Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulera Ana Azaka Zapakati pa 5 ndi 12

Kulera Ana Azaka Zapakati pa 5 ndi 12

Kulera Ana Azaka Zapakati pa 5 ndi 12

“Ana akakhala kuti sanakwanitse zaka zisanu, savuta kuwaphunzitsa makhalidwe abwino chifukwa amakhala asanayambe kupita kusukulu. Koma akangoyamba sukulu, amakakumana ndi anthu amene zochita zawo komanso zolankhula zawo n’zosiyana ndi zimene munawaphunzitsa.”—Anatero Valter, wa ku Italy.

ANA akamakula amayamba kuchita zinthu zina zatsopano zimene sankachita poyamba. Amayamba kucheza ndi anthu osiyanasiyana monga anzawo akusukulu, oyandikana nawo nyumba komanso achibale awo. Mogwirizana ndi zimene ananena Valter, pa nthawiyi mwina amaphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa anthu osiyanasiyana, osati kwa inu nokha. N’chifukwa chake pa nthawi imeneyi n’kofunika kwambiri kuyesetsa kuphunzitsa mwana wanu ubwino wogonjera komanso kukhala ndi makhalidwe abwino. Zimakhalanso bwino kumuphunzitsa kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Kuti mwana akhale ndi makhalidwe amenewa, sizimangochitika zokha. Mumafunika kuyesetsa ‘kumudzudzula, kumutsutsa, ndi kumudandaulira.’ Ndipo pochita zimenezi mumafunika ‘luso la kuphunzitsa ndiponso kuleza mtima kwambiri.’ (2 Timoteyo 4:2) Mulungu anauza makolo achiisiraeli kuti azikhomereza mawu ake m’mitima ya ana awo. Iye anati: ‘Muzilankhula nawo za mawuwo mukakhala pansi m’nyumba zanu, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Monga mmene lembali likusonyezera, kulangiza mwana wanu nthawi zonse n’kofunika kwambiri.

Kulera ana ndi udindo waukulu. Taonani zinthu zina zimene zimafunika.

Nthawi Yokhala Chete

Baibulo limanena kuti pali “nthawi yolankhula,” koma limasonyezanso kuti pali nthawi yokhala chete n’kumamvetsera ena akamalankhula. (Mlaliki 3:7) Kodi mungaphunzitse bwanji mwana wanu kuti azimvetsera pamene inuyo komanso anthu ena akulankhula? Njira imodzi imene angaphunzirire zimenezi ndi kuona zimene inuyo mumachita. Kodi mumamvetsera pamene anthu ena, kuphatikizapo ana anu, akulankhula?

Ana amatha kuyamba kuganizira kapena kuchita zinthu zina pamene mukulankhula nawo, ndipo mwina zimenezi mungamakhumudwe nazo. Koma dziwani kuti mwana aliyense amasiyana ndi mnzake, choncho muyenera kulankhula naye mogwirizana ndi mmene iyeyo alili. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake David, yemwe amakhala ku Britain, anati: “Ndimauza mwana wathu kuti andifotokozerenso zinthu zimene ndangomuuza kumene. Zimenezi zathandiza kuti pamene akukula azimvetsera kwambiri munthu wina akamalankhula naye.”

Popereka malangizo kwa ophunzira ake, Yesu anawauza kuti: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.” (Luka 8:18) Ngati anthu achikulire amafunika kumvetsera mwatcheru, kuli bwanji ana?

“Kukhululukirana ndi Mtima Wonse”

Baibulo limati: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.” (Akolose 3:13) Makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kukhala ndi mtima wokhululuka. Kodi angachite bwanji zimenezi?

Choyamba, inuyo makolo muyenera kukhala ndi mtima wokhululuka. Ana anu akamaona kuti mumakhululukira anthu ena, adzatengera zimenezo. Mayi wina wa ku Russia, dzina lake Marina, amayesetsa kuchita zimenezi. Iye anati: “Timayesetsa kupatsa ana athu chitsanzo chabwino pa nkhani yokhululuka. Ena akatilakwira timawamvetsa. Ndipo ineyo ndikawalakwira ana anga, ndimawapepesa. Ndimafuna kuti nawonso azichita zomwezo ena akawalakwira.”

Kuphunzitsa ana kuti azithetsa mwachangu kusamvana komanso kuti azikhululukira ena n’kofunika kwambiri chifukwa kungadzawathandize akadzakula. Muyenera kuphunzitsa ana anu panopa kuti aziganizira ena komanso kuti azipepesa akalakwitsa. Kuchita zimenezi kuli ngati kuwapatsa mphatso inayake yabwino imene ingadzawathandize kwambiri m’tsogolo.

“Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”

Panopa tikukhala m’nthawi “yovuta” ndipo anthu ambiri ndi “odzikonda.” (2 Timoteyo 3:1, 2) Choncho, pamene ana anu adakali aang’ono muyenera kuwaphunzitsa kukhala ndi mtima woyamikira. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”—Akolose 3:15.

Ana aang’ono angathe kusonyeza makhalidwe abwino ndiponso kuchita zinthu zosonyeza kuti amaganizira ena. Kodi mungawathandize bwanji kuchita zimenezi? Dr. Kyle Pruett anauza olemba magazini ya Parents kuti: “Njira yabwino yophunzitsira ana anu kukhala ndi mtima woyamikira ndi kuonetsetsa kuti inuyo mukusonyeza mtima umenewu. Nthawi zonse muziwauza kuti mumayamikira ntchito zimene amagwira panyumba komanso zinthu zina zimene amachita . . . Koma kuchita zimenezi si kophweka.”

