Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumafuna Kuti Mwana Wanu Adzakhale Wotani Akadzakula?

Kodi Mumafuna Kuti Mwana Wanu Adzakhale Wotani Akadzakula?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mumafuna Kuti Mwana Wanu Adzakhale Wotani Akadzakula?

KODI mungakonde kuti mwana wanu adzakhale wotani?

A. Azidzangochita ndendende zimene inuyo mumachita.

B. Adzakhale wolowerera.

C. Azidzachita zinthu mwanzeru.

Makolo ena amene angasankhe yankho C, amachita zinthu ngati asankha yankho A. Makolo oterewa amaumiriza mwana wawo kuti azitsatira chilichonse chimene iwo akufuna. Mwachitsanzo, iwo amatha kumusankhira ntchito yoti adzagwire. Kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Iye akangoyamba kuchita zinthu payekha, amayamba kuchita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene makolo ake amayembekezera. Ndipotu nthawi zina makolo amene amachita zinthu ngati asankha yankho A, ana awo amadzachita zinthu zimene zili pa yankho B.

N’chifukwa Chiyani Kumangouza Ana Anu Zochita N’kosathandiza?

Kodi mungatani kuti muthandize mwana wanu kuti akadzakula azidzachita zinthu mwanzeru? Chinthu chimodzi chofunika kwambiri ndi kupewa kumangomuuza zochita. N’chifukwa chiyani muyenera kupewa zimenezi? Taonani zifukwa ziwiri izi:

1. N’zosagwirizana ndi Baibulo. Yehova Mulungu analenga anthu m’njira yakuti azitha kusankha okha zochita. Iye amawapatsa ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. Mwachitsanzo, pamene Kaini anali ndi maganizo ofuna kupha m’bale wake, Abele, Yehova anamuchenjeza kuti: “Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?”—Genesis 4:7.

Onani kuti Yehova anangomuchenjeza Kaini, koma sanamukakamize kuti atsatire malangizo ake. Kaini anali ndi ufulu wosankha kumvera malangizo a Yehova kapena ayi. Kodi makolo angaphunzire chiyani pamenepa? Ngati Yehova sakakamiza anthu kuti azichita zimene iye akufuna, makolonso sayenera kukakamiza ana awo kuchita zimene iwo akufuna. *

2. Ana amasiya kukumverani. Tayerekezani kuti mwakumana ndi munthu wamalonda yemwe akukukakamizani kuti mugule katundu wake. Kodi mungamugule? Ngakhale zitakhala kuti mukumufunadi katunduyo, mwina simungagule chifukwa chakuti akukukakamizani. Mwinanso mungangofuna kuchokapo pamalopo.

Zimenezi n’zimenenso zingachitike ngati mukukakamiza mwana wanu kuti azingotsatira maganizo anu pa chilichonse. Dziwani kuti kuchita zimenezi kungapangitse mwanayo kuyamba kudana ndi chilichonse chimene mukumuuza. Makolo amene amakakamiza ana awo kuchita zimene iwo akufuna, amakhumudwa chifukwa nthawi zambiri anawo amayamba kuchita zinthu zolowerera. Ndiyeno kodi makolo angatani kuti zimenezi zisachitike?

Makolo ayenera kuthandiza mwana wawo kuti azitha kusankha zinthu mwanzeru payekha. Mwachitsanzo, ngati ndinu Mkhristu muyenera kuthandiza mwana wanu kuona kuti kutsatira malamulo a Mulungu kudzamuthandiza kwa moyo wake wonse.—Yesaya 48:17, 18.

Kuti zimenezi zitheke, inuyo makolo muyenera kusonyeza chitsanzo chabwino. Yesetsani kukhala ndi makhalidwe amene mungafune kuti mwana wanu adzakhale nawo. (1 Akorinto 11:1) Ana anu azitha kuona mosavuta mfundo zimene mumatsatira. (Miyambo 4:11) Iwo akamakonda Mulungu ndi malamulo ake, adzatha kusankha zinthu mwanzeru, ngakhale pamene ali okha.—Salimo 119:97; Afilipi 2:12.

Aphunzitseni Zinthu Zothandiza

Monga mmene tafotokozera patsamba 2, nthawi imafika, mwinanso mofulumirirapo kusiyana ndi mmene makolo akuyembekezerera, pamene mwana ‘amasiya bambo ake ndi mayi ake.’ (Genesis 2:24) Inuyo monga kholo, muli ndi udindo womuphunzitsa zinthu zimene zingadzamuthandize akadzachoka. Taonani zinthu zina zimene mungamuphunzitse asanachoke.

Ntchito Zapakhomo. Kodi mwana wanu amatha kuphika, kuchapa ndi kusita zovala, kusamalira chipinda chake, kapena kukonza galimoto? Kudziwa ntchito zimenezi n’kofunika kuti mwana wanuyo asadzavutike akadzachoka pakhomo panu. Mtumwi Paulo ananena kuti: “M’zinthu zonse ndi m’zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi.”—Afilipi 4:12.

Kukhala Bwino ndi Anthu. (Yakobo 3:17) Kodi mwana wanu amatha kukhala bwino ndi anthu ena? Akasemphana maganizo ndi munthu wina, kodi amatha kukambirana naye bwinobwino? Kodi mwamuphunzitsa kulemekeza anthu ena ndi kuthetsa kusamvana mwamtendere? (Aefeso 4:29, 31, 32) Baibulo limati: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.”—1 Petulo 2:17.

Kusamala Ndalama. (Luka 14:28) Kodi mwaphunzitsa mwana wanu ntchito imene ingamamubweretsere ndalama, kupanga bajeti komanso kupewa ngongole? Kodi mwaphunzitsa mwana wanu kusunga ndalama? Kodi mwamuphunzitsa kupewa kugula zinthu mwachisawawa? Kodi mwana wanu amakhutira ndi zimene ali nazo? (Miyambo 22:7) Paulo analemba kuti: “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.

Achinyamata amene aphunzitsidwa kutsatira malamulo a Mulungu komanso amene aphunzitsidwa ntchito ndi kukhala bwino ndi anthu, zimawayendera bwino akachoka n’kukakhala paokha. Nthawi ikakwana yakuti anawo achoke, makolo amasangalala chifukwa amadziwa kuti anawaphunzitsa bwino.—Miyambo 23:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mukafuna kudziwa zambiri zokhudza nkhani imeneyi, onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 2011, tsamba 18 ndi 19.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi makolo mumafuna kuti mwana wanu adzakhale wotani?—Aheberi 5:14.

● Kodi mwana wanu adzakhala ndi ufulu wotani akadzakula?—Yoswa 24:15.

[Chithunzi patsamba 25]

Kodi mumafuna kuti mwana wanu adzakhale wotani akadzakula?

Wongotsatira chilichonse

Wolowerera

Wochita zinthu mwanzeru