Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Malo Ochezera a pa Intaneti?—Gawo 1

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Malo Ochezera a pa Intaneti?—Gawo 1

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Malo Ochezera a pa Intaneti?—Gawo 1

“Ndili ndi anzanga m’mayiko osiyanasiyana, ndipo ndimaona kuti njira yabwino kwambiri yolankhulana nawo ndi kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. Ndimacheza nawo pafupipafupi ngakhale kuti ali kutali kwambiri.”—Anatero Sue, wazaka 17. *

“Kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti n’kungowononga nthawi. Ndimaona kuti kucheza ndi anzako pamasom’pamaso ndiye kofunika kwambiri.”—Anatero Gregory, wazaka 19.

KODI pa achinyamata awiriwa, ndi uti amene mukugwirizana naye? Kaya maganizo anu ndi otani, mfundo yosatsutsika ndi yakuti: Masiku ano anthu ambiri akugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. * Taganizirani izi: Zinatenga zaka 38 kuti wailesi iyambe kugwiritsidwa ntchito ndi anthu 50 miliyoni, ndipo zinatenga zaka 13 kuti anthu ochuluka chonchi ayambe kugwiritsa ntchito TV, ndiponso zinatenga zaka zinayi kuti anthu ochulukanso chonchi ayambe kugwiritsa ntchito Intaneti. Koma zinangotenga chaka chimodzi chokha kuti anthu 200 miliyoni ayambe kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti a Facebook.

Lembani ngati chiganizo chotsatirachi chikunena zoona kapena zabodza:

Achinyamata osakwanitsa zaka 25 ndi amene amagwiritsa ntchito kwambiri malo ochezera a pa Intaneti. ․․․․․ Zoona ․․․․․ Zabodza

Yankho: Zabodza. Pafupifupi anthu awiri pa anthu atatu alionse amene amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti ndi azaka 25 kapena kupitirira. M’chaka cha 2009, anthu ambiri amene anayamba kugwiritsa ntchito malowa anali opitirira zaka 55.

Komabe achinyamata mamiliyoni ambiri amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti amenewa, ndipo ena amaona kuti ndi njira yabwino kwambiri yochezera ndi anzawo. Mtsikana wina dzina lake Jessica ananena kuti: “Nthawi ina ndinatseka malo anga a pa Intaneti koma kenako ndinawatsegulanso chifukwa ndinaona kuti palibe aliyense amene ankacheza nane pondiimbira foni. Ndaona kuti ngati munthu sugwiritsa ntchito malowa, anzako amakuiwala.”

Kodi n’chiyani chimachititsa anthu ambiri kuti azikonda malo amenewa? Yankho lake ndi losavuta: Anthufe mwachibadwa timafuna kucheza ndi anthu ena. Ndipo malo ochezera a pa Intaneti amakwaniritsa cholinga chimenechi. Taonani zifukwa zina zimene zingachititse anthu ambiri kukhala ndi malo ochezera a pa Intaneti.

1. Ndi njira yachangu.

“N’zovuta kumalankhulana ndi anzako nthawi zonse, koma ngati anzakowo ungawapeze pamalo amodzi, zimakhala zosavuta.”—Anatero Leah, wazaka 20.

“Ndikalemba zinazake pamalo anga a pa Intaneti, ndimakhala ngati kuti ndalembera anzanga onse nthawi imodzi.”—Anatero Kristine, wazaka 20.

2. Kutengera anzawo.

“Nthawi zambiri anzanga amandiuza kuti ndiyambe kucheza ndi anthu amene iwo amacheza nawo, koma ndimalephera kuchita zimenezi chifukwa chakuti ndilibe malo ochezera a pa Intaneti. Choncho ndimaona kuti ndiyenera kukhala ndi malowa.”—Anatero Natalie, wazaka 22.

“Ndikawauza anthu kuti ndinasankha kuti ndisakhale ndi malo ochezera a pa Intaneti, amadabwa kwambiri, ndipo amandiyang’ana ngati anena kuti, ‘Vuto lako n’chiyani?’”—Anatero Eve, wazaka 18.

3. Zimene olemba ndi oulutsa nkhani amanena.

“Olemba ndi oulutsa nkhani amalimbikitsa maganizo akuti ngati ulibe malo ochezera a pa Intaneti ndiye kuti sungakhale ndi anzako. Ndipo ngati ulibe anzako ndiye kuti ndiwe wotsalira. Choncho, ngati ulibe malo ochezera a pa Intaneti, ndiwe wopanda phindu.”—Anatero Katrina, wazaka 18.

4. Sukulu.

“Aphunzitsi anga amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. Nthawi zina amagwiritsa ntchito malo amenewa akafuna kutidziwitsa kuti kuli mpikisano woyankha mafunso. Nthawi zinanso ngati sindinamvetse samu inayake, ndimangowatumizira uthenga wowafotokozera zimenezi ndipo iwo amandithandiza.”—Anatero Marina, wazaka 17.

