Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chipani cha Nazi Chinalephera Kundisintha

Chipani cha Nazi Chinalephera Kundisintha

Chipani cha Nazi Chinalephera Kundisintha

Yosimbidwa ndi Hermine Liska

M’CHAKA cha 1938, Adolf Hitler ndi chipani chake cha Nazi analanda dziko lathu la Austria. Kuyambira nthawi imeneyi, zinthu zinasokonekera pa moyo wanga. Pasanapite nthawi, ine ndi ana asukulu anzanga tinkauzidwa kuti tikamapatsana moni tizinena mawu akuti “Heil Hitler.” Tinkauzidwanso kuti tiziimba nyimbo za chipani cha Nazi komanso kuti tilowe m’gulu la achinyamata a Hitler. Ine ndinkakaniratu kuchita zinthu zimenezi. Ndiloleni kuti ndifotokoze zambiri.

M’banja mwathu tinalimo ana asanu, ndipo wamkazi ndinalipo ndekha komanso ndinali wamng’ono pa onsewo. Banja lathu linali ndi famu ku St. Walburgen, mumzinda wa Carinthia, m’dziko la Austria. Bambo anga anali a Johann Obweger ndipo mayi anga anali a Elisabeth. M’chaka cha 1925, bambo analowa gulu la Ophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinkadziwika nalo pa nthawiyo. Mayi anga anabatizidwa m’chaka cha 1937. Kuyambira ndili mwana, makolo anga ankandiphunzitsa mfundo za m’Baibulo komanso ankandithandiza kuti ndizikonda kwambiri Mulungu ndi chilengedwe chake. Mwachitsanzo, iwo ankandiuza kuti si bwino kulambira anthu. Ankandiuza zimene Yesu Khristu ananena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”—Luka 4:8.

Makolo anga ankakonda kuchereza alendo, moti kunyumba kwathu kunkabwera alendo ambirimbiri. Ngakhalenso anthu ena ogwira ntchito pafamu yathu ankakhala kunyumba kwathu komweko. Ku Carinthia anthu amakonda kwambiri kuimba ndipo ifeyo tinkakonda kukhala pamodzi n’kumaimba komanso kukambirana nkhani za m’Baibulo. Ndimakumbukirabe kuti Lamlungu lililonse m’mawa, banja lathu linkakumana pamodzi n’kumaphunzira Baibulo.

Tinayamba Kukhala Mwamantha

Pa nthawi imene dziko la Germany linalanda dziko la Austria, n’kuti ndili ndi zaka pafupifupi 8. Kuchokera nthawi imeneyi, chipani cha Nazi chinayamba kukakamiza kwambiri anthu kuti azitsatira mfundo zake. Munthu aliyense ankalamulidwa kuti popereka moni azinena kuti, “Heil Hitler.” Ineyo ndinkakana chifukwa mawu akuti “heil” m’Chijeremani amatanthauza “chipulumutso,” ndipo ndinkaona kuti chipulumutso sichingachokere kwa Hitler. Ndinkadziwa kuti Yesu Khristu ndiye Mpulumutsi wathu. (Machitidwe 4:12) Chifukwa chakuti ndinkakana, aphunzitsi komanso ana asukulu anzanga ankakhalira kundinyoza. Tsiku lina ndili ndi zaka 11, mphunzitsi wamkulu wa pasukulu yathu anandiopseza kuti: “Hermine, ubwerera ku sitandade 1. Sindifuna kukhala ndi mwana wamakani chonchi m’kalasi mwanga.”

Popeza kuti ine ndi achimwene anga tinkakanitsitsa kunena kuti “Heil Hitler,” bambo anaitanidwa kuti akaonekere kukhoti. Atafika kumeneko anauzidwa kuti asaine chikalata chosonyeza kuti asiya chipembedzo chawo. Chikalatacho chinkafunanso kuti munthu avomereze kuti azilera ana ake motsatira mfundo za chipani cha Nazi. Iwo anakana kusaina, ndipo chifukwa cha zimenezi, bambo ndi mayi anga anauzidwa kuti alibe ufulu wolera ana awofe. Choncho, ineyo ndinatumizidwa kumalo ophunzitsira ana mfundo za chipani cha Nazi, omwe anali pa mtunda wa makilomita 40 kuchokera kunyumba kwathu.

Nditangokhala nthawi yochepa kumalowa, ndinayamba kulakalaka kunyumba, moti ndinkangokhalira kulira. Pa nthawiyi aboma ankayesetsa kundikakamiza kuti ndilowe m’gulu la achinyamata a Hitler, koma anandilephera. Atsikana ena ankayesetsa kukweza mkono wanga m’mwamba kuti ndichitire sawatcha mbendera ya Nazi, koma ankalephera. Ndinkamva ngati atumiki a Mulungu akale amene anati: “Sitingayerekeze kusiya Yehova, kuti tizitumikira milungu ina.”—Yoswa 24:16.

Makolo anga sankaloledwa kudzandiona. Komabe nthawi zina ankandipeza kusukulu kapena tinkakumana m’njira ndikamapita kusukulu. Ngakhale kuti tinkacheza nthawi yochepa kwambiri, zimene ankandiuza zinandithandiza kuti ndipitirize kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Pa nthawi ina nditakumana ndi bambo, anandipatsa Baibulo laling’ono, limene ndinkalibisa pansi pa bedi. Ndinkakonda kwambiri kuliwerenga ngakhale kuti ndinkachita zimenezi mobisa. Tsiku lina ndinangotsala pang’onong’ono kugwidwa, koma ndinalibisa msangamsanga m’bulangete.

