Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani 1 Mbiri 16:1, 2, 4-10. Kenako yang’anani chithunzichi. Tchulani zinthu zimene zikusowekapo. Lembani mayankho anu m’munsimu. Malizitsani kujambula chithunzichi polumikiza timadonthoto, ndipo chikongoletseni ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KAMBIRANANI:

Kodi Yehova Mulungu amamva bwanji tikamaimba ngati njira yomulambirira? N’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 5:13, 14; Aefeso 5:19.

Kodi mungatchule nkhani zina za m’Baibulo zomwe anthu anaimba polambira Mulungu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 15:1-20; Maliko 14:26; Machitidwe 16:25.

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziyesetsabe kuimbira Yehova ngakhale kuti ndinu wamanyazi kapena ngati mumaona kuti simutha kuimba?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 33:1-3.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Aliyense wam’banjamo asankhe nyimbo yotamanda Yehova imene amaikonda. Ndiyeno, muphunzirire pamodzi nyimbozo mpaka mutazidziwa bwino.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 17 YONA

MAFUNSO

A. Mulungu anatuma Yona kuti akalalikire ku ․․․․․, kumene kunkakhala anthu oposa ․․․․․.

B. Ngakhale kuti poyamba Yona sanapite kumene Yehova anamutuma, kodi iye anachita chiyani, chimene chinathandiza kuti anthu apulumuke?

C. Malizitsani mawu a m’Baibulo awa: “Yona anakhala m’mimba . . . ”

[Tchati]

4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

Anakhala ndi moyo m’zaka za m’ma 840 B.C.E.

1 C.E.

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

Anathawa kuchoka ku Gati-heferi kupita ku Tariso

Gati-heferi

TARISO

Nineve

YONA

ANALI NDANI?

Anali mneneri wa Yehova yemwe anatumikira pa nthawi ya mfumu Yerobowamu Wachiwiri. (2 Mafumu 14:23-25) Yehova anaphunzitsa Yona kuti asamangoganiza za iye yekha, koma aziganiziranso za anthu ena. (Yona 4:6-11) Zimene zinamuchitikira Yona zimatiphunzitsa mfundo yoti Yehova ndi woleza mtima kwambiri, wachifundo komanso amakomera mtima anthu ochimwa.

MAYANKHO

A. Nineve, 120,000.—Yona 1:1, 2; 4:11.

B. Anauza anthu a m’sitimayo kuti amuponyere m’madzi kuti panyanja pakhale bata.—Yona 1:3, 9-16.

C.“ . . . mwa nsomba masiku atatu, usana ndi usiku.”—Yona 1:17.

Anthu ndi Mayiko

4. Mayina athu ndi Melissa ndi Edilo ndipo tili ndi zaka 9 ndi 7. Timakhala ku Cuba. Kodi mukudziwa kuti ku Cuba kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 51,000; 91,000, kapena 131,000?

5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Cuba.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti, “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 14

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Chihema chosungiramo Likasa.

2. Zeze.

3. Lipenga.

4. 91,000.

5. C.