5. Ntchito.

“Anthu amene akufunafuna ntchito amalumikizana ndi anzawo kudzera pa malo ochezera a pa Intaneti. Nthawi zina zimenezi zimawathandiza kuti apeze ntchito.”—Anatero Amy, wazaka 20.

“Malo ochezera a pa Intaneti amandithandiza kwambiri pa ntchito yanga yojambula chifukwa anthu amatha kuona pamalowa zithunzi zimene ndajambula.”—Anatero David, wazaka 21.

Kodi mukuona kuti mukufunikira kukhala ndi malo ochezera a pa Intaneti? Ngati mudakali pakhomo pa makolo anu, iwo ndi amene ali ndi udindo wokusankhirani ngati mukufunikira kukhala ndi malowa kapena ayi. * (Miyambo 6:20) Choncho, ngati makolo anu akuona kuti simukufunikira kukhala ndi malowa, muyenera kuwamvera.—Aefeso 6:1.

Komabe, makolo ena amalola ana awo okhwima maganizo kukhala ndi malowa ndipo amaona mmene akuwagwiritsira ntchito. Ngati makolo anu amaona mmene mukuwagwiritsira ntchito, kodi ndiye kuti akukuphwanyirani ufulu wanu? Ayi. Ngakhale kuti malowa ndi othandiza, ngati mutamawagwiritsa ntchito molakwika akhoza kukhala oopsa. Ndiye ngati makolo anu anakulolani kukhala ndi malo amenewa, kodi mungatani kuti mupewe mavuto?

Muziwagwiritsa Ntchito Moyenerera

Kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti tingakuyerekezere ndi kuyendetsa galimoto. Mwina mukudziwa kuti si onse amene ali ndi laisensi amene amayendetsa bwino galimoto, ndipotu anthu ambiri okhala ndi laisensi achitapo ngozi zoopsa chifukwa choyendetsa mosasamala.

N’chimodzimodzinso ndi kugwiritsa ntchito Intaneti. Ena amaigwiritsa ntchito mosamala ndipo ena mosasamala. Ngati makolo anu anakulolani kukhala ndi malo anu a pa Intaneti, ndiye kuti akukudalirani kuti muziwagwiritsa ntchito mwanzeru. Kodi inuyo mumawagwiritsa ntchito bwanji malo amenewa? Kodi mumachita zinthu mwanzeru ndiponso moganiza bwino?—Miyambo 3:21.

M’nkhani ino tikambirana zinthu ziwiri zofunika kuziganizira mofatsa. Zinthu zake n’zokhudza zinthu zachinsinsi zimene simufunika kuika pa Intaneti komanso kuchuluka kwa nthawi imene mumakhala pa Intaneti. Nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” ya m’magazini yotsatira idzafotokoza mmene malo ochezera a pa Intaneti amakhudzira mbiri yanu komanso anzanu amene mumapeza.

MUSAMAIKEPO ZINTHU ZACHINSINSI

Pogwiritsa ntchito malo amenewa, kodi mumaganizira zinthu zachinsinsi zimene simufunikira kuikapo? Mwina mungaganize kuti kuika zinthu zimenezo pa Intaneti kulibe vuto chifukwa cholinga cha malo amenewo ndi chakuti anthu akudziweni. Komabe, ngati mutapanda kusamala, zimenezi zikhoza kukupezetsani mavuto.

Taganizirani kuti muli ndi ndalama zambiri ndipo mukuyenda m’tawuni ndi anzanu. Kodi mungaike ndalamazo poyera kuti aliyense azione? Kuchita zimenezi kungakhale kupanda nzeru chifukwa mukhoza kuberedwa. Munthu wanzeru angaike ndalama zake pamalo amene anthu ena sangazione.

N’chimodzimodzinso ndi zinthu zanu zachinsinsi. Zili ngati ndalama zomwe zimafuna kuzisunga mosamala. Ndi mfundo imeneyi, taonani zinthu zimene zili m’munsizi ndipo chongani zimene simungafune kuti munthu wina aliyense adziwe.

․․․․․ kumene ndimakhala

․․․․․ adiresi yanga ya imelo

․․․․․ sukulu imene ndimaphunzira

․․․․․ nthawi imene ndimapezeka pakhomo

․․․․․ nthawi imene panyumba pathu sipakhala munthu

․․․․․ zithunzi zanga

․․․․․ maganizo anga pa nkhani inayake

․․․․․ zimene ndimakonda ndi zimene ndimadana nazo

Ngakhale kuti mwina ndinu munthu womasuka kwambiri, mungavomereze kuti zina mwa zinthu zimene zili pamwambazi sizifunika kumangouza kapena kuonetsa aliyense. Komabe, achinyamata ambiri ngakhalenso achikulire ena, amaulula kwa aliyense zinthu zachinsinsi zokhudza iwowo popanda kuganizira kuopsa kwake. Kodi mungapewe bwanji kuchita zimenezi?

