Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Pafupifupi ana 17 pa ana 100 alionse azaka 10 mpaka 13 amene ali pasukulu m’dziko la Brazil, amachitiridwa nkhanza kapena iwowo amachitira anzawo nkhanza.—O ESTADO DE SÃO PAULO, BRAZIL.

Masiku ano, ana azaka 12 akupezeka ndi mavuto a matenda othamanga magazi, kuchuluka kwa mafuta m’thupi, ndiponso matenda a chiwindi ndi impso. Kodi n’chiyani chikuchititsa mavuto amenewa? Akuti ana ambiri amangokhala osachita masewera olimbitsa thupi, akudya zakudya zosapatsa thanzi, komanso akumakhala onenepa kwambiri.—ABC, SPAIN.

Kafukufuku amene dziko la America linachita anasonyeza kuti, makolo amene si olemera kwenikweni angafunike ndalama zokwana madola 221,190 (kapena madola 291,570, ngati ndalamayo itachepa mphamvu) kuti alere mwana amene anabadwa m’chaka cha 2008 mpaka mwanayo kufika zaka 18.—UNITED STATES DEPARTMENT OF AGRICULTURE, U.S.A.

Anaiwala Kusewera

Kafukufuku waposachedwa wasonyeza kuti kholo limodzi pa makolo asanu aliwonse ku Britain anaiwala “kusewera ndi ana awo.” Ndipo kholo limodzi pa makolo atatu alionse, limaona kuti kusewera ndi ana n’kotopetsa, ndipo makolo enawo sasewera ndi ana awo chifukwa chakuti amasowa nthawi kapena sadziwa kuti azisewera chiyani ndi ana awo. Ponena za kafukufukuyu, Pulofesa Tanya Byron, ananena kuti: “Pali zinthu zinayi zofunika kwambiri zimene zingathandize makolo kuti azisangalala posewera ndi ana awo. Masewerawo ayenera kukhala ophunzitsa, osangalatsa, oti makolo ndi ana omwe akhoza kusewera, komanso olimbikitsa kuti makolo ndi ana awo azilankhulana.” Ngakhale kuti kholo limodzi pa makolo atatu alionse amafuna kuti azisewera masewera a pakompyuta ndi ana awo, ana ambiri safuna kusewera ndi makolo awo masewera amenewa. Masewera amene ana azaka zoyambira 5 mpaka 15 amafuna kusewera ndi makolo awo, ndi masewera amene amachitikira panja komanso masewera ena monga draft ndi chess.

Kuwerenga Nkhani Pogona

M’malo mowerengera ana awo nkhani pamasom’pamaso pa nthawi yogona, makolo ena akugwiritsa ntchito pulogalamu ya pa Intaneti. Nyuzipepala ina ya Daily Telegraph ya ku Sidney ku America, inati: “Pali pulogalamu yapamwamba imene imajambula mawu a bambo akuwerengera mwana wake nkhani zosiyanasiyana. Pojambula nkhanizo, bamboyo amatha kuwonjezerapo nyimbo, ndi timawu tina tokometsera ndipo kenako amamutumizira mwanayo kudzera pa Intaneti.” Koma akatswiri ena akuona kuti njira imeneyi si yothandiza kwenikweni. Mphunzitsi wina wa payunivesite ya Newcastle m’dziko la Australia, Dr. Richard Fletcher, anati: “Pa nthawi imene kholo likuwerengera mwana wake nkhani, pamachitika zambiri zimene zimathandiza kuti mwana ndi kholo lakelo azikondana.” Fletcher ananenanso kuti pamakhala kulankhulana, kugiligishana, ndiponso kuseka. Palibe pulogalamu ya pa Intaneti imene ingakwanitse kuchita zonse zimene kholo limachita powerengera mwana wake nkhani.