Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani Zokhudza Kusuta Fodya?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani Zokhudza Kusuta Fodya?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani Zokhudza Kusuta Fodya?

Werengani mfundo zili m’munsizi, ndipo chongani kabokosi kamene kali pambali pa mfundo iliyonse imene mukuona kuti ikukukhudzani kwambiri.

□ Ndikufuna kudziwa kuti zimakhala bwanji

□ Ndikufuna kuchepetsa nkhawa

□ Ndikufuna ndizigwirizana ndi anzanga

□ Ndikufuna ndichepe thupi

NGATI mwachonga kabokosi kalikonse, ndiye kuti maganizo anu ndi ofananirako ndi anzanu amene amasuta fodya kapena amene anaganizapo zosuta. * Taonani zimene achinyamata ena ananena:

Kufuna kudziwa kuti zimakhala bwanji. “Ndinkafuna kudziwa kuti kodi zimakhala bwanji munthu akasuta fodya, choncho mtsikana winawake atandipatsa ndudu kusukulu, ndinalandira n’kupita panja kukasuta.”—Anatero Tracy.

Kufuna kuchepetsa nkhawa komanso kugwirizana ndi anzanga. “Anzanga a kusukulu ankakonda kunena kuti, ‘Zinthu sizikundiyendera. Ndikungofuna n’tasuta.’ Kenako akasuta ankati, ‘Eya! Ndikumva bwino tsopano.’ Kenako nanenso ndikakhala ndi nkhawa, ndinkangofuna kusuta.”—Anatero Nikki.

Kufuna kuchepa thupi. “Atsikana ena amasuta fodya kuti asanenepe. N’zophweka kwambiri kusiyana ndi kusala zakudya.”—Anatero Samantha.

Koma musanayambe kusuta kapena kupitiriza kusuta, yambani kaye mwaganiza bwino. Musakhale ngati nsomba imene ikufuna kudya nyambo yomwe ili kumbedza. N’zoona kuti nsombayo ikhoza kumva kukoma itadya nyamboyo, koma mapeto ake ikhoza kufa. Choncho, tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti muzigwiritsira ntchito “mphamvu zanu zotha kuganiza bwino.” (2 Petulo 3:1) Tayankhani mafunso otsatirawa.

Kodi Zimene Mukudziwa Zokhudza Kusuta Fodya N’zolondola?

Nenani ngati mfundo zili m’munsizi zili zoona kapena zabodza.

a. ․․․ Kusuta kumachepetsa nkhawa.

b. ․․․ Ndikhoza kutulutsa pafupifupi utsi wonse umene ndasuta.

c. ․․․ Kusuta sikungawononge thanzi langa panopa.

d. ․․․ Kusuta kungachititse kuti anyamata kapena atsikana azindifuna.

e. ․․․ Kusuta kumawononga thanzi langa basi, osati la munthu wina.

f. ․․․ Kaya ndikusuta kapena ayi, Mulungu alibe nazo ntchito.

Mayankho

a. Kusuta kumachepetsa nkhawa.—Zabodza. Ngakhale kuti kusuta kumamuthandiza kwakanthawi munthu amene akuvutika ndi nkhawa chifukwa choti wasiya kusuta, asayansi apeza kuti mankhwala amene amapezeka mu fodya amawonjezera nkhawa.

b. Ndikhoza kutulutsa pafupifupi utsi wonse umene ndasuta.—Zabodza. Pa kafukufuku wina, anapeza kuti munthu akamasuta, pafupifupi 80 peresenti ya utsi wonse umene akusutawo umatsalira m’thupi.

c. Kusuta sikungawononge thanzi langa panopa.—Zabodza. Ngakhale kuti n’zoona kuti thanzi lanu limawonongeka kwambiri mukasuta kwa nthawi yaitali, pali zinthu zina zimene zimasokonekera m’thupi mwanu ngakhale mutangoyamba kumene kusuta. Mwachitsanzo, anthu ena amalephera kusiya kusuta ngakhale atangosuta ndudu imodzi yokha. M’mapapo mwanu simulowa mpweya wokwanira ndiponso mumayamba kudwala chifuwa chosatherapo. Khungu lanu limachita makwinya ambiri ndiponso limakalamba msanga. Kusuta kumachititsa kuti munthu akhale ndi mavuto okhudza kugonana, kuti nthawi zina azichita mantha kwambiri ndi zinthu zinazake, komanso kuti azivutika maganizo.