Ngati makolo anu amakulolani kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, muyenera kudziwa bwino zimene mungachite kuti zinthu zimene mwaika pamalowa zisamangoonedwa ndi aliyense. Musamangosiyira udindo umenewu kampani imene inakhazikitsa malowa kuti izikutetezerani zinthu zanu. Dziwani kuti malowa amatha kupangidwa moti anthu ambiri akhoza kuona zimene zaikidwapo komanso kulemba ndemanga zawo. Chimenechi n’chifukwa chimodzi chimene chinachititsa mtsikana winawake, dzina lake Allison, kusintha zina ndi zina pa pamalo ake ochezera a pa Intaneti kuti malo akewo azionedwa ndi anthu ochepa okha. Iye anati: “Anzanga ena analinso ndi anzawo amene sindinkawadziwa, ndipo sindinkafuna kuti anthu amenewa aziwerenga zinthu zokhudza ineyo.”

Ngakhale ngati malo anu ochezera a pa Intaneti amaonedwa ndi anzanu ochepa chabe, muyenerabe kusamala. Mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Corrine, anati: “Nthawi zina ungakomedwe n’kuwerenga zimene anzako alemba, ndipo kenako iwenso ungayambe kulemba zinthu zambiri zomwe zina zingakhale zachinsinsi.”

Nthawi zonse muzikumbukira kuti pa Intaneti palibe chinsinsi. N’chifukwa chiyani tikutero? Mayi wina dzina lake Gwenn Schurgin O’Keeffe, analemba m’buku lake kuti: “Nthawi zambiri, zimene zimalembedwa pa Intaneti zimasungika pamakompyuta enaake ndipo ngakhale zitachotsedwa, sizichokeratu. Tiyenera kukhala ndi maganizo akuti zilipobe, ndipo kuganiza mosiyana ndi zimenezi n’kudzinamiza.”

NTHAWI IMENE MUMAKHALA PA INTANETI

Si zinthu zachinsinsi zokha zimene tingaziyerekezere ndi ndalama, chifukwa nthawinso ndi ndalama. Choncho, muyenera kugwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru. (Mlaliki 3:1) Ndipotu anthu ambiri amalephera kugwiritsa ntchito Intaneti, kuphatikizapo malo ochezera, mwanzeru moti amawononga nthawi yambiri. *

“Nthawi zambiri ndinkaganiza kuti, ‘Ndingokhala pa Intaneti kwa mphindi imodzi yokha.’ Koma zimapezeka kuti ola limodzi latha ndikadali pa Intaneti pomwepo.”—Anatero Amanda, wazaka 18.

“Ndikakhala pa Intaneti, sindinkafuna kuchokapo. Tsiku lililonse ndikaweruka kusukulu, ndinkangofikira pa Intaneti ndipo ndinkakhalapo nthawi yaitali. Ndinkawerenga zimene anthu ena alemba zokhudza zinthu zimene ndinaika pamalo anga komanso kuona zimene iwowo aika pamalo awo.”—Anatero Cara, wazaka 16.

“Ndinkatha kulowa pa malowa pogwiritsa ntchito foni yanga nthawi iliyonse, kaya ndikupita kusukulu, ndili kusukulu kapena ndikamabwerera kunyumba. Ndiyeno ndikangofika kunyumba ndinkafikira pa kompyuta. Ndinkadziwa kuti ndazolowera zachabe koma sindinkafuna kusiya.”—Anatero Rianne, wazaka 17.

Ngati makolo anu amakulolani kukhala ndi malo ochezera a pa Intaneti, muzionetsetsa kuti simukukhalapo kwa nthawi yaitali. Muzilemba nthawi imene mumakhala pa Intaneti ndipo potha pa mwezi muziona kuti mwakhalapo nthawi yochuluka bwanji. Nthawi zonse muzikumbukira kuti nthawi ndi ndalama. Choncho musalole kuti malo ochezera a pa Intaneti azikudyerani nthawi yanu. Ndipo dziwani kuti pali zinthu zina pa moyo zimene n’zofunika kwambiri kuposa Intaneti.—Aefeso 5:15, 16; Afilipi 1:10.

Achinyamata ena amene ankathera nthawi yambiri pa Intaneti anasintha. Tamvani zimene ena ananena.

