Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Wanditonthoza M’mayesero Anga Onse

Mulungu Wanditonthoza M’mayesero Anga Onse

Mulungu Wanditonthoza M’mayesero Anga Onse

Yosimbidwa ndi Victoria Colloy

Dokotala wina anauza mayi anga kuti: “Palibe chilichonse chomwe tingachite kuti mwana wanu akhale bwino. Akufunika azivala zitsulo m’miyendo komanso aziyendera ndodo moyo wake wonse.” Nditamva zimenezi, ndinakhumudwa kwambiri chifukwa ndinkaona kuti ngati sindingathe kuyenda, ndiye kuti palibe chilichonse chimene ndingakwanitse kuchita.

NDINABADWA pa November 17, 1949, ku Tapachula mumzinda wa Chiapas m’dziko la Mexico. Ndinali woyamba kubadwa m’banja la ana anayi. Ndinabadwa wathanzi bwinobwino koma patangotha miyezi 6 ndinasiya kukwawa mwadzidzidzi ndipo ndinkangotha kusuntha pang’ono. Patapita miyezi ina iwiri sindinkathanso kusuntha ngakhale pang’ono. Madokotala a m’dera lathu anadabwa kwambiri chifukwa ana enanso a ku Tapachula ankasonyeza zizindikiro zomwezi. Choncho, dokotala wa zamafupa wa ku Mexico City anabwera kudzatiyeza ndipo anapeza kuti tili ndi poliyo.

Ndili ndi zaka zitatu anandichita opaleshoni m’chiuno, m’mawondo, ndiponso polumikizira mwendo ndi phazi. Kenako phewa langa lakumanja linapuwalanso. Ndili ndi zaka 6, anandipititsa kuchipatala chinachake cha ana ku Mexico City. Mayi anga ankagwira ntchito pa famu inayake kwathu ku Chiapas, choncho ku Mexico City ndinkakhala ndi agogo anga aakazi. Koma nthawi zambiri ndinkakhala ndili m’chipatala.

Ndili ndi zaka pafupifupi 8, ndinayamba kupezako bwino. Koma kenako zinthu zinasinthanso ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukanikanso kuyenda. Madokotala ananena kuti ndikufunika ndizivala zitsulo m’miyendo komanso ndiziyendera ndodo kwa moyo wanga wonse.

Pamene ndinkakwanitsa zaka 15, n’kuti nditapangidwa maopaleshoni okwana 25. Anandipanga opaleshoni ya msana, miyendo, mawondo, polumikizira mwendo ndi phazi, ndiponso zala zakumapazi. Akamaliza kundichita opaleshoni iliyonse, ankandiphunzitsanso kugwiritsa ntchito chiwalo chimene andichita opaleshonicho. Nthawi ina atandipanga opaleshoni, anaika miyendo yanga m’chikhakha. Atachotsa chikhakhacho, anandiuza kuti ndiziyendetsayendetsa miyendoyo, ndipo ndinkamva kupweteka kwambiri pochita zimenezi.

Ndinatonthozedwa Kwambiri

Ndili ndi zaka 11, mayi anga anabwera kudzandiona nditangochitidwa kumene opaleshoni. Iwo anali atangophunzira kumene kuti Yesu anachiritsa anthu odwala komanso anathandiza munthu wofa ziwalo kuti ayambe kuyenda. Anawerenga zimenezi m’magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe imafalitsidwa ndi Mboni za Yehova, ndipo anandipatsa magaziniyo. Ndinaibisa pansi pa pilo koma tsiku lina ndinapeza kuti yasowa. Manesi anali ataiona magaziniyo n’kuitenga. Iwo anandikalipira kwambiri chifukwa chowerenga magaziniyo.

Patapita pafupifupi chaka chimodzi, mayi anga anabweranso kudzandiona kuchokera ku Chiapas. Panthawiyi n’kuti iwo akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Anandibweretsera buku lakuti Kucokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezekanso. * Iwo anandiuza kuti, “Ngati ukufuna kudzakhala m’dziko latsopano limene Mulungu analonjeza, uyenera kuphunzira Baibulo. M’dziko limenelo Yesu adzakuchiritsa.” Choncho ndili ndi zaka pafupifupi 14, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ngakhale kuti agogo anga ankandiletsa. Chaka chotsatira ananditulutsa m’chipatalamo chifukwa tsopano ndinali nditakula ndipo chipatalacho chinali cha ana aang’ono.

