Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Musamapse Mtima Kwambiri?

Kodi Mungatani Kuti Musamapse Mtima Kwambiri?

Kodi Mungatani Kuti Musamapse Mtima Kwambiri?

ZAKA zoposa 2,000 zapitazo, munthu wina yemwe anali wotchuka kwambiri wa ku Greece, dzina lake Aristotle, anagwiritsa ntchito mawu akuti “catharsis” pofotokoza “kutulutsa” nkhawa zimene munthu ali nazo chifukwa choonera sewero loopsa. Mfundo yake inali yakuti, munthu akatulutsa nkhawa zimenezi amamva bwino.

Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, wasayansi wina wa ku Austria, dzina lake Sigmund Freud, anagwirizananso ndi mfundo imeneyi. Iye ankanena kuti ngati anthu sangatulutse zinthu zopweteka zimene akumva mumtima mwawo, akhoza kudwala matenda amene angamawachititse kuti nthawi zina azisangalala, kukhumudwa kapena kukwiya kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, Freud ankalimbikira mfundo yakuti munthu ayenera kutulutsa mkwiyo wake m’malo mongousunga mumtima.

M’zaka za m’ma 1970 ndi 1980, akatswiri ena anafufuza bwino mfundo imeneyi ndipo sanapeze chilichonse chosonyeza kuti ndi yoona. Zimene anapezazi zinachititsa wasayansi wina, dzina lake Carol Tavris, kunena kuti: “Ino si nthawi yokhulupiriranso mfundo yakuti munthu akapsa mtima ayenera kutulutsa mkwiyo wake. Kafukufuku wasonyeza kuti kuonerera zinthu zachiwawa (kapena kuchita zachiwawazo) n’cholinga chothetsa nkhawa n’kosathandiza.”

Wasayansi wina, dzina lake Gary Hankins, anati: “Kafukufuku wasonyeza kuti munthu akatulutsa mkwiyo wake wonse n’cholinga choti amveko bwino, amakhala wokhumudwa kwambiri kuposa poyamba m’malo mokhala wosangalala.” Komabe, n’zovuta kuti akatswiri azachipatala agwirizane chimodzi pa nkhani imeneyi. Koma anthu ambiri apindula ndi malangizo anzeru ochokera m’Baibulo.

“Usapse Mtima”

Wamasalimo Davide anafotokoza momveka bwino njira yopewera kupsa mtima. Iye anati: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya. Usapse mtima kuti ungachite choipa.” (Salimo 37:8) Njira yabwino yopewera kunena kapena kuchita zinazake zimene mungakhumudwe nazo pamapeto pake ndi kungopewa ‘kupsa mtima.’ N’zoona kuti kuchita zimenezi n’kovuta koma n’zotheka. Tiyeni tione njira zokuthandizani kupewa kupsa mtima.

Musamapse Mtima Kwambiri

Kuti musamapse mtima kwambiri muzipewa kuchita zinthu mopupuluma ndipo muziugwira mtima ena akakuputani. Musamangonena chilichonse chomwe chabwera m’maganizo mwanu. Ngati mukuona kuti mwasangalala kwambiri moti mukhoza kulankhula zinthu zimene zingakwiyitse ena kapena zimene pamapeto pake mungadandaule nazo, tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti: “Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Choncho mkangano usanabuke, chokapo.”—Miyambo 17:14.

Mfundo imeneyi inathandiza munthu wina dzina lake Jack, yemwe anali ndi vuto lopsa mtima. Bambo ake anali chidakwa ndipo sankachedwa kupsa mtima, moti nayenso anatengera khalidwe lopsa mtimali. Iye anati: “Ndikakwiya ndinkakhala ngati thupi langa lonse likuyaka moto, ndipo ndinkalankhula mokalipa kwambiri komanso sindinkachedwa kuyambitsa ndewu.”