Bambo wina wa ku Britain, dzina lake Richard, amayesetsa kuchita zimenezi. Iye anati: “Ine ndi mkazi wanga, timathokoza anthu amene atichitira zabwino monga aphunzitsi a ana athu kapena agogo a ana athu. Anzathu akatiitanira chakudya kunyumba kwawo, timawalembera khadi loyamikira ndipo ana athu onse amasayina khadilo kapena kujambulapo chithunzi.” Kuphunzitsa ana anu kukhala ndi mtima woyamikira komanso woganizira ena kungawathandize kwambiri kuti azidzagwirizana ndi anthu akadzakula.

“Usam’mane Chilango Mwana”

Ana anu akamakula, amafunikira kudziwa kuti chilichonse chimene akuchita chimakhala ndi zotsatira zake. Ngakhale pamene ali ndi zaka zochepa, ana amafunika kukhala omvera osati panyumba pokha komanso kusukulu ndi kumalo ena. Muyenera kuphunzitsa ana anu kumvetsa mfundo yakuti, munthu amakolola chimene wafesa. (Agalatiya 6:7) Kodi mungawaphunzitse bwanji zimenezi?

Baibulo limanena kuti: “Usam’mane chilango mwana.” (Miyambo 23:13) Ngati munawachenjezapo ana anu kuti akadzachita chinachake mudzawalanga, muyenera kuwalangadi akachita chinthucho. Mayi wina wa ku Argentina, dzina lake Norma, ananena kuti: “Kusasinthasintha malamulo n’kofunika chifukwa mukamasinthasintha mwana wanu amapezerapo mwayi wochita zimene iye akufuna.”

Makolo angapewe kukangana ndi mwana wawo ngati atamamuuziratu chilango chimene angamupatse akachita zinthu zosamvera. Ana akhoza kumakumverani mosavuta ngati atadziwiratu malamulo amene mwakhazikitsa, chilango chimene angalandire akaphwanya malamulowo komanso atadziwa kuti malamulo amene munakhazikitsawo sangasinthe.

Kuti chilango chimene mukupatsa ana anu chikhale chothandiza, muyenera kupewa kuwalanga mutapsa mtima. Baibulo limanena kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu.” (Aefeso 4:31) Muyenera kupewa kulanga ana mpaka kufika powavulaza kapena kuwasokoneza maganizo.

Kodi n’zotheka kuugwira mtima ngati mwana wachita zinthu zokhumudwitsa kwambiri? Bambo wina wa ku New Zealand, dzina lake Peter, ananena kuti: “Pa nthawi imeneyi kuugwira mtima kumakhala kovuta. Koma ngati mukulanga ana mutapsa mtima, anawo sadziwa ngati mukuwalanga chifukwa chakuti alakwa kapena chifukwa chakuti mwakwiya.”

Peter ndi mkazi wake amayesetsa kuthandiza ana awo kumvetsa kuti cholinga cha chilango n’kuwathandiza anawo kuti akule ndi makhalidwe abwino. Iye ananena kuti: “Ngakhale ana athu atalakwitsa bwanji, timayesetsa kuwauza makhalidwe amene ayenera kukhala nawo m’malo mowapangitsa kudziona kuti ndi anthu oipa.”

“Anthu Onse Adziwe Kuti Ndinu Ololera”

Mulungu anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Ndidzakulanga pamlingo woyenera.” (Yeremiya 46:28) Kupatsa ana anu chilango choyenera, chogwirizana ndi zimene alakwitsa, kumathandiza kwambiri anawo. Mtumwi Paulo analembera Akhristu anzake kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.”—Afilipi 4:5.

Njira imodzi yosonyezera kuti ndinu wololera ndiyo kupewa kunyoza ana anu. Bambo wina wa ku Italy, dzina lake Santi, anati: “Ndimayesetsa kuti ndisanyoze ana anga. Pakakhala vuto linalake, ndimafufuza chimene chachititsa vutolo n’kulimbana ndi chinthucho. Ndimapewa kulanga mwana wanga pamaso pa ana anga ena kapena pagulu. Tikakhala pagulu kapena patokha, ndimapewa kuwaseka chifukwa cha zimene alakwitsa.”

Richard, amene tinamutchula uja, amaona kuti kupereka chilango choyenerera n’kofunika kwambiri. Iye anati: “Simuyenera kulanga ana chifukwa cha zinthu zimene anachita kalekale. Mwana akalakwitsa n’kumupatsa chilango, muyenera kupewa kumangomukumbutsa zimene analakwazo kapena kumangozilankhula kwa anthu ena.”

Kulera ana si ntchito yamasewera. Ndi ntchito yofuna kudzipereka kwambiri, koma ubwino wake ndi wakuti imabweretsa madalitso. Tamvani zimene mayi wina wa ku Russia, dzina lake Yelena, ananena. Iye anati: “Ndinasankha kuti masiku ena pa mlungu ndisamapite kuntchito n’cholinga choti ndizikhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi mwana wanga. Kuchita zimenezi kumafuna khama komanso kumachititsa kuti ndizipeza ndalama zochepa, koma ubwino wake ndi wakuti ine ndi mwana wanga timagwirizana kwambiri komanso iye amakhala wosangalala.”

[Chithunzi patsamba 11]

Ana amafunikira kuphunzitsidwa kuti azichita zinthu zoganizira ena

[Chithunzi patsamba 12]

Musamanyoze ana anu powalangiza