d. Kusuta kungachititse kuti anyamata kapena atsikana azindifuna.—Zabodza. Munthu wina wochita kafukufuku, dzina lake Lloyd Johnston, anapeza kuti nthawi zambiri “anyamata kapena atsikana sakopeka” ndi munthu wosuta.

e. Kusuta kumawononga thanzi langa basi, osati la munthu wina.—Zabodza. Utsi wochokera ku fodya amene munthu wina akusuta umapha anthu masauzande ambiri chaka chilichonse. Utsi umenewu ukhoza kudwalitsa kapena kupha achibale anu ndiponso anzanu.

f. Kaya ndikusuta kapena ayi, Mulungu alibe nazo ntchito.—Zabodza. Anthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu ayenera kuchotsa “chinthu chilichonse choipitsa thupi.” (2 Akorinto 7:1) N’zosachita kufunsa kuti kusuta kumaipitsa thupi. Mukasankha dala kuipitsa thupi lanu, kudzidwalitsa nokha komanso kudwalitsa ena chifukwa cha fodya, simungakhale bwenzi la Mulungu.—Mateyu 22:39; Agalatiya 5:19-21.

Kodi Mungakane Bwanji Kusuta Fodya?

Choncho, kodi mungatani ngati wina atakupatsani fodya kuti musute? Kuyankha mwachidule koma mwamphamvu kungakuthandizeni. Mwachitsanzo, munganene kuti, “Ayi, pepani sindisuta.” Ngati munthuyo akukukakamizani kapenanso kukunyozani, musadandaule chifukwa muli ndi ufulu wochita zimene mukufuna. Mukhoza kumuuza kuti:

● “Nditafufuza kuopsa kwa fodya, ndasankha kuti ndisamasute.”

● “Ndili ndi zochita zambiri m’tsogolomu ndipo kuti ndizikwaniritse ndikufunika kuti ndikhale ndi moyo wathanzi.”

Komabe, mofanana ndi achinyamata amene tawagwira mawu kumayambiriro kwa nkhaniyi, mungaone kuti maganizo ofuna kusuta sachokera kwa wina koma kwa inuyo. Ngati zili choncho, kuganizira mafunso otsatirawa kungakuthandizeni.

● Kodi kusuta kuli ndi phindu lina lililonse kwa ine? Mwachitsanzo, ngati ndimafuna kusuta chifukwa chongofuna kuti anzanga azindikonda, kodi angamandikondedi ngakhale ngati sitigwirizana pa zinthu zinanso? Kodi ndingafunedi kugwirizana ndi anthu amene amafuna kuti ndiwononge thanzi langa?

● Kodi kusuta kungamandiwonongere ndalama zochuluka bwanji? Nanga kungakhudze bwanji thanzi langa komanso ulemu umene anthu amandipatsa?

● Kodi m’pomveka kuwononga ubwenzi wanga ndi Yehova chifukwa chofuna kusuta?

Koma ngati munayamba kale kusuta, kodi mungatani kuti musiye?

Zimene Mungachite Kuti Musiye Kusuta

1. Mutsimikize kuti mukufunadi kusiya. Lembani zifukwa zosiyira, ndipo muziona zifukwazo nthawi ndi nthawi. Kufuna kukhala woyera pa maso pa Mulungu, n’chifukwa chachikulu chosiyira kusuta.—Aroma 12:1; Aefeso 4:17-19.

2. Pemphani thandizo. Ngati mwakhala mukusuta mobisa, inoyo ndi nthawi yabwino youza ena kuti akuthandizeni. Auzeni kuti mwakhala mukubisa zoti mumasuta koma tsopano mukufuna kusiya ndipo mukufuna kuti akuthandizeni. Ngati mukufuna kutumikira Mulungu, m’pempheni kuti akuthandizeni.—1 Yohane 5:14.

