Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

4—Muziteteza Thanzi Lanu

4—Muziteteza Thanzi Lanu

4​—Muziteteza Thanzi Lanu

“Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Kuchita zinthu zina ndi zina zosavuta zoteteza thanzi lanu, kungakuthandizeni kupewa matenda ndi mavuto ena ambiri, komanso mungapulumutse nthawi ndi ndalama zambiri.

Khalani aukhondo. Bungwe la ku America loona za matenda osiyanasiyana ndi mmene anthu angawapewere, linati: “Kusamba m’manja n’chinthu chofunika kwambiri pa zinthu zonse zothandiza kuti musafalitse matenda komanso kuti mukhale athanzi.” Akuti pafupifupi matenda 8 pa matenda 10 alionse amafalitsidwa chifukwa chosasamba m’manja. Choncho muzisamba m’manja pafupipafupi. Muzisamba m’manja makamaka musanadye, musanayambe kukonza chakudya, ngakhalenso musanagwire kapena kumanga chilonda. Komanso muzisamba m’manja mukakhudza chiweto, mukachoka kuchimbudzi, kapena mukasintha mwana thewera.

Kusamba m’manja ndi madzi ndiponso sopo n’kumene kumapha majelemusi ambiri kusiyana n’kungopukuta m’manja ndi mankhwala opha tizilombo. Ana sadwaladwala ngati makolo awo awaphunzitsa kuti azisamba m’manja komanso asamakonde kugwira pakamwa ndiponso maso awo. Kusamba tsiku lililonse ndiponso kuchapa zovala ndi zofunda zanu pafupipafupi kumathandiza kuti mukhale ndi thanzi labwino.

Pewani matenda opatsirana. Pewani kukhala pafupi kwambiri kapena kudyera mbale imodzi ndi munthu amene akudwala chimfine, chifukwa malovu kapena mamina ake akhoza kukupatsirani matendawo. Matenda monga a chiwindi a mtundu wa B ndi C, komanso HIV/AIDS, amafalikira makamaka pogonana, kubwerekana majakisoni obayira mankhwala osokoneza bongo, ndiponso kuthiridwa magazi. Katemera amatha kuteteza munthu ku matenda ena, komabe munthu wanzeru amachita zinthu mosamala akakhala pafupi ndi munthu amene ali ndi matenda opatsirana. Muzipewa kulumidwa ndi tizilombo. Musamakhale kapena kugona panja osadziteteza pa nthawi imene kuli udzudzu kapena tizilombo tina tofalitsa matenda. Muzigona m’masikito kapena kudzola mankhwala othamangitsa udzudzu. Ana makamaka amafunikira kwambiri zimenezi. *

Panyumba panu pazikhala paukhondo. Muziyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe kuti panyumba panu pazikhala paukhondo, m’kati ndi panja. Muzikwirira malo alionse amene pangadikhe madzi n’kuswana udzudzu. Zinyalala, zakudya zosavundikira, ndi zinyansi zimaitana tizilombo touluka ndiponso makoswe, ndipo zonsezi zimatha kuyambitsa matenda. Ngati mulibe chimbudzi, ndi bwino kuti mukumbe chimbudzi m’malo momangodzithandiza kutchire. Muzivundikira pachimbudzipo kuti ntchentche zisamatuluke, chifukwa zimayambitsa matenda a maso ndi matenda ena.

Pewani kudzivulaza. Muzitsatira malamulo opewera ngozi mukakhala kuntchito, mukakwera njinga yakapalasa kapena njinga yamoto, kapenanso mukamayendetsa galimoto. Muzionetsetsa kuti galimoto yanu ili ndi zonse zofunika. Muzivala zinthu zokutetezani kuti musavulale monga magalasi, chipewa, ndi nsapato. Muzimanganso lamba komanso muzivala zoteteza m’makutu. Pewani kukhala nthawi yaitali padzuwa chifukwa dzuwa limayambitsa khansa ndipo limachititsa kuti khungu likalambe mwamsanga. Ngati mumasuta fodya, siyani. Mukasiya panopa, mukhoza kupewa kudzadwala mtima, khansa ya m’mapapo, ndiponso matenda opha ziwalo. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani nkhani zoyambirira zonena za matenda ofalitsidwa ndi tizilombo mu Galamukani! ya June 8, 2003.

^ ndime 7 Onani nkhani zoyambirira za mu Galamukani! ya May 2010 ya mutu wakuti “Kodi Munthu Angatani Kuti Asiye Kusuta?”