Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Anthu Azindikonda Ndikangokumana Nawo Koyamba?

Kodi Ndingatani Kuti Anthu Azindikonda Ndikangokumana Nawo Koyamba?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Anthu Azindikonda Ndikangokumana Nawo Koyamba?

“Ndikukhulupirira kuti andilemba ntchito basi. Bwana amene akundifunsa mafunsoyu akuchita kudziwa kuti ndilibe mantha. Chilowereni mu ofesi mwake ndakhala ndikumutchula ndi dzina lake loyamba. Ndikuona kuti ntchito ndiyamba basi.”

“Sindikukhulupirira kuti mnyamata amene anatumiza CV yake yabwino kwambiri uja ndi ameneyu. Sindingayerekeze n’komwe kumulemba ntchito. Ngati akuchita zimenezi asanayambe ntchito, kuli bwanji akadzayamba?”

Onani chithunzichi ndipo werengani mawu amene ali pamwambawo. Kodi mungatchule zinthu zitatu zimene mnyamatayo akuchita zomwe zingapangitse bwanayo kuti asamukonde?

1 ․․․․․

2 ․․․․․

3 ․․․․․

● Mayankho ali pansipa

1. Mnyamatayo sanavale zovala zoyenera. 2. Akutchula bwanayo ndi dzina lake loyamba ngati kuti anadziwana kale. 3. Zimene akuchita pampandopo zikusonyezeratu kuti ndi wopanda ulemu.

NGATI mukulawa chakudya chinachake chimene simunayambe mwachidyapo, kodi zimakutengerani nthawi yaitali bwanji kuti mudziwe kuti chakudyacho n’chokoma? Mukangoika chakudyacho m’kamwa, nthawi yomweyo mumadziwa kuti chakudyacho n’chokoma kapena ayi.

Zimenezi n’zimenenso zimachitika mukangokumana ndi munthu winawake koyamba. Pasanapite nthawi yaitali mumadziwa kuti munthuyo ndi wotani. Koma dziwani kuti pa nthawi imeneyonso munthu winayo amadziwa kuti inuyo ndi wotani.

Kodi mukufuna kupeza ntchito, munthu wocheza naye kapena woti n’kumanga naye banja? Zimene mungachite mukangokumana koyamba ndi bwana kapena munthu winayo ndi zimene zingachititse kuti ayambe kukukondani kapena kudana nanu. Tiyeni tione zinthu zingapo zimene mutazitsatira zingakuthandizeni kuti anthu azikukondani mukakumana nawo koyamba.

1. Maonekedwe Anu

Chinthu choyamba chimene anthu amachita nacho chidwi mukangokumana nawo ndi maonekedwe anu. Anthu ena amanyalanyaza mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Clarissa * ananena kuti: “Masiku ano ukapita ku lesitilanti, umaona anthu atavala zosalongosoka ngati kuti sakupita kugulu kwa anthu.”

Muyenera kuvala zovala zogwirizana ndi malo amene mukupita. Zovala zimene mungavale kumpira sizingakhale zofanana ndi zimene mungavale popita kokafunsira ntchito. Koma kodi mungadziwe bwanji zovala zogwirizana ndi malo amene mukupita? Chinsinsi chake n’chakuti musamavale motayirira. Ngati mukukaikira kuti zovala zimene mwavala zingakhumudwitse anthu ena, sinthani n’kuvala zina.

KUMBUKIRANI IZI: Zovala zanu zimasonyeza kuti ndinu munthu wotani.

“Ndikaona anthu pagulu amene sanavale bwino, sindimafuna kucheza nawo. Zovala zawozo zimangosonyezeratu kuti si anthu abwino.”​—Anatero Diane

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizivala “zovala zoyenera” zosonyeza kuti ndife anthu ‘aulemu ndi anzeru.’​—1 Timoteyo 2:9.

Dzifunseni kuti: “Kodi ineyo ndimavala zovala zoyenera kapena ndimangovala chilichonse? Kodi munthu amene akufuna kundilemba ntchito kapena anzanga ena anganene kuti zimene ndimavala zimasonyeza kuti ndine munthu ‘wanzeru’?”

Yesani izi: Funsani munthu wina amene mumamudalira kuti akuuzeni ngati mumavala moyenera.

2. Zolankhula Zanu

Zimene mumalankhula zimasonyeza ngati muli wodzichepetsa kapena wodzitukumula, komanso ngati muli wodekha kapena wopupuluma. Choncho muzisamala ndi zolankhula zanu, makamaka ngati mukulankhula ndi mnyamata kapena mtsikana amene mumafuna mutadzamanga naye banja. Mtsikana wina, dzina lake Valerie, anati: “Zimandikwana ndikamalankhulana ndi mnyamata n’kuona kuti akungolankhula zimene iyeyo amachita. Ndiye pali anyamata enanso oti amafuna adziwe chilichonse chokhudza iweyo nthawi yomweyo. Atsikana ambiri sasangalala ndi zimenezi chifukwa amaona kuti mnyamatayo akuwapanikiza.”