Ananditumiza Kusukulu ya Akatolika

Popeza kuti zonse zimene anayesa kuchita zinakanika, akuluakulu anaganiza kuti makolo anga akundiuzabe zochita. Choncho, mu September 1942, anandikweza sitima n’kunditumiza kusukulu ya Akatolika yotchedwa Adelgunden, mumzinda wa Munich ku Germany. Pasukuluyi pankakhalanso masisitere. Pa nthawi yomwe ndimasamukayi, masisitere anaona Baibulo langa lija ndipo anandilanda.

Ngakhale kuti anachita zimenezi, ndinapitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndipo ndinkakana kuchita nawo mapemphero awo. Nditauza sisitere wina kuti makolo anga ankandiwerengera Baibulo Lamlungu lililonse, zimene anachita zinandidabwitsa kwambiri. Iye anandibwezera Baibulo langa. Ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri ndi zimene ndinamuuza. Ndipotu anandipempha kuti ndimuwerengere Baibulo.

Pa nthawi ina, mphunzitsi wina anandiuza kuti: “Hermine, uli ndi tsitsi loyera komanso maso a buluu. Iwetu ndi Mjeremani, osati Myuda. Yehova ndi Mulungu wa Ayuda.”

Koma ine ndinamuyankha kuti: “Yehova ndi amene analenga chilichonse. Iye ndi Mlengi wa anthu a mitundu yonse.”

Nayenso mphunzitsi wamkulu wa pasukulupo ankandinyengerera kuti ndisinthe maganizo. Tsiku lina anandiuza kuti: “Hermine, kodi ukudziwa kuti mchimwene wako wina wayamba usilikali? Nawenso ungachite bwino kusintha maganizo ngati mchimwene wako.” Ndinkadziwa zoti mchimwene wanga walowa usilikali, koma sindinkafuna kutsatira chitsanzo chake.

Ndinamuyankha kuti, “Sindine wotsatira wa mchimwene wanga. Ndimatsatira Yesu Khristu.” Kenako mphunzitsi wamkuluyo anandiopseza kuti anditumiza kuchipatala cha anthu amisala, moti anauza sisitere wina kuti akonzeke kunditengera kuchipatalako. Koma iye ankangoopseza chabe.

M’chaka cha 1943, mzinda wa Munich unaphulitsidwa ndi mabomba ndipo ana a pasukulu ya Adelgunden anawasamutsira kumudzi winawake. Pa nthawi yonseyi, ndinkakonda kuganizira mawu amene mayi anga anandiuza, akuti: “Ngati titati tasiyana moti sukulandiranso makalata anga, usadzadandaule. Udzakumbukire kuti Yehova ndi Yesu ali nawe ndipo sangakusiye. Pitirizabe kupemphera.”

Anandilola Kubwerera Kunyumba

M’mwezi wa March, 1944, tinabwereranso ku Adelgunden. Pa nthawiyi, mumzinda wa Munich munkaphulika mabomba, choncho sitinkaloledwa kuyendayenda. Makolo anga ankayesetsa kupempha kuti ndibwerere kunyumba, choncho kumapeto kwa mwezi wa April, 1944, ndinabwerera kunyumba.

Ndikutsanzika, mphunzitsi wamkulu anandiuza kuti: “Hermine, usakaiwale kutilembera kalata ukakafika kunyumba. Ndipo usakasinthe khalidwe lako.” Sindinakhulupirire ngakhale pang’ono kuti iwo anganene zimenezi. Koma zinali zomvetsa chisoni kuti nditangochoka, pasukuluyi panaphulika bomba limene linapha atsikana 9 ndi masisitere atatu. Zinandichititsa kuona kuti nkhondo ndi yoipa kwambiri.

Komabe, ndinasangalala kubwerera kunyumba n’kukumananso ndi abale anga. M’mwezi wa May, nkhondo ili mkati, ndinabatizidwa, posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova. Nkhondo itatha mu 1945, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse. Ndinkasangalala kuuza anthu uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, lomwe ndi boma lokhalo limene lidzabweretse mtendere ndiponso chitetezo padzikoli.—Mateyu 6:9, 10.

M’chaka cha 1950, ndinakumana ndi Erich Liska, mnyamata yemwe pa nthawiyo ankayendera mipingo ya Mboni za Yehova ku Vienna, m’dziko la Austria. Tinakwatirana m’chaka cha 1952, ndipo kwa nthawi yochepa ndinkayenda naye polimbikitsa mipingo yosiyanasiyana.

M’chaka cha 1953, ndinabereka mwana wathu woyamba ndipo m’kupita kwa nthawi tinakhalanso ndi ana ena awiri. Kenako tinasiya utumiki wa nthawi zonse chifukwa chakuti tinali ndi udindo waukulu wosamalira ana. Pa nthawi yonseyi, ndaphunzira kuti Mulungu sasiya atumiki ake ngati akumudalira komanso amawapatsa mphamvu zoti apirire. Kuchokera pamene mwamuna wanga anamwalira m’chaka cha 2002, Yehova wakhala akunditonthoza komanso kundilimbikitsa kwambiri.

Ndikaganizira zinthu zimene ndakumana nazo pa moyo wanga, ndimathokoza kwambiri makolo anga chifukwa chondiphunzitsa kuyambira ndili mwana kukonda Mulungu ndi Mawu ake, omwe ndi nkhokwe ya nzeru. (2 Timoteyo 3:16, 17) Koposa zonse, ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa wakhala akundithandiza kupirira mayesero osiyanasiyana.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

“Sindine wotsatira wa mchimwene wanga. Ndimatsatira Yesu Khristu”

[Chithunzi patsamba 19]

Banja lathu ku St. Walburgen

[Zithunzi patsamba 19]

Makolo anga

[Mawu a Chithunzi]

Both photos: Foto Hammerschlag

[Chithunzi patsamba 20]

Ndili ndi mwamuna wanga Erich