Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyama Zochititsa Chidwi za M’nkhalango ya Tasmania

Nyama Zochititsa Chidwi za M’nkhalango ya Tasmania

Nyama Zochititsa Chidwi za M’nkhalango ya Tasmania

MASANA, m’nkhalango ya Tasmania, yomwe ili ku Australia, mumakhala muli zii mopanda phokoso. Koma usiku mumamveka phokoso logonthetsa m’makutu la nyama zinazake zolusa kwambiri zimene zimadya nyama zinzawo. Nyamazi zimatchedwa Tasmanian devil. Nyama zimenezi ndi zamphamvu ndipo zimaoneka zolusa, komanso zimalira moopseza kwambiri makamaka zikamadya. Komabe si zoopsa kwambiri ngati mmene zimaonekera.

Nyamazi zimadya kwambiri moti zikhoza kumaliza kudya nyama zonse zakufa za m’nkhalangoyo m’kanthawi kochepa. Zili ndi mano amphamvu moti zikapeza nyama, zimatha kudya chilichonse ndi mafupa omwe. Ndipo nyama imodzi imatha kudya chakudya chambiri cholemera kuposa thupi lake mu mphindi 30 zokha, moti ali munthu tingati amadya nyama yokwana makilogalamu 25 masana okha.

Kanyama kenanso kochititsa chidwi kamene kamapezeka m’nkhalangoyi ndi kotchedwa Common wombat, komwe ndi kakafupi kooneka ngati mbira. Monga mmene zililinso ndi nyama zina zamtunduwu, nyama zazikazi zimakhala ndi kathumba kosungiramo ana ndipo zimayamwitsa. Koma mosiyana ndi nyama zina zomwe zimakhala ndi kathumba, mwana wa kanyamaka akakhala m’kathumba amayang’ana kumimba osati kutsogolo. Zimenezi zimathandiza kuti mayi ake akamakumba pansi asamamuthire dothi. Tinyamati tilinso ndi mano ataliatali amene amathandiza kwambiri pokumba. Manowa akaperepeseka amaphukiranso. Ngakhale kuti kanyamaka kamaoneka kaulesi chifukwa chonenepa, kamachita zinthu mwadongosolo komanso mwaluso kwambiri, moti kamatha kuthyola masamba ndi miyendo yake yakutsogolo n’kuwaika mkamwa.

Palinso kanyama kena kotchedwa Platypus. Kanyama kameneka kali ndi mlomo komanso mapazi ngati a bakha ndipo thupi lake lili ndi ubweya ngati mbewa. Kamaikira mazira ngati nkhuku, kamakumba una ngati mbewa komanso kamayamwitsa ana ake ngati mbuzi. Wasayansi wina ataona kanyamaka anachita chidwi kwambiri kuona kuti kamafanana ndi nyama zina pa zinthu zambiri.

N’chifukwa chiyani timasangalala tikaona nyama zimenezi? Chifukwa chakuti ndi zimene Mlengi wathu amafuna. Baibulo limanena kuti Iye anauza Adamu ndi Hava kuti: “Muyang’anire . . . cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.” (Genesis 1:28) Tikamaona nyama zimenezi timatsimikiza mtima kupitirizabe kukwaniritsa udindo umene Mulungu anatipatsa wosamalira nyama zakutchire.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

MULINSO MITENGO YAIKULU

M’nkhalango ya ku Tasmania muli mitengo ikuluikulu kwambiri moti anthu ambiri amachita nayo chidwi. Mitengo yaitali kwambiri m’nkhalangoyi yotchedwa mountain ash, yomwe imaoneka ngati bulugamu, imatalika mamita 75. Pali mtengo wina wamtunduwu womwe ndi wautali mamita 99.6. Mtengowu umangoperewera ndi mamita 16 okha kuti ufanane ndi mtengo wina wautali padziko lonse wa redwood, womwe uli ku California, m’dziko la America. Mtengo wa redwood umaoneka ngati mkungudza.

Mtengo wina wochititsa chidwi m’nkhalangoyi ndi wa mkungudza. Mtengo umenewu sutalika kwambiri ngati wa mountain ash koma umakhala zaka zambiri kuwirikiza ka 6 kuposa zaka zimene mtengo wa mountain ash umakhala. Asayansi ena amanena kuti mtengo wa mkungudza umatha kukhala zaka 3,000 ndipo amati padziko lonse palibe mtengo wina umene umakhala nthawi yaitali chonchi. Anthu amaona kuti mtengo umenewu ndi wapadera kwambiri moti amaugwiritsa ntchito akafuna kukonza maboti komanso zinthu zina zamatabwa. Matabwa a mtengowu savuta kupangira zinthu ndipo ali ndi mafuta enaake amene amathandiza kuti matabwawo akhale nthawi yaitali asanawongeke komanso kufumbwa. Mitengo ina ya mkungudza imene anaidula m’nkhalangoyi yatha zaka zambirimbiri osawonongeka ndipo ikhoza kugwiritsidwa ntchito panopa.

[Chithunzi patsamba 10]

Nyama yotchedwa Tasmanian devil

[Mawu a Chithunzi]

© J & C Sohns/age fotostock

[Chithunzi patsamba 11]

Kanyama kotchedwa Common wombat

[Chithunzi patsamba 11]

Kanyama kotchedwa Platypus

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Wombat and platypus: Tourism Tasmania; giant tree: Tourism Tasmania and George Apostolidis