ankatanthauza kuti munthu wina akaputa mnzake pomumenya mbama kapena kumulankhula mawu opweteka, munthu woputidwayo asabwezere. Iye ayenera kupewa kuchita zinthu zimene zingachititse kuti iyeyo ndi munthu winayo azingokhalira kubwezerana choipa pa choipa.—Aroma 12:17.

Zimene Yesu ananenazi n’zofanana kwambiri ndi zimene Mfumu Solomo inanena, zakuti: “Usanene, Ndidzam’chitira zomwezo anandichitira ine; ndidzabwezera munthuyo monga mwa machitidwe ake.” (Miyambo 24:29) Munthu amene akufuna kutsatira Yesu amatembenuza tsaya lake posalola kuti zochita za munthu wina zimuchititse kukangana ndi munthuyo.—Agalatiya 5:26.

Nanga Bwanji Kudziteteza?

Kutembenuza tsaya lina sikutanthauza kuti Mkhristu sayenera kudziteteza akamamenyedwa ndi anthu. Yesu sankatanthauzanso kuti tisamachite chilichonse kuti tidzipulumutse. Iye ankatanthauza kuti tisamayambe ndi ifeyo kumenya munthu komanso tisamabwezere chifukwa chopsa mtima. Ngakhale kuti nthawi zina zingakhale bwino kungochokapo poopa kumenyana, sikulakwa kuyesetsa kudziteteza kapena kuitana apolisi kuti atithandize.

Otsatira a Yesu oyambirira ankatsatiranso mfundo zimenezi kuti ateteze ufulu wawo. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito malamulo a nthawi imeneyo kuti ateteze ufulu wake wogwira ntchito yolalikira, imene Yesu anauza otsatira ake kuti azichita. (Mateyo 28:19, 20) Paulo ndi mmishonale mnzake, Sila, atapita kukalalikira mumzinda wa Filipi, anamangidwa ndi akuluakulu a boma ndipo anawaimba mlandu woti aphwanya malamulo.

Kenako iwo anakwapulidwa pamaso pa anthu n’kuponyedwa m’ndende asanaweruzidwe n’komwe kukhoti. Paulo atapeza mpata, anagwiritsira ntchito ufulu umene anali nawo monga nzika ya Roma kuti adziteteze. Akuluakulu a boma atazindikira kuti Paulo anali nzika ya Roma, anachita mantha kwambiri ndipo anachonderera Paulo ndi Sila kuti achoke mumzindawo pasanabuke mavuto alionse. Choncho, Paulo anatisiyira chitsanzo pa nkhani ya “kuteteza uthenga wabwino ndi kuutsimikizira mwalamulo.”—Machitidwe 16:19-24, 35-40; Afilipi 1:7.

Mofanana ndi Paulo, Mboni za Yehova mobwerezabwereza zakhala zikupita kukhoti pofuna kuteteza ufulu wawo wachipembedzo. Mbonizi zimachita zimenezi ngakhale m’mayiko amene olamulira ake amati muli ufulu wolambira. Komanso anthu a Mboni za Yehova akaukiridwa ndi achifwamba kapena moyo wawo ukakhala pa ngozi, sikuti amangoperekera tsaya lina, osadziteteza. Iwo amagwiritsira ntchito malamulo a boma kuti adziteteze.

Choncho Akhristu a Mboni za Yehova amayesetsa kuteteza ufulu wawo. Komabe amadziwa kuti kuchita zimenezi nthawi zina sikungapangitse kuti apatsidwe ufulu wawo wonse. Mofanana ndi Yesu, iwo amasiya zonse m’manja mwa Mulungu. Amakhulupirira kuti Mulungu adzachitapo kanthu chifukwa iye amadziwa zonse ndipo chilango chilichonse chimene amapereka pobwezera adani ake, chimakhala chachilungamo. (Mateyo 26:51-53; Yuda 9) Akhristu oona amadziwa kuti kubwezera ndi kwa Yehova.—Aroma 12:17-19.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Akhristu ayenera kupewa kuchita chiyani?—Aroma 12:17.

● Kodi Baibulo limaletsa Akhristu kupita kukhoti pofuna kudziteteza?—Afilipi 1:7.

● Kodi Yesu sankakayikira kuti Atate ake angachite chiyani?—Mateyo 26:51-53.