Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikumbukira Kunena Kuti Zikomo Kwambiri

Muzikumbukira Kunena Kuti Zikomo Kwambiri

Muzikumbukira Kunena Kuti Zikomo Kwambiri

KODI munthu anayambapo wakuthokozani chifukwa cha zinazake zimene mwamuchitira? Nanga inuyo munayamba mwathokozapo chifukwa cha zimene winawake anakuchitirani?

Chifukwa chakuti masiku ano anthu akumagwiritsa ntchito makompyuta kapena Intaneti, anasiya kulemberana makalata othokoza wina akawachitira chinachake. Koma kulemba kalata yothokoza ndi njira yabwino yosonyezera kuti mukuyamikira zimene ena akuchitirani. Taonani zina mwa zinthu zimene mungatsatire polemba kalata yothokoza:

1. Mungachite bwino kulemba kalatayo pamanja chifukwa munthu amasangalala kwambiri mukachita zimenezi kusiyana n’kulemba pa kompyuta.

2. Gwiritsani ntchito dzina lolemekeza potchula munthu amene wakupatsani mphatsoyo.

3. Mukalandira mphatso, muziitchula mphatsoyo m’kalatamo ndipo muzifotokoza mmene mukufuna kuigwiritsira ntchito.

4. Muzibwerezanso mawu othokoza kumapeto kwa kalatayo.

Munthu amene wakupatsani mphatso amasangalala kwambiri mukamulembera kalata yomuthokoza.

Choncho, winawake akadzakupatsani mphatso kapena kukuchitirani zinazake zabwino, mudzakumbukire kunena kuti zikomo kwambiri.

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 28, 29]

Okondedwa Azakhali, (2)

Ndalemba kalatayi pofuna kukuthokozani chifukwa cha wotchi imene munandipatsa ija. (3) Ineyo ndimagona kwambiri moti ndimavutika kudzuka nthawi yabwino. Choncho wotchi imeneyi izindithandiza kwambiri chifukwa ili ndi alamu imene izindidzutsa. Tinasangalala kwambiri kuti munabwera kudzationa mlungu wathawu ndipo ndikukhulupirira kuti munayenda bwino. Tidzasangalala kuonananso.

Pomaliza ndikuthokozanso chifukwa cha mphatso imeneyi. (4)

Ndine mwana wanu,

John

[Chithunzi]

(1)

[Bokosi patsamba 29]

MFUNDO ZOTHANDIZA

● Ngati mwapatsidwa ndalama, musamatchule nambala yeniyeni ya ndalamazo m’kalatayo. Mwachitsanzo, munganene kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha ndalama zimene munandipatsa zija. Ndalama zimenezi zindithandiza . . . ”

● M’kalatayo muzingolemba zokhudza mphatsoyo basi komanso mawu anu othokoza. Sibwino kulembamo nkhani zina monga za mmene munayendera ulendo winawake.

● Ngati mwadziwa kuti mphatsoyo ili ndi vuto linalake, musamalembe za vutolo m’kalatayo. Mwachitsanzo, sibwino kulemba kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha thalauza lija, ngakhale kuti likukhwepa.”

[Bokosi patsamba 29]

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizithokoza. (Luka 17:11-19) Komanso limati tizipemphera “mosalekeza” kwa Mulungu. Limatilimbikitsanso kuti: “Muziyamika pa chilichonse.”—1 Atesalonika 5:17, 18.