“Nditatseka malo anga ochezera a pa Intaneti, ndinaona kuti ndinali ndi nthawi yambiri. Posachedwapa ndayambanso kugwiritsa ntchito malo angawo, koma ndimayesetsa kudziletsa. Pamatha kupita masiku angapo ndisanapitepo. Nthawi zina ndimachita kuwaiwaliratu. Ndikadzayambiranso kukhala nthawi yaitali pamalo angawa, ndidzangowatsekanso.”—Anatero Allison, wazaka 19.

“Nthawi zina ndimatseka malo anga a pa Intaneti kwa miyezi ingapo, kenako n’kuwatsegulanso. Ndimachita zimenezi ndikaona kuti akundidyera nthawi yanga. Panopa sindikonda kupitapita pa malowa ngati mmene ndinkachitira poyamba. Ndimangowagwiritsa ntchito ndikafuna kuchita zinazake ndipo ndikatero basi ndathana nawo.”—Anatero Anne, wazaka 22.

Zimene Muyenera Kudziwa

Pali chinthu chinanso chofunika kwambiri chokhudza malo ochezera a pa Intaneti chimene muyenera kudziwa. Pofuna kukuthandizani kumvetsa, chongani chonchi ✔ yankho limene mukuona kuti ndi lolondola.

Cholinga chenicheni cha malo ochezera a pa Intaneti ndi

(A) ․․․․․ kuchitirapo bizinezi.

(B) ․․․․․ kucheza ndi anzanu basi.

(C) ․․․․․ kungokusangalatsani.

Kodi mukuganiza kuti yankho lolondola ndi liti? Kaya munachonga liti, dziwani kuti yankho lolondola ndi A. Cholinga chachikulu cha malo amenewa ndi kuchitira bizinezi. Makampani amene amapanga malo amenewa amapeza phindu kwambiri chifukwa amatsatsapo malonda. Malo amene amagwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri ndi amene amawapangira ndalama zambiri. Ndipotu dziwani kuti mukakhala nthawi yaitali pa Intaneti m’pamenenso mumaona malonda ambiri akutsatsidwa.

Kudziwa zimenezi kungakuthandizeni kuzindikira kuti kugwiritsa ntchito malowa nthawi yaitali komanso kuikapo zinthu zanu zambiri, sikungakupindulitseni. Chifukwatu amene amapindula kwambiri ndi makampani amene amatsatsa malondawo. Choncho, ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, muzionetsetsa kuti simukuikapo zinthu zanu zachinsinsi komanso simukukhalapo nthawi yaitali kwambiri.

NKHANI YOTSATIRA YA “ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA” ILI NDI MUTU WAKUTI:

Kodi malo ochezera a pa Intaneti amakhudza bwanji mbiri yanu komanso anzanu amene mumapeza?

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina m’nkhaniyi.

^ ndime 5 Kuti munthu ayambe kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, choyamba amafunika kulembetsa kuti apatsidwe malo akeake, omwe amatha kulembapo komanso kuikapo zinthu zake ngati zithunzi ndi zina zotero. Ndipo kenako amasankha anthu oti azicheza nawo.

^ ndime 24 Galamukani! siilimbikitsa kapena kuletsa anthu kugwiritsa ntchito malo enaake ochezera a pa Intaneti. Akhristu ayenera kuonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito Intaneti popanda kuphwanya mfundo za m’Baibulo.—1 Timoteyo 1:5, 19.

^ ndime 47 Mukafuna kudziwa zambiri, onani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndimagwiritsira Ntchito Foni, TV, Kompyuta Kapena Intaneti Mopitirira Malire?” mu Galamukani! ya January 2011. Onani makamaka bokosi lakuti “Ndinkangokhalira Kucheza pa Intaneti,” lomwe lili patsamba 26.

[Mawu Otsindika patsamba 25]

Zinatenga zaka 38 kuti wailesi iyambe kugwiritsidwa ntchito ndi anthu 50 miliyoni

[Mawu Otsindika patsamba 25]

Koma zinangotenga chaka chimodzi chokha kuti anthu oposa 200 miliyoni ayambe kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti a Facebook

[Bokosi patsamba 27]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kambiranani ndi makolo anu zinthu zokhudza inuyo zimene simufunika kuika pamalo ochezera a pa Intaneti ndiponso chifukwa chake. Kodi ndi zinthu ziti zimene sizifunikira ngakhale pang’ono kuikidwa pa Intaneti? Funsaninso makolo anu kuti akuuzeni zimene mungachite kuti muzithanso kucheza ndi anthu pamasom’pamaso m’malo momangokhala pa Intaneti. Kodi ndi zinthu ziti zimene iwo akuona kuti muyenera kusintha?

[Chithunzi patsamba 26]

Zinthu zimene mumachita pamalo ochezera a pa Intaneti sizikhala zachinsinsi kwenikweni

[Chithunzi patsamba 27]

Nthawi ndi ndalama. Mukaziwonongera pa chinthu chimodzi, mumalephera kugula zinthu zina