Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Boma la Mulungu Lidzabweretsa Chilungamo Chenicheni

Boma la Mulungu Lidzabweretsa Chilungamo Chenicheni

Boma la Mulungu Lidzabweretsa Chilungamo Chenicheni

ULOSI wa m’Baibulo umasonyeza kuti Mulungu watsala pang’ono kukhazikitsa dziko latsopano. Dziko limenelo lidzakhala ndi boma limodzi, lomwe ndi Ufumu wa Mulungu ndipo mfumu yake ndi Yesu Khristu. (Chivumbulutso 11:15) Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa bwanji zinthu zopanda chilungamo? Udzachita zimenezi m’njira ziwiri.

1. Ufumu wa Mulungu udzathetseratu ulamuliro wa anthu, womwe ndi wopanda chilungamo komanso wolephera. Lemba la Danieli 2:44 limati: “M’masiku a mafumu amenewo [maboma], Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. . . . koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [maboma a anthu], ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”

2. Ufumu wa Mulungu udzawononga anthu onse oipa n’kusiya anthu okonda chilungamo. Lemba la Salimo 37:10 limati: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.” Ndipo vesi 28 limati: “Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika. Adzawateteza mpaka kalekale.”

Anthu “okhulupirika” amenewo adzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a m’pemphero lachitsanzo la Yesu akuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Kodi Mulungu amafuna kuti zinthu zidzakhale bwanji pa dziko lapansili Ufumu wake ukadzayamba kulamulira?

Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira . . .

Ziphuphu ndi kuponderezana zidzatha. Ponena za Yesu Khristu, lemba la Aheberi 1:9 limati: “Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo.” Yesu, yemwe ndi Wolamulira wachilungamo, “adzalanditsa wosauka wofuulira thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. . . . Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa, ndipo adzaona magazi awo kukhala amtengo wapatali.”—Salimo 72:12-14.

Aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira. Baibulo limati: “Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.” (Salimo 67:6) Limanenanso kuti: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.” (Salimo 72:16) Pa nthawi ina Yesu anadyetsa anthu masauzande ambiri ndipo zimenezi zinasonyeza zimene adzachite mu Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 14:15-21; 15:32-38.

Palibe amene adzalepheretse kuti chilungamo chichitike. Baibulo limati: “Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona. Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.” (Aheberi 4:13) Ponena za Khristu, timawerenga kuti: “Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.”—Yesaya 11:3, 4.

Ufumu wa Mulungu Wayandikira

Zinthu padzikoli zafika poipa kwambiri ndipo zimenezi ndi umboni wakuti dzikoli lili kumapeto. Lemba la Salimo 92:7 limati: “Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, amatero kuti awonongeke kwamuyaya.” Kodi mungatani kuti mukhale m’gulu la anthu omwe adzapulumuke, osati owonongedwa? Yesu Khristu anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Kodi mungakonde kuphunzira zinthu zofunika kwambiri zimenezi? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kukambirana ndi a Mboni za Yehova ngati mmene Heide, Dorothy, ndi Firuddin anachitira. A Mboni za Yehova ndikonzeka kuyankha mafunso anu kwaulere ndipo sakakamiza aliyense kulowa chipembedzo chawo.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

KODI MUNGAPIRIRE BWANJI MAVUTO?

Mtsikana wina, dzina lake Emily, yemwe amakhala ku United States anapezeka ndi khansa ya m’magazi ali ndi zaka 7. Ana anzake amangodwala matenda ngati chifuwa ndi chimfine koma iye amangokhalira kumwa mankhwala osiyanasiyana kuphatikizapo kulandira chithandizo chopweteka kwambiri. Emily anati: “Khansa ya m’magazi ndi matenda opweteka kwambiri.”

Ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ambiri, amayesetsa kuti asamangokhala wokhumudwa. Iye akuyembekezera Ufumu wa Mulungu womwe Baibulo limalonjeza kuti: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Emily ananenanso kuti: “Lemba limene limandisangalatsa kwambiri ndi la Maliko 12:30 lomwe limati: ‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’ Ndikapemphera kwa Yehova, amandilimbikitsa. Ndimathokoza Yehova kuti anandipatsa banja labwino, Akhristu anzanga komanso chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lomwe simudzakhala mavuto. Kuyembekezera zinthu zimenezi kumandilimbikitsa kwambiri.”

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira, adzasangalala ndi chilungamo chenicheni komanso dziko lidzakhala lopanda tsankho