Koma Jack anasintha atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anazindikira kuti Mulungu angamuthandize kusintha n’kuyamba kulamulira mkwiyo wake. Ndipo anasinthadi. Jack anafotokoza mmene anamvera mnzake wina kuntchito atamutukwana. Iye anati: “Thupi langa linkachita kunjenjemera ndi mkwiyo. Chinthu choyamba chimene ndinaganiza ndi kumugwira pakhosi n’kumugwetsera pansi.”

Koma kodi chinamuthandiza n’chiyani kuti asachite zimenezi? Iye ananena kuti: “Ndimakumbukira kuti ndinapemphera kuti, ‘Chonde Yehova, ndithandizeni kuti mtima wanga ukhale m’malo.’ Kenako, kwa nthawi yoyamba, maganizo anga anakhazikika ndipo ndinangochokapo.” Jack anapitirizabe kuphunzira Baibulo, kupemphera komanso kuganizira mozama malemba monga Miyambo 26:20 limene limati: “Popanda nkhuni moto umazima.” Kuchita zimenezi kwamuthandiza kuti athetse vuto lake lopsa mtima.

Muziyesetsa Kudekha

“Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miyambo 14:30) Kutsatira malangizo a m’Baibulo amenewa kungathandize munthu kupewa kuchita zinthu zimene zingawononge thanzi lake komanso ubwenzi wake ndi Mulungu. Kuyesetsa kuchita zinthu zolimbitsa thupi ngakhale pang’ono chabe, kungakuthandizeni kuti musamakwiye msanga. Zinthu zotsatirazi zathandiza anthu ambiri kupewa kupsa mtima:

● Kupuma mokoka mpweya ndi njira yabwino kwambiri komanso yachangu yochepetsera mkwiyo.

● Pamene mukupuma mokoka mpweya choncho muzinena mobwerezabwereza mawu monga akuti, “mtima m’malo,” “ingozisiya,” kapena “n’zazing’ono.”

● Muzitanganidwa kwambiri ndi zinthu zimene zimakusangalatsani monga kuwerenga, kumvera nyimbo kapena kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti muchepetse mkwiyo wanu.

● Muzichita masewera olimbitsa thupi kawirikawiri komanso muzidya zakudya zopatsa thanzi.

Sinthani Mmene Mumaganizira

Simungathe kupeweratu anthu amene angakupsetseni mtima kapena zinthu zimene zingakukwiyitseni, koma mukhoza kupeza njira zokuthandizani kudziletsa. Zimenezi zikutanthauzanso kuti mufunika kusintha mmene mumaganizira.

Anthu amene amayembekeza zambiri pa moyo wawo amakhalanso ndi vuto lopsa mtima. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ngati zinthu zimene amayembekeza sizinachitike kapena ngati munthu wina sanachite zimene iwo amayembekezera, amakhumudwa ndipo amakwiya. Pofuna kuthetsa vuto limeneli, ndi bwino kukumbukira mfundo yakuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe. . . . Anthu onse apanduka.” (Aroma 3:10, 12) Choncho, tikamayembekezera kuti anthu azichita zinthu mwangwiro, tidzakhumudwa.

Si bwino kuyembekezera kuti inuyo kapena anthu ena azichita zinthu popanda kulakwitsa chilichonse. Baibulo limati: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri. Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2) Kunena zoona, “palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Choncho, ngati timafuna kuti tizichita zinthu ngati munthu wangwiro tikhoza kumangokhumudwa komanso kupsa mtima.

Chifukwa chakuti ndife anthu opanda ungwiro, timakwiya nthawi zina. Koma timachita kusankha zimene tingachite wina akatiputa. Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake kuti: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Kunena zoona, n’zotheka kusonyeza mmene tikumvera popanda kuchita zinthu molusa. Tikamachita zinthu m’njira imeneyi timapewa kudzibweretsera mavuto amene amakhudzanso anthu ena.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]

MUZIYESETSA KUDEKHA

Muzipuma mokoka mpweya

Muzitanganidwa ndi zinthu zimene zimakusangalatsani

Muzichita masewera olimbitsa thupi