Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinapangidwa Modabwitsa’

Tinapangidwa Modabwitsa’

Tinapangidwa Modabwitsa’

MUKAGANIZIRA zinthu zodabwitsa zimene nyama zosiyanasiyana zimachita, kodi nthawi zina mumasirira? Mwina mumafuna mutakhala katswiri wodziwa kuuluka ngati mbalame, wodziwa kusambira ngati nsomba, wotha kuona patali ngati chiwombankhanga ndiponso wodziwa kuthamanga ngati kambuku.

Koma si nyama zokha zimene zimachita zinthu zodabwitsazi. Anthufenso timachita zinthu zogometsa. Tili ndi nzeru zotha kutulukira zinthu zatsopano, timatha kuganizira zinthu zoti sitinayambe tazionapo komanso tili ndi chidwi chophunzira zinthu zatsopano nthawi zonse. N’chifukwa chake anthu amatha kupanga makina komanso zinthu zosiyanasiyana zimene zimawathandiza kukwanitsa kuchita pafupifupi chilichonse. Zinthu zimene anthu amapanga, zimawathandiza kuyenda pa liwiro la mtondo wodooka m’mlengalenga, kuwoloka nyanja zikuluzikulu, kuona kutali kwambiri m’mlengalenga, kuona tinthu ting’onoting’ono kwambiri ta mkati mwa maselo, komanso kupanga mankhwala ndiponso zipangizo zopezera ndi kuchizira matenda osiyanasiyana.

Ngakhale popanda kugwiritsa ntchito chipangizo chilichonse, anthu amatha kuchita zinthu zodabwitsa malinga ngati ali ndi thanzi labwino komanso ngati aphunzitsidwa bwino. Mwachitsanzo, pamipikisano ya masewera a Olympic, anthu amachita zinthu zodabwitsa kwambiri ndi thupi lawo monga kudumpha m’mwamba, kusambira, ndi kuchita masewera ena ambiri ogometsa. Masewera amenewa amafuna mphamvu, luso komanso nzeru.

Mwina inuyo simungakwanitse kuchita zinthu zimene akatswiri ochita masewera a Olympic amachita, komabe payenera kuti pali zinthu zina zimene mumakwanitsa kuchita. Kodi mumathokoza Mulungu chifukwa cha zinthu zimenezi? Munthu wina amene analemba nawo Baibulo analemba nyimbo yoyamikira Mulungu chifukwa cha zimene iye ankakwanitsa kuchita. Iye anaimba kuti: “Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa.” * (Salimo 139:14) Mungachite bwino kuganizira mawu amenewa pamene mukuwerenga nkhani zotsatirazi. Nkhani zimenezi zifotokoza mwatsatanetsatane kudabwitsa kwa thupi lathu komanso makhalidwe amene amachititsa kuti anthufe tikhale apadera kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Ngati muli ndi chidwi chofuna kudziwa ngati zinthu zinachita kulengedwa kapena kusanduka, mungawerenge kabuku ka m’chingelezi kakuti Was Life Created? ndiponso kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking. Mungapeze timabuku timeneti kwa Mboni za Yehova za kwanuko kapena kwa ofalitsa a magazini ino.

[Bokosi patsamba 3]

ANTHU SAGWIRITSA NTCHITO MPHAMVU ZAMBIRI AKAIMIRIRA

Mosiyana ndi nyama, anthufe tinapangidwa moti tizitha kuimirira popanda kugwiritsa ntchito mphamvu zambiri. Malinga ndi zimene katswiri wina wa mmene ubongo wathu umagwirira ntchito, dzina lake John R. Skoyles, ananena, ‘timangofunika kuwonjezera mphamvu pang’ono kuti tiimirire, mwina 7 peresenti yokha kuposa mphamvu zimene timagwiritsa ntchito tikakhala pansi.’ Iye anawonjezera kuti galu amafunika mphamvu zambiri kuti aimirire (ndi miyendo inayi), mwina pafupifupi 70 peresenti kuposa mphamvu zimene amagwiritsa ntchito akagona.