Zimene Zandithandiza Kupirira

Zonsezi zinandichititsa kuti ndizikhala wosasangalala nthawi zonse. Popeza agogo anga ankandiletsa kuphunzira Baibulo, ndinasamuka n’kubwerera ku Chiapas komwe ndinkakhala ndi makolo anga. Komabe, panyumba pathu panali mavuto ambiri chifukwa bambo anga anali chidakwa. Kwa nthawi ndithu ndinkaona kuti palibe chifukwa chokhalira ndi moyo. Ndinkaganiza zongomwa poizoni n’kufa. Koma nditapitiriza kuphunzira Baibulo ndinasintha maganizo. Lonjezo la m’Baibulo lakuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso linandithandiza kuti ndizikhala wosangalala.

Ndinayamba kuuza anthu ena za zinthu zosangalatsa kwambiri zimene Baibulo limalonjeza. (Yesaya 2:4; 9:6, 7; 11:6-9; Chivumbulutso 21:3, 4) Patapita nthawi, pa May 8, 1968, ndili ndi zaka 18, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Kuyambira m’chaka cha 1974, ndakhala ndikulalikira kwa maola oposa 70 mwezi uliwonse. Ndimasangalala kuuza anthu ena za chiyembekezo chimenechi, chifukwa n’chimene chandithandiza kukhala ndi moyo.

Ndakhala ndi Moyo Waphindu ndi Wosangalala

Patapita nthawi, ine ndi mayi anga tinasamukira mumzinda wa Tijuana, womwe uli m’malire mwa dziko la Mexico ndi United States. Chifukwa cha mavuto athu, tinasankha malo oyenererana bwino ndi ifeyo. Zitsulo zovala m’miyendo komanso ndodo, n’zimene zimandithandiza kuti ndizitha kuyenda ndikakhala panyumba. Ndikafuna kuphika ndiponso kuchapa ndi kusita zovala, ndimakhala pa njinga ya olumala. Ndikafuna kulalikira, ndimayenda pa njinga yoyendera magetsi yomwe inapangidwa mogwirizana ndi mavuto anga.

Kuwonjezera pa kuuza anthu zimene Baibulo limaphunzitsa m’misewu komanso m’nyumba zawo, ndimapitanso pachipatala china chapafupi kukakambirana nkhani za m’Baibulo ndi anthu amene akudikirira kuti aonane ndi adokotala. Ndikamaliza kulankhula ndi anthuwo ndimapita kumsika pa njinga yangayo kukagula zinthu. Ndikabwerera kunyumba, ndimathandiza mayi anga kuphika ndi kugwira ntchito zina zapakhomo.

Kuti ndipeze ndalama, ndimagulitsa zovala zakaunjika. Panopa mayi anga ali ndi zaka 78 ndipo sangathe kuchita zambiri chifukwa amadwala matenda a mtima. Katatu konse mtima wawo unasiyapo kugunda. Choncho, ndimaonetsetsa kuti akumwa mankhwala awo komanso akudya chakudya choyenera. Ngakhale kuti ine ndi mayi anga ndife odwaladwala, timayesetsa kupita kumisonkhano ya mpingo. Pa moyo wanga ndaphunzitsa Baibulo anthu oposa 30, ndipo panopa nawonso amagwira nawo ntchito yolalikira.

Ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti m’tsogolomu lonjezo la m’Baibulo ili lidzakwaniritsidwa: “Pa nthawiyo [m’dziko latsopano la Mulungu], munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.” Panopa mawu a Mulungu otsatirawa amanditonthoza: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”—Yesaya 35:6; 41:10. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Bukuli linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1958 koma tsopano anasiya kulisindikiza.

^ ndime 18 Victoria Colloy anamwalira pa November 30, 2009, ali ndi zaka 60. Mayi ake anamwalira pa July 5, 2009.

[Chithunzi patsamba 12]

Nditavala zitsulo za m’miyendo. Apa n’kuti ndili ndi zaka 7

[Chithunzi patsamba 13]

Ndikafuna kulalikira, ndimagwiritsa ntchito njinga yoyendera magetsi yomwe inapangidwa mogwirizana ndi mavuto anga