3. Dziikireni tsiku losiyira. Mudzipatse milungu iwiri kapena kuchepera pamenepa yoti mudzasiye kusuta, ndipo mulembe deti limene mukufuna kusiyalo pakalendala yanu. Uzani achibale anu ndiponso anzanu kuti mukusiya pa tsiku limenelo.

4. Fufuzani ndi kutaya chilichonse chimene mumagwiritsira ntchito posuta. Tsiku limene mukufuna kusiyalo lisanafike, fufuzani bwinobwino m’chipinda mwanu, m’galimoto, ndi m’zovala zanu kuti muone ngati muli ndudu zilizonse. Mukazipeza muzitaye. Mutayenso zoyatsira fodya, machesi, ndi motayira phulusa la fodya.

5. Pezani njira yopiririra ululu umene umabwera munthu akangosiya kusuta. Muzimwa madzi ambiri kapena madzi a zipatso, ndipo muzigona mokwanira. Musaiwale kuti ululu uliwonse umene mungamve panopa ndi wakanthawi, koma zidzakupindulirani mpaka kalekale.

6. Pewani zinthu zimene zingakuchititseni kuyambiranso kusuta. Pewani malo komanso zochitika zimene zingakukopeni kuti musute. Mwina mungafunikenso kusiya kucheza ndi anzanu amene amasuta.—Miyambo 13:20.

7. Pewani zodzikhululukira. Musadzinyenge poganiza kuti, “Ndingosuta kamodzi kokha.” Maganizo onyenga ngati amenewa nthawi zambiri amachititsa kuti munthu ayambirenso kusuta.—Yeremiya 17:9.

Ena Asakupusitseni

Chaka chilichonse, makampani opanga fodya amawononga ndalama mabiliyoni ambiri potsatsa malonda. Iwo amadziwa kuti achinyamata ambiri akopeka ndi malonda awowo n’kuyamba kusuta, ndipo akatero adzakhala makasitomala awo mpaka kalekale.

Koma musalole kuti akuluakulu a makampani a fodya akubereni ndalama zanu. Musakodwe ndi nyambo yawo. Iwo, komanso anzanu osuta fodya, sakufunirani zabwino. M’malo momvera anthu amenewa, mverani malangizo a m’Baibulo n’cholinga choti “zinthu zikuyendereni bwino.”—Yesaya 48:17.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ngakhale kuti nkhani ino ikukhudza anthu amene amasuta fodya, ingathandizenso anthu amene amatafuna fodya chifukwa kuipa kwake n’kofanana.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 27]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Munthu akandifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani susuta fodya?’ ndinkamuyankha kuti, ‘Chifukwa sindifuna kuwononga mapapo anga n’kufupikitsa moyo wanga.’

Munthu akafuna kundipatsa fodya, ndinkamuyankha kuti, ‘Ayi, sindikufuna.’ Akandiumiriza ndinkamuuza kuti, ‘Ndi ufulu wanga kukana kusuta fodya. Nthawi youmirizana kuchita zinthu inapita kalekale.’

[Zithunzi]

Benjamin

Heather

[Bokosi patsamba 28]

KODI MUKUDZIWA?

Fodya wopanda utsi, monga amene anthu amatafuna, ali ndi mankhwala akupha ambiri kuposa ndudu. Fodya ameneyu ali ndi mankhwala osiyanasiyana okwana 25 oyambitsa khansa, amene amachititsa kuti zikhale zosavuta kwa munthu kudwala khansa yapakhosi ndi yam’kamwa.

[Chithunzi patsamba 28]

FUNSANI MAKOLO ANU

N’zosavuta kupewa kutengera zimene anzanu akuchita ngati mwakonzekera bwino. Bwanji osafunsa makolo anu kuti muyesezere nawo, kuti mudzakhale wokonzeka kuyankha ngati wina atakupatsani fodya kuti musute? Poyesezerapo, kholo lanu likhale ngati mnzanu wina amene akukukakamizani kusuta. Zokuthandizani: Gwiritsirani ntchito gawo lakuti “Mmene Mungakonzekerere” patsamba 132 ndi 133 m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, kuti mupeze njira zina zabwino zoyankhira.

[Chithunzi patsamba 28]

Mofanana ndi nsomba imene ikufuna kudya nyambo, munthu wosuta fodya amasangalala kwa kanthawi kochepa koma akhoza kufa