KUMBUKIRANI IZI: Anthu ena amadziwa zimene zili mumtima mwanu kuchokera pa zimene mumalankhula. Choncho muzionetsetsa kuti mukulankhula zinthu zosangalatsa.

“Ndimasangalala ndi mnyamata amene amachita zinthu mwachibadwa. Ngati mnyamata akutenga nthawi kuganizira zoti anene, ndimadziwa kuti zimene akufuna kunenazo si zochokera mumtima.”​—Anatero Selena.

Baibulo limati: “Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa, koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.”​—Miyambo 10:19.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndingatani kuti ndisamangokhala phe, kapena kuti ndisamalankhule kwambiri? Kodi anthu ena amakhumudwa ndi mmene ndimalankhulira?’

Yesani izi: Onani mmene anthu amene amadziwa kucheza bwino ndi anthu amachitira. Kodi amachita chiyani kuti azilankhula bwino ndi anthu? Kodi mungakwanitse kutsanzira zimene amachitazo?

3. Zochita Zanu

Anthu amaona kwambiri zimene timachita kuposa zimene timalankhula. Mwachitsanzo, ngati ndinu waulemu, zochita zanu zimasonyeza kuti mumalemekeza ena. Kuzindikira mfundo imeneyi kungakuthandizeni ngati mukufuna kupeza mnzanu woti mudzamange naye banja. Mtsikana wina dzina lake Carrie, ananena kuti: “Mungasonyeze kuti mumamulemekeza munthu winayo pomuchitira tinthu ting’onoting’ono monga kumutsegulira chitseko. Zina zimene mungachite ndi zoti mukhoza kungoona nokha.”

KUMBUKIRANI IZI: Zochita zanu zili ngati chikwangwani chosonyeza zimene zili mumtima mwanu. (Miyambo 20:11) Kodi zochita zanu zimawasonyeza anthu ena kuti ndinu munthu wotani?

“Ndimaona kuti ndi bwino kwambiri kumvetsera anthu ena akamalankhula. Sibwino kuwadula anthu ena mawu, pokhapokha ngati patakhala chifukwa chomveka.”​—Anatero Natalia.

Baibulo limanena kuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”​—Luka 6:31.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine munthu waulemu? Kodi ndimachita zinthu zosonyeza kuti ndimaganizira ena? Kodi ndine wodalirika? Kodi ndimasunga nthawi?’

Yesani izi: Mukapangana ndi munthu kuti mupezane nthawi inayake, yesetsani kunyamuka mwamsanga n’cholinga chakuti ngati mutachedwa m’njira mukafikebe panthawi yake. Mukamakakumana koyamba musam’patse munthu winayo maganizo oti ndinu wosasunga nthawi.

Chenjezo: Musamachite zinthu zachinyengo kapena zachiphamaso n’cholinga choti anthu akukondeni. (Salimo 26:4) M’malomwake ganizirani za makhalidwe amene mukufuna kuti muzidziwika nawo ndiyeno muziyesetsa kuwatsatira tsiku ndi tsiku. (Akolose 3:9, 10) Dziwani kuti ndi ufulu wanu kusankha makhalidwe amene mukufuna kukhala nawo. Kumbukirani kuti maonekedwe anu, zolankhula zanu, komanso zochita zanu zingachititse kuti anthu ayambe kukukondani kapena kudana nanu.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 27]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Pamafunika kusankha bwino anthu ocheza nawo. Ineyo sindichedwa kutengera zochita za anzanga, choncho ndimaonetsetsa kuti ndikusankha anthu amene ndingakonde kutengera zochita zawo.”

“Kuti munthu uzicheza bwino ndi anthu suchita kufunikira kukhala wokongola kapena wandalama zambiri. Chifukwatu zimangochitika kuti munthu ukhale ndi zinthu zimenezi. Koma khalidwe labwino ndiye lofunikira kwambiri, chifukwa umachita kusankha kukhala ndi khalidwe labwino kapena loipa.”

[Zithunzi]

Sier

Ashley

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

ZINTHU ZIMENE ZINGACHITITSE KUTI ENA AKUKONDENI

● Kumwetulira

● Mukamapereka moni, mugwireni munthu winayo dzanja mwamphamvu (koma osati mpaka kumuthyola mafupa)

● Muzikhala aukhondo

● Muzimuyang’ana munthu winayo mwaulemu

[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]

MUSACHITE ZINTHU MONYANYIRA

Muzilankhula KOMA musamangolankhula nokha

Muzifunsa mafunso KOMA musamakakamire kuti akuyankheni

Muzimasuka KOMA musachite zinthu zomukopa

Muzidzidalira KOMA musamachite matama

[Bokosi patsamba 28]

FUNSANI MAKOLO ANU

Inuyo muli wachinyamata, kodi munkatani kuti anthu azikukondani mukakumana nawo koyamba